Matthew 26 (BOGWICC)

1 Yesu atamaliza kuyankhula zonsezi, anati kwa ophunzira ake, 2 “Monga mukudziwa, kwatsala masiku awiri kuti Paska ifike ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti apachikidwe.” 3 Pamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa, 4 ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha. 5 Ndipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.” 6 Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate, 7 mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo. 8 Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? 9 Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.” 10 Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 11 Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 12 Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 13 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.” 14 Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe 15 nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu. 16 Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu. 17 Pa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?” 18 Iye anayankha kuti, “Pitani mu mzinda kwa munthu wakutiwakuti ndipo kamuwuzeni kuti, ‘Aphunzitsi akuti, nthawi yanga yoyikidwa yayandikira. Ine ndidzadya phwando la Paska ndi ophunzira anga ku nyumba kwako.’ ” 19 Pamenepo ophunzira ake anachita monga momwe Yesu anawawuzira ndipo anakonza Paska. 20 Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiriwo anakhala pa tebulo nʼkumadya. 21 Akudya, Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka.” 22 Iwo anamva chisoni kwambiri ndipo anayamba kuyankhulana naye mmodzimmodzi nati, “Kodi nʼkukhala ine Ambuye?” 23 Yesu anayankha nati, “Iye amene akusunsa mʼmbale pamodzi ndi Ine, yemweyo adzandipereka. 24 Mwana wa Munthu adzaphedwa monga mmene kunalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene apereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.” 25 Ndipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?”Yesu anayankha nati, “Iwe watero.” 26 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, idyani; ili ndi thupi langa.” 27 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati, “Imwani nonsenu. 28 Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri kuti akhululukidwe machimo. 29 Ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mtengo wa mpesa kuyambira lero mpaka tsiku ilo pamene ndidzamwenso mwatsopano ndi inu mu ufumu wa Atate anga.” 30 Atayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi. 31 Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Usiku omwe uno inu nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “ ‘Kantha mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’ 32 Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.” 33 Petro anayankha nati, “Ngakhale onsewa atakuthawani, ine ndekha ayi.” 34 Yesu anayankha nati, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti usiku omwe uno, asanalire tambala, udzandikana Ine katatu.” 35 Koma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi. 36 Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti, “Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo.” 37 Anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima. 38 Pamenepo anawawuza kuti, “Moyo wanga uli ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo dikirani pamodzi ndi Ine.” 39 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, “Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.” 40 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti, “Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha? 41 Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.” 42 Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, “Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.” 43 Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo. 44 Choncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi. 45 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo, “Kodi mukanagonabe ndi kupumula? Taonani, ora layandikira ndipo Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa ochimwa. 46 Imirirani, tiyeni tizipita! Wondipereka Ine wafika!” 47 Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu. 48 Womuperekayo anawawuziratu chizindikiro anthuwo kuti, “Amene ndidzapsompsona ndi iyeyo; mugwireni.” 49 Pamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye. 50 Yesu anayankha kuti, “Bwenzi langa, chita chimene wabwerera.”Pamenepo anthuwo anabwera patsogolo namugwira Yesu ndi kumumanga. 51 Pa chifukwa ichi, mmodzi wa anzake a Yesu anagwira lupanga lake, nalisolola ndi kutema wantchito wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake. 52 Yesu anati kwa iye, “Bwezera lupanga lako mʼchimake, chifukwa onse amene amapha ndi lupanga adzafa ndi lupanga. 53 Kodi mukuganiza kuti sindingathe kupempha Atate anga ndipo nthawi yomweyo nʼkundipatsa magulu a angelo oposa khumi ndi awiri? 54 Koma nanga malemba akwaniritsidwa bwanji amene akuti ziyenera kuchitika motere?” 55 Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo, “Kodi ndine mtsogoleri wa anthu owukira kuti mwabwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mʼNyumba ya Mulungu kuphunzitsa, koma simunandigwire. 56 Koma zonsezi zachitika kuti zolembedwa ndi aneneri zikwaniritsidwe.” Pamenepo ophunzira anamusiya nathawa. 57 Iwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana. 58 Koma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira. 59 Akulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu. 60 Koma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka.Pomalizira mboni ziwiri zinabwera patsogolo. 61 Ndipo zinati, “Munthu uyu anati, ‘Ndikhoza kupasula Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso mʼmasiku atatu.’ ” 62 Pamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?” 63 Koma Yesu anakhalabe chete.Mkulu wa ansembe anati kwa Iye, “Ndikulamulira Iwe ndi lumbiro pamaso pa Mulungu wa Moyo: utiwuze ife ngati ndiwe Khristu Mwana wa Mulungu.” 64 Yesu anayankha nati, “Mwanena ndinu. Koma ndikunena kwa inu nonse: mʼtsogolomo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera ndi mitambo ya kumwamba.” 65 Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake. 66 Mukuganiza bwanji?”Iwo anayankha kuti, “Ayenera kuphedwa!” 67 Kenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi. 68 Ndipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?” 69 Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.” 70 Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.” 71 Kenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.” 72 Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!” 73 Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.” 74 Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!”Nthawi yomweyo tambala analira. 75 Ndipo Petro anakumbukira mawu amene Yesu anayankhula kuti, “Tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.” Ndipo anatuluka panja nakalira kwambiri.

In Other Versions

Matthew 26 in the ANGEFD

Matthew 26 in the ANTPNG2D

Matthew 26 in the AS21

Matthew 26 in the BAGH

Matthew 26 in the BBPNG

Matthew 26 in the BBT1E

Matthew 26 in the BDS

Matthew 26 in the BEV

Matthew 26 in the BHAD

Matthew 26 in the BIB

Matthew 26 in the BLPT

Matthew 26 in the BNT

Matthew 26 in the BNTABOOT

Matthew 26 in the BNTLV

Matthew 26 in the BOATCB

Matthew 26 in the BOATCB2

Matthew 26 in the BOBCV

Matthew 26 in the BOCNT

Matthew 26 in the BOECS

Matthew 26 in the BOHCB

Matthew 26 in the BOHCV

Matthew 26 in the BOHLNT

Matthew 26 in the BOHNTLTAL

Matthew 26 in the BOICB

Matthew 26 in the BOILNTAP

Matthew 26 in the BOITCV

Matthew 26 in the BOKCV

Matthew 26 in the BOKCV2

Matthew 26 in the BOKHWOG

Matthew 26 in the BOKSSV

Matthew 26 in the BOLCB

Matthew 26 in the BOLCB2

Matthew 26 in the BOMCV

Matthew 26 in the BONAV

Matthew 26 in the BONCB

Matthew 26 in the BONLT

Matthew 26 in the BONUT2

Matthew 26 in the BOPLNT

Matthew 26 in the BOSCB

Matthew 26 in the BOSNC

Matthew 26 in the BOTLNT

Matthew 26 in the BOVCB

Matthew 26 in the BOYCB

Matthew 26 in the BPBB

Matthew 26 in the BPH

Matthew 26 in the BSB

Matthew 26 in the CCB

Matthew 26 in the CUV

Matthew 26 in the CUVS

Matthew 26 in the DBT

Matthew 26 in the DGDNT

Matthew 26 in the DHNT

Matthew 26 in the DNT

Matthew 26 in the ELBE

Matthew 26 in the EMTV

Matthew 26 in the ESV

Matthew 26 in the FBV

Matthew 26 in the FEB

Matthew 26 in the GGMNT

Matthew 26 in the GNT

Matthew 26 in the HARY

Matthew 26 in the HNT

Matthew 26 in the IRVA

Matthew 26 in the IRVB

Matthew 26 in the IRVG

Matthew 26 in the IRVH

Matthew 26 in the IRVK

Matthew 26 in the IRVM

Matthew 26 in the IRVM2

Matthew 26 in the IRVO

Matthew 26 in the IRVP

Matthew 26 in the IRVT

Matthew 26 in the IRVT2

Matthew 26 in the IRVU

Matthew 26 in the ISVN

Matthew 26 in the JSNT

Matthew 26 in the KAPI

Matthew 26 in the KBT1ETNIK

Matthew 26 in the KBV

Matthew 26 in the KJV

Matthew 26 in the KNFD

Matthew 26 in the LBA

Matthew 26 in the LBLA

Matthew 26 in the LNT

Matthew 26 in the LSV

Matthew 26 in the MAAL

Matthew 26 in the MBV

Matthew 26 in the MBV2

Matthew 26 in the MHNT

Matthew 26 in the MKNFD

Matthew 26 in the MNG

Matthew 26 in the MNT

Matthew 26 in the MNT2

Matthew 26 in the MRS1T

Matthew 26 in the NAA

Matthew 26 in the NASB

Matthew 26 in the NBLA

Matthew 26 in the NBS

Matthew 26 in the NBVTP

Matthew 26 in the NET2

Matthew 26 in the NIV11

Matthew 26 in the NNT

Matthew 26 in the NNT2

Matthew 26 in the NNT3

Matthew 26 in the PDDPT

Matthew 26 in the PFNT

Matthew 26 in the RMNT

Matthew 26 in the SBIAS

Matthew 26 in the SBIBS

Matthew 26 in the SBIBS2

Matthew 26 in the SBICS

Matthew 26 in the SBIDS

Matthew 26 in the SBIGS

Matthew 26 in the SBIHS

Matthew 26 in the SBIIS

Matthew 26 in the SBIIS2

Matthew 26 in the SBIIS3

Matthew 26 in the SBIKS

Matthew 26 in the SBIKS2

Matthew 26 in the SBIMS

Matthew 26 in the SBIOS

Matthew 26 in the SBIPS

Matthew 26 in the SBISS

Matthew 26 in the SBITS

Matthew 26 in the SBITS2

Matthew 26 in the SBITS3

Matthew 26 in the SBITS4

Matthew 26 in the SBIUS

Matthew 26 in the SBIVS

Matthew 26 in the SBT

Matthew 26 in the SBT1E

Matthew 26 in the SCHL

Matthew 26 in the SNT

Matthew 26 in the SUSU

Matthew 26 in the SUSU2

Matthew 26 in the SYNO

Matthew 26 in the TBIAOTANT

Matthew 26 in the TBT1E

Matthew 26 in the TBT1E2

Matthew 26 in the TFTIP

Matthew 26 in the TFTU

Matthew 26 in the TGNTATF3T

Matthew 26 in the THAI

Matthew 26 in the TNFD

Matthew 26 in the TNT

Matthew 26 in the TNTIK

Matthew 26 in the TNTIL

Matthew 26 in the TNTIN

Matthew 26 in the TNTIP

Matthew 26 in the TNTIZ

Matthew 26 in the TOMA

Matthew 26 in the TTENT

Matthew 26 in the UBG

Matthew 26 in the UGV

Matthew 26 in the UGV2

Matthew 26 in the UGV3

Matthew 26 in the VBL

Matthew 26 in the VDCC

Matthew 26 in the YALU

Matthew 26 in the YAPE

Matthew 26 in the YBVTP

Matthew 26 in the ZBP