Matthew 20 (BOGWICC)

1 “Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. 2 Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa. 3 “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. 4 Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ 5 Ndipo anapita. “Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. 6 Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ 7 “Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’ “Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’ 8 “Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’ 9 “Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. 10 Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. 11 Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. 12 Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’ 13 “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? 14 Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. 15 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’ 16 “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.” 17 Tsopano pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, anatengera pambali ophunzira ake khumi ndi awiriwo nati kwa iwo, 18 “Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, 19 ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!” 20 Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye. 21 Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?”Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.” 22 Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?”Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.” 23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.” 24 Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo. 25 Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira. 26 Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. 27 Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. 28 Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.” 29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” 31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” 32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?” 33 Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!” 34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.

In Other Versions

Matthew 20 in the ANGEFD

Matthew 20 in the ANTPNG2D

Matthew 20 in the AS21

Matthew 20 in the BAGH

Matthew 20 in the BBPNG

Matthew 20 in the BBT1E

Matthew 20 in the BDS

Matthew 20 in the BEV

Matthew 20 in the BHAD

Matthew 20 in the BIB

Matthew 20 in the BLPT

Matthew 20 in the BNT

Matthew 20 in the BNTABOOT

Matthew 20 in the BNTLV

Matthew 20 in the BOATCB

Matthew 20 in the BOATCB2

Matthew 20 in the BOBCV

Matthew 20 in the BOCNT

Matthew 20 in the BOECS

Matthew 20 in the BOHCB

Matthew 20 in the BOHCV

Matthew 20 in the BOHLNT

Matthew 20 in the BOHNTLTAL

Matthew 20 in the BOICB

Matthew 20 in the BOILNTAP

Matthew 20 in the BOITCV

Matthew 20 in the BOKCV

Matthew 20 in the BOKCV2

Matthew 20 in the BOKHWOG

Matthew 20 in the BOKSSV

Matthew 20 in the BOLCB

Matthew 20 in the BOLCB2

Matthew 20 in the BOMCV

Matthew 20 in the BONAV

Matthew 20 in the BONCB

Matthew 20 in the BONLT

Matthew 20 in the BONUT2

Matthew 20 in the BOPLNT

Matthew 20 in the BOSCB

Matthew 20 in the BOSNC

Matthew 20 in the BOTLNT

Matthew 20 in the BOVCB

Matthew 20 in the BOYCB

Matthew 20 in the BPBB

Matthew 20 in the BPH

Matthew 20 in the BSB

Matthew 20 in the CCB

Matthew 20 in the CUV

Matthew 20 in the CUVS

Matthew 20 in the DBT

Matthew 20 in the DGDNT

Matthew 20 in the DHNT

Matthew 20 in the DNT

Matthew 20 in the ELBE

Matthew 20 in the EMTV

Matthew 20 in the ESV

Matthew 20 in the FBV

Matthew 20 in the FEB

Matthew 20 in the GGMNT

Matthew 20 in the GNT

Matthew 20 in the HARY

Matthew 20 in the HNT

Matthew 20 in the IRVA

Matthew 20 in the IRVB

Matthew 20 in the IRVG

Matthew 20 in the IRVH

Matthew 20 in the IRVK

Matthew 20 in the IRVM

Matthew 20 in the IRVM2

Matthew 20 in the IRVO

Matthew 20 in the IRVP

Matthew 20 in the IRVT

Matthew 20 in the IRVT2

Matthew 20 in the IRVU

Matthew 20 in the ISVN

Matthew 20 in the JSNT

Matthew 20 in the KAPI

Matthew 20 in the KBT1ETNIK

Matthew 20 in the KBV

Matthew 20 in the KJV

Matthew 20 in the KNFD

Matthew 20 in the LBA

Matthew 20 in the LBLA

Matthew 20 in the LNT

Matthew 20 in the LSV

Matthew 20 in the MAAL

Matthew 20 in the MBV

Matthew 20 in the MBV2

Matthew 20 in the MHNT

Matthew 20 in the MKNFD

Matthew 20 in the MNG

Matthew 20 in the MNT

Matthew 20 in the MNT2

Matthew 20 in the MRS1T

Matthew 20 in the NAA

Matthew 20 in the NASB

Matthew 20 in the NBLA

Matthew 20 in the NBS

Matthew 20 in the NBVTP

Matthew 20 in the NET2

Matthew 20 in the NIV11

Matthew 20 in the NNT

Matthew 20 in the NNT2

Matthew 20 in the NNT3

Matthew 20 in the PDDPT

Matthew 20 in the PFNT

Matthew 20 in the RMNT

Matthew 20 in the SBIAS

Matthew 20 in the SBIBS

Matthew 20 in the SBIBS2

Matthew 20 in the SBICS

Matthew 20 in the SBIDS

Matthew 20 in the SBIGS

Matthew 20 in the SBIHS

Matthew 20 in the SBIIS

Matthew 20 in the SBIIS2

Matthew 20 in the SBIIS3

Matthew 20 in the SBIKS

Matthew 20 in the SBIKS2

Matthew 20 in the SBIMS

Matthew 20 in the SBIOS

Matthew 20 in the SBIPS

Matthew 20 in the SBISS

Matthew 20 in the SBITS

Matthew 20 in the SBITS2

Matthew 20 in the SBITS3

Matthew 20 in the SBITS4

Matthew 20 in the SBIUS

Matthew 20 in the SBIVS

Matthew 20 in the SBT

Matthew 20 in the SBT1E

Matthew 20 in the SCHL

Matthew 20 in the SNT

Matthew 20 in the SUSU

Matthew 20 in the SUSU2

Matthew 20 in the SYNO

Matthew 20 in the TBIAOTANT

Matthew 20 in the TBT1E

Matthew 20 in the TBT1E2

Matthew 20 in the TFTIP

Matthew 20 in the TFTU

Matthew 20 in the TGNTATF3T

Matthew 20 in the THAI

Matthew 20 in the TNFD

Matthew 20 in the TNT

Matthew 20 in the TNTIK

Matthew 20 in the TNTIL

Matthew 20 in the TNTIN

Matthew 20 in the TNTIP

Matthew 20 in the TNTIZ

Matthew 20 in the TOMA

Matthew 20 in the TTENT

Matthew 20 in the UBG

Matthew 20 in the UGV

Matthew 20 in the UGV2

Matthew 20 in the UGV3

Matthew 20 in the VBL

Matthew 20 in the VDCC

Matthew 20 in the YALU

Matthew 20 in the YAPE

Matthew 20 in the YBVTP

Matthew 20 in the ZBP