Matthew 14 (BOGWICC)

1 Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu. 2 Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.” 3 Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo. 4 Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.” 5 Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri. 6 Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri. 7 Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe. 8 Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” 9 Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe; 10 ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende. 11 Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake. 12 Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu. 13 Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda. 14 Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo. 15 Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.” 16 Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.” 17 Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.” 18 Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.” 19 Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. 20 Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. 21 Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000. 22 Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo. 23 Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha. 24 Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo. 25 Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja. 26 Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha. 27 Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.” 28 Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.” 29 Iye anati, “Bwera.”Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu. 30 Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!” 31 Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?” 32 Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka. 33 Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” 34 Atawoloka, anafika ku Genesareti. 35 Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye. 36 Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.

In Other Versions

Matthew 14 in the ANGEFD

Matthew 14 in the ANTPNG2D

Matthew 14 in the AS21

Matthew 14 in the BAGH

Matthew 14 in the BBPNG

Matthew 14 in the BBT1E

Matthew 14 in the BDS

Matthew 14 in the BEV

Matthew 14 in the BHAD

Matthew 14 in the BIB

Matthew 14 in the BLPT

Matthew 14 in the BNT

Matthew 14 in the BNTABOOT

Matthew 14 in the BNTLV

Matthew 14 in the BOATCB

Matthew 14 in the BOATCB2

Matthew 14 in the BOBCV

Matthew 14 in the BOCNT

Matthew 14 in the BOECS

Matthew 14 in the BOHCB

Matthew 14 in the BOHCV

Matthew 14 in the BOHLNT

Matthew 14 in the BOHNTLTAL

Matthew 14 in the BOICB

Matthew 14 in the BOILNTAP

Matthew 14 in the BOITCV

Matthew 14 in the BOKCV

Matthew 14 in the BOKCV2

Matthew 14 in the BOKHWOG

Matthew 14 in the BOKSSV

Matthew 14 in the BOLCB

Matthew 14 in the BOLCB2

Matthew 14 in the BOMCV

Matthew 14 in the BONAV

Matthew 14 in the BONCB

Matthew 14 in the BONLT

Matthew 14 in the BONUT2

Matthew 14 in the BOPLNT

Matthew 14 in the BOSCB

Matthew 14 in the BOSNC

Matthew 14 in the BOTLNT

Matthew 14 in the BOVCB

Matthew 14 in the BOYCB

Matthew 14 in the BPBB

Matthew 14 in the BPH

Matthew 14 in the BSB

Matthew 14 in the CCB

Matthew 14 in the CUV

Matthew 14 in the CUVS

Matthew 14 in the DBT

Matthew 14 in the DGDNT

Matthew 14 in the DHNT

Matthew 14 in the DNT

Matthew 14 in the ELBE

Matthew 14 in the EMTV

Matthew 14 in the ESV

Matthew 14 in the FBV

Matthew 14 in the FEB

Matthew 14 in the GGMNT

Matthew 14 in the GNT

Matthew 14 in the HARY

Matthew 14 in the HNT

Matthew 14 in the IRVA

Matthew 14 in the IRVB

Matthew 14 in the IRVG

Matthew 14 in the IRVH

Matthew 14 in the IRVK

Matthew 14 in the IRVM

Matthew 14 in the IRVM2

Matthew 14 in the IRVO

Matthew 14 in the IRVP

Matthew 14 in the IRVT

Matthew 14 in the IRVT2

Matthew 14 in the IRVU

Matthew 14 in the ISVN

Matthew 14 in the JSNT

Matthew 14 in the KAPI

Matthew 14 in the KBT1ETNIK

Matthew 14 in the KBV

Matthew 14 in the KJV

Matthew 14 in the KNFD

Matthew 14 in the LBA

Matthew 14 in the LBLA

Matthew 14 in the LNT

Matthew 14 in the LSV

Matthew 14 in the MAAL

Matthew 14 in the MBV

Matthew 14 in the MBV2

Matthew 14 in the MHNT

Matthew 14 in the MKNFD

Matthew 14 in the MNG

Matthew 14 in the MNT

Matthew 14 in the MNT2

Matthew 14 in the MRS1T

Matthew 14 in the NAA

Matthew 14 in the NASB

Matthew 14 in the NBLA

Matthew 14 in the NBS

Matthew 14 in the NBVTP

Matthew 14 in the NET2

Matthew 14 in the NIV11

Matthew 14 in the NNT

Matthew 14 in the NNT2

Matthew 14 in the NNT3

Matthew 14 in the PDDPT

Matthew 14 in the PFNT

Matthew 14 in the RMNT

Matthew 14 in the SBIAS

Matthew 14 in the SBIBS

Matthew 14 in the SBIBS2

Matthew 14 in the SBICS

Matthew 14 in the SBIDS

Matthew 14 in the SBIGS

Matthew 14 in the SBIHS

Matthew 14 in the SBIIS

Matthew 14 in the SBIIS2

Matthew 14 in the SBIIS3

Matthew 14 in the SBIKS

Matthew 14 in the SBIKS2

Matthew 14 in the SBIMS

Matthew 14 in the SBIOS

Matthew 14 in the SBIPS

Matthew 14 in the SBISS

Matthew 14 in the SBITS

Matthew 14 in the SBITS2

Matthew 14 in the SBITS3

Matthew 14 in the SBITS4

Matthew 14 in the SBIUS

Matthew 14 in the SBIVS

Matthew 14 in the SBT

Matthew 14 in the SBT1E

Matthew 14 in the SCHL

Matthew 14 in the SNT

Matthew 14 in the SUSU

Matthew 14 in the SUSU2

Matthew 14 in the SYNO

Matthew 14 in the TBIAOTANT

Matthew 14 in the TBT1E

Matthew 14 in the TBT1E2

Matthew 14 in the TFTIP

Matthew 14 in the TFTU

Matthew 14 in the TGNTATF3T

Matthew 14 in the THAI

Matthew 14 in the TNFD

Matthew 14 in the TNT

Matthew 14 in the TNTIK

Matthew 14 in the TNTIL

Matthew 14 in the TNTIN

Matthew 14 in the TNTIP

Matthew 14 in the TNTIZ

Matthew 14 in the TOMA

Matthew 14 in the TTENT

Matthew 14 in the UBG

Matthew 14 in the UGV

Matthew 14 in the UGV2

Matthew 14 in the UGV3

Matthew 14 in the VBL

Matthew 14 in the VDCC

Matthew 14 in the YALU

Matthew 14 in the YAPE

Matthew 14 in the YBVTP

Matthew 14 in the ZBP