Matthew 10 (BOGWICC)

1 Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse. 2 Mayina a atumwi khumi ndi awiriwo ndi awa: woyamba, Simoni (wotchedwa Petro) ndi mʼbale wake Andreya; Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mʼbale wake Yohane, 3 Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo; 4 Simoni Mzerote ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye. 5 Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya. 6 Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. 7 Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ 8 Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere. 9 “Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; 10 musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. 11 Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. 12 Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. 13 Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. 15 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo. 16 “Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda. 17 Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. 18 Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina. 19 Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, 20 pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu. 21 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 22 Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. 23 Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere. 24 “Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo wantchito saposa bwana wake. 25 Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake! 26 “Chifukwa chake musaope iwo. Pakuti palibe chinthu chobisika chimene sichidzavundukulidwa, ndi chobisika chimene sichidzadziwika. 27 Chimene ndikuwuzani Ine mu mdima, muchiyankhule poyera; chimene akunongʼonezani mʼkhutu, muchilalikire muli pa denga. 28 Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena. 29 Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. 30 Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. 31 Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri. 32 “Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. 33 Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba. 34 “Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. 35 Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa “ ‘Munthu ndi abambo ake, mwana wamkazi ndi amayi ake, mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake, 36 adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’ 37 “Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. 38 Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. 39 Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza. 40 “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine. 41 Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama. 42 Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”

In Other Versions

Matthew 10 in the ANGEFD

Matthew 10 in the ANTPNG2D

Matthew 10 in the AS21

Matthew 10 in the BAGH

Matthew 10 in the BBPNG

Matthew 10 in the BBT1E

Matthew 10 in the BDS

Matthew 10 in the BEV

Matthew 10 in the BHAD

Matthew 10 in the BIB

Matthew 10 in the BLPT

Matthew 10 in the BNT

Matthew 10 in the BNTABOOT

Matthew 10 in the BNTLV

Matthew 10 in the BOATCB

Matthew 10 in the BOATCB2

Matthew 10 in the BOBCV

Matthew 10 in the BOCNT

Matthew 10 in the BOECS

Matthew 10 in the BOHCB

Matthew 10 in the BOHCV

Matthew 10 in the BOHLNT

Matthew 10 in the BOHNTLTAL

Matthew 10 in the BOICB

Matthew 10 in the BOILNTAP

Matthew 10 in the BOITCV

Matthew 10 in the BOKCV

Matthew 10 in the BOKCV2

Matthew 10 in the BOKHWOG

Matthew 10 in the BOKSSV

Matthew 10 in the BOLCB

Matthew 10 in the BOLCB2

Matthew 10 in the BOMCV

Matthew 10 in the BONAV

Matthew 10 in the BONCB

Matthew 10 in the BONLT

Matthew 10 in the BONUT2

Matthew 10 in the BOPLNT

Matthew 10 in the BOSCB

Matthew 10 in the BOSNC

Matthew 10 in the BOTLNT

Matthew 10 in the BOVCB

Matthew 10 in the BOYCB

Matthew 10 in the BPBB

Matthew 10 in the BPH

Matthew 10 in the BSB

Matthew 10 in the CCB

Matthew 10 in the CUV

Matthew 10 in the CUVS

Matthew 10 in the DBT

Matthew 10 in the DGDNT

Matthew 10 in the DHNT

Matthew 10 in the DNT

Matthew 10 in the ELBE

Matthew 10 in the EMTV

Matthew 10 in the ESV

Matthew 10 in the FBV

Matthew 10 in the FEB

Matthew 10 in the GGMNT

Matthew 10 in the GNT

Matthew 10 in the HARY

Matthew 10 in the HNT

Matthew 10 in the IRVA

Matthew 10 in the IRVB

Matthew 10 in the IRVG

Matthew 10 in the IRVH

Matthew 10 in the IRVK

Matthew 10 in the IRVM

Matthew 10 in the IRVM2

Matthew 10 in the IRVO

Matthew 10 in the IRVP

Matthew 10 in the IRVT

Matthew 10 in the IRVT2

Matthew 10 in the IRVU

Matthew 10 in the ISVN

Matthew 10 in the JSNT

Matthew 10 in the KAPI

Matthew 10 in the KBT1ETNIK

Matthew 10 in the KBV

Matthew 10 in the KJV

Matthew 10 in the KNFD

Matthew 10 in the LBA

Matthew 10 in the LBLA

Matthew 10 in the LNT

Matthew 10 in the LSV

Matthew 10 in the MAAL

Matthew 10 in the MBV

Matthew 10 in the MBV2

Matthew 10 in the MHNT

Matthew 10 in the MKNFD

Matthew 10 in the MNG

Matthew 10 in the MNT

Matthew 10 in the MNT2

Matthew 10 in the MRS1T

Matthew 10 in the NAA

Matthew 10 in the NASB

Matthew 10 in the NBLA

Matthew 10 in the NBS

Matthew 10 in the NBVTP

Matthew 10 in the NET2

Matthew 10 in the NIV11

Matthew 10 in the NNT

Matthew 10 in the NNT2

Matthew 10 in the NNT3

Matthew 10 in the PDDPT

Matthew 10 in the PFNT

Matthew 10 in the RMNT

Matthew 10 in the SBIAS

Matthew 10 in the SBIBS

Matthew 10 in the SBIBS2

Matthew 10 in the SBICS

Matthew 10 in the SBIDS

Matthew 10 in the SBIGS

Matthew 10 in the SBIHS

Matthew 10 in the SBIIS

Matthew 10 in the SBIIS2

Matthew 10 in the SBIIS3

Matthew 10 in the SBIKS

Matthew 10 in the SBIKS2

Matthew 10 in the SBIMS

Matthew 10 in the SBIOS

Matthew 10 in the SBIPS

Matthew 10 in the SBISS

Matthew 10 in the SBITS

Matthew 10 in the SBITS2

Matthew 10 in the SBITS3

Matthew 10 in the SBITS4

Matthew 10 in the SBIUS

Matthew 10 in the SBIVS

Matthew 10 in the SBT

Matthew 10 in the SBT1E

Matthew 10 in the SCHL

Matthew 10 in the SNT

Matthew 10 in the SUSU

Matthew 10 in the SUSU2

Matthew 10 in the SYNO

Matthew 10 in the TBIAOTANT

Matthew 10 in the TBT1E

Matthew 10 in the TBT1E2

Matthew 10 in the TFTIP

Matthew 10 in the TFTU

Matthew 10 in the TGNTATF3T

Matthew 10 in the THAI

Matthew 10 in the TNFD

Matthew 10 in the TNT

Matthew 10 in the TNTIK

Matthew 10 in the TNTIL

Matthew 10 in the TNTIN

Matthew 10 in the TNTIP

Matthew 10 in the TNTIZ

Matthew 10 in the TOMA

Matthew 10 in the TTENT

Matthew 10 in the UBG

Matthew 10 in the UGV

Matthew 10 in the UGV2

Matthew 10 in the UGV3

Matthew 10 in the VBL

Matthew 10 in the VDCC

Matthew 10 in the YALU

Matthew 10 in the YAPE

Matthew 10 in the YBVTP

Matthew 10 in the ZBP