Mark 15 (BOGWICC)

1 Mmamawa, akulu a ansembe pamodzi ndi akuluakulu, aphunzitsi amalamulo ndi olamulira onse anamanga fundo. Anamumanga Yesu, namutenga ndi kukamupereka kwa Pilato. 2 Pilato anafunsa kuti, “Kodi Iwe ndi Mfumu ya Ayuda?”Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.” 3 Akulu a ansembe anamunenera zinthu zambiri. 4 Ndipo Pilato anamufunsanso Iye kuti, “Kodi Iwe suyankhapo kanthu? Tamva zinthu zambiri akukunenerazi.” 5 Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa. 6 Pa nthawi ya Phwando, panali chizolowezi chomasula munthu wamʼndende amene anthu amupempha. 7 Munthu wotchedwa Baraba anali mʼndende pamodzi ndi anthu owukira amene anapha anthu pa nthawi ya chipolowe. 8 Gulu la anthu linabwera kwa Pilato ndi kumufunsa kuti awachitire zimene amachita nthawi zonse. 9 “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” Pilato anafunsa, 10 podziwa kuti akulu a ansembe anamupereka Yesu kwa iye chifukwa cha nsanje. 11 Koma akulu a ansembe anasonkhezera anthu kuti Pilato amasule Baraba mʼmalo mwa Yesu. 12 Pilato anawafunsa kuti, “Kodi nanga ndichite chiyani ndi uyu amene mukumutcha mfumu ya Ayuda?” 13 Anafuwula kuti, “Mpachikeni!” 14 Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?”Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!” 15 Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe. 16 Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali. 17 Anamuveka Iye mwinjiro wofiira, kenaka analuka chipewa cha minga ndi kuyika pa mutu pake. 18 Ndipo anayamba kunena kwa lye kuti, “Ulemu kwa inu Mfumu ya Ayuda!” 19 Ndipo anamugogoda pa mutu mobwerezabwereza ndi ndodo ndi kumulavulira. Anamugwadira ndi kumulambira Iye. 20 Ndipo anamuchita chipongwe, anamuvula mwinjiro wofiira uja ndi kumuveka zovala zake. Kenaka anamutenga kuti akamupachike. 21 Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda. 22 Anafika naye Yesu pa malo otchedwa Gologota (kutanthauza kuti, malo a bade) 23 Kenaka anamupatsa Iye vinyo wosakaniza ndi mure, koma Iye sanamwe. 24 Ndipo anamupachika Iye. Anachita maere ogawana zovala zake kuti aone chimene aliyense angatenge. 25 Linali ora lachitatu mmawa pamene anamupachika Yesu. 26 Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: MFUMU YA AYUDA. 27 Achifwamba awiri anapachikidwanso pamodzi ndi Iye, wina kumanja kwake ndi wina kumanzere kwake. 28 (Ndipo malemba anakwaniritsidwa amene amati, “Iye anayikidwa mʼgulu la anthu oyipa).” 29 Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu, 30 tsika kuchoka pa mtandapo ndipo udzipulumutse wekha!” 31 Chimodzimodzinso akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamunyoza Iye pakati pawo. Iwo anati, “Anapulumutsa ena, koma sangathe kudzipulumutsa yekha! 32 Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira. 33 Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana. 34 Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” 35 Ena amene anali pafupi atamva izi anati, “Tamverani, akuyitana Eliya.” 36 Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.” 37 Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza. 38 Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. 39 Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.” 40 Amayi ena anali patali kuonerera. Pakati pawo panali Mariya Magadalena, Mariya amayi a Yakobo wamngʼono ndi Yose ndi Salome. 41 Amayi awa ankamutsatira Iye mu Galileya ndi kumutumikira Iye pa zosowa zake. Amayi enanso ambiri amene anabwera naye ku Yerusalemu analinso pomwepo. 42 Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira, 43 Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu. 44 Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale. 45 Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe. 46 Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo. 47 Mariya Magadalena ndi Mariya amayi a Yose anaona kumene anamuyika Yesu.

In Other Versions

Mark 15 in the ANGEFD

Mark 15 in the ANTPNG2D

Mark 15 in the AS21

Mark 15 in the BAGH

Mark 15 in the BBPNG

Mark 15 in the BBT1E

Mark 15 in the BDS

Mark 15 in the BEV

Mark 15 in the BHAD

Mark 15 in the BIB

Mark 15 in the BLPT

Mark 15 in the BNT

Mark 15 in the BNTABOOT

Mark 15 in the BNTLV

Mark 15 in the BOATCB

Mark 15 in the BOATCB2

Mark 15 in the BOBCV

Mark 15 in the BOCNT

Mark 15 in the BOECS

Mark 15 in the BOHCB

Mark 15 in the BOHCV

Mark 15 in the BOHLNT

Mark 15 in the BOHNTLTAL

Mark 15 in the BOICB

Mark 15 in the BOILNTAP

Mark 15 in the BOITCV

Mark 15 in the BOKCV

Mark 15 in the BOKCV2

Mark 15 in the BOKHWOG

Mark 15 in the BOKSSV

Mark 15 in the BOLCB

Mark 15 in the BOLCB2

Mark 15 in the BOMCV

Mark 15 in the BONAV

Mark 15 in the BONCB

Mark 15 in the BONLT

Mark 15 in the BONUT2

Mark 15 in the BOPLNT

Mark 15 in the BOSCB

Mark 15 in the BOSNC

Mark 15 in the BOTLNT

Mark 15 in the BOVCB

Mark 15 in the BOYCB

Mark 15 in the BPBB

Mark 15 in the BPH

Mark 15 in the BSB

Mark 15 in the CCB

Mark 15 in the CUV

Mark 15 in the CUVS

Mark 15 in the DBT

Mark 15 in the DGDNT

Mark 15 in the DHNT

Mark 15 in the DNT

Mark 15 in the ELBE

Mark 15 in the EMTV

Mark 15 in the ESV

Mark 15 in the FBV

Mark 15 in the FEB

Mark 15 in the GGMNT

Mark 15 in the GNT

Mark 15 in the HARY

Mark 15 in the HNT

Mark 15 in the IRVA

Mark 15 in the IRVB

Mark 15 in the IRVG

Mark 15 in the IRVH

Mark 15 in the IRVK

Mark 15 in the IRVM

Mark 15 in the IRVM2

Mark 15 in the IRVO

Mark 15 in the IRVP

Mark 15 in the IRVT

Mark 15 in the IRVT2

Mark 15 in the IRVU

Mark 15 in the ISVN

Mark 15 in the JSNT

Mark 15 in the KAPI

Mark 15 in the KBT1ETNIK

Mark 15 in the KBV

Mark 15 in the KJV

Mark 15 in the KNFD

Mark 15 in the LBA

Mark 15 in the LBLA

Mark 15 in the LNT

Mark 15 in the LSV

Mark 15 in the MAAL

Mark 15 in the MBV

Mark 15 in the MBV2

Mark 15 in the MHNT

Mark 15 in the MKNFD

Mark 15 in the MNG

Mark 15 in the MNT

Mark 15 in the MNT2

Mark 15 in the MRS1T

Mark 15 in the NAA

Mark 15 in the NASB

Mark 15 in the NBLA

Mark 15 in the NBS

Mark 15 in the NBVTP

Mark 15 in the NET2

Mark 15 in the NIV11

Mark 15 in the NNT

Mark 15 in the NNT2

Mark 15 in the NNT3

Mark 15 in the PDDPT

Mark 15 in the PFNT

Mark 15 in the RMNT

Mark 15 in the SBIAS

Mark 15 in the SBIBS

Mark 15 in the SBIBS2

Mark 15 in the SBICS

Mark 15 in the SBIDS

Mark 15 in the SBIGS

Mark 15 in the SBIHS

Mark 15 in the SBIIS

Mark 15 in the SBIIS2

Mark 15 in the SBIIS3

Mark 15 in the SBIKS

Mark 15 in the SBIKS2

Mark 15 in the SBIMS

Mark 15 in the SBIOS

Mark 15 in the SBIPS

Mark 15 in the SBISS

Mark 15 in the SBITS

Mark 15 in the SBITS2

Mark 15 in the SBITS3

Mark 15 in the SBITS4

Mark 15 in the SBIUS

Mark 15 in the SBIVS

Mark 15 in the SBT

Mark 15 in the SBT1E

Mark 15 in the SCHL

Mark 15 in the SNT

Mark 15 in the SUSU

Mark 15 in the SUSU2

Mark 15 in the SYNO

Mark 15 in the TBIAOTANT

Mark 15 in the TBT1E

Mark 15 in the TBT1E2

Mark 15 in the TFTIP

Mark 15 in the TFTU

Mark 15 in the TGNTATF3T

Mark 15 in the THAI

Mark 15 in the TNFD

Mark 15 in the TNT

Mark 15 in the TNTIK

Mark 15 in the TNTIL

Mark 15 in the TNTIN

Mark 15 in the TNTIP

Mark 15 in the TNTIZ

Mark 15 in the TOMA

Mark 15 in the TTENT

Mark 15 in the UBG

Mark 15 in the UGV

Mark 15 in the UGV2

Mark 15 in the UGV3

Mark 15 in the VBL

Mark 15 in the VDCC

Mark 15 in the YALU

Mark 15 in the YAPE

Mark 15 in the YBVTP

Mark 15 in the ZBP