Numbers 23 (BOGWICC)

1 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano, ndipo mukonzenso ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” 2 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo awiriwo anapereka ngʼombe imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse. 3 Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu. 4 Mulungu anakumana naye ndipo Balaamu anati, “Ndakonza maguwa asanu ndi awiri ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo nsembe ya ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzinso.” 5 Yehova anawuza Balaamu kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.” 6 Ndipo anabwerera kwa iye namupeza atayima pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu onse a Mowabu. 7 Ndipo Balaamu ananena uthenga wake:“Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu,mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa.Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga,pita nyoza Israeli.’ 8 Ndingatemberere bwanjiamene Mulungu sanawatemberere?Ndinganyoze bwanjiamene Yehova sanawanyoze? 9 Kuchokera pamwamba pa mapiri ndikuona anthu,ndikuwaona kuchokera pa zitunda.Ndikuona anthu okhala pawokha,osakhala mʼgulu limodzi ndi mitundu ina. 10 Ndani angawerenge zidzukulu za Yakobo zochuluka ngati fumbi,kapena chimodzi mwa zigawo zinayi za Israeli?Lekeni ndife imfa ya oyera mtima,ndi chimaliziro changa chikhale ngati chawo!” 11 Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!” 12 Iye anayankha kuti, “Kodi sindinayenera kuyankhula zimene Yehova anandiwuza?” 13 Kenaka Balaki anawuza Balaamu kuti, “Tiye tipite limodzi ku malo ena komwe ungawaone. Udzangoona gulu limodzi osati onsewo. Ndipo pamenepo, ukawatemberere mʼmalo mwanga.” 14 Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse. 15 Balaamu anawuza Balaki kuti, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu pamene ine ndikukakumana ndi Mulungu cha uko.” 16 Yehova anakumana ndi Balaamu ndipo anamuyankhula kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.” 17 Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?” 18 Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake:“Nyamuka Balaki ndipo tamvera;Undimvere iwe mwana wa Zipori. 19 Mulungu si munthu kuti aname,kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake.Kodi amayankhula koma osachita?Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa? 20 Wandilamula kuti ndidalitse,Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe. 21 “Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo,sanaone chovuta mu Israeli.Yehova Mulungu wawo ali nawo:mfuwu wa mfumu uli pakati pawo. 22 Mulungu wowatulutsa mʼdziko la Igupto,ali ndi mphamvu ngati za njati. 23 Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo,palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli.Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti,‘Onani zimene Mulungu wachita!’ 24 Taonani, anthu anyamuka ngati mkango waukazi;adzuka okha ngati mkango waumunaumene supuma mpaka utadya nyama imene wagwirandi kumwa magazi a nyama yogwidwayo.” 25 Ndipo Balaki anati kwa Balaamu, “Usawatemberere ndi pangʼono pomwe kapena kuwadalitsa! 26 “Balaamu anayankha Balaki kuti, ‘Kodi sindinakuwuzeni kuti ndiyenera kuchita zimene Yehova wanena?’ ” 27 Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.” 28 Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu. 29 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” 30 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse.

In Other Versions

Numbers 23 in the ANGEFD

Numbers 23 in the ANTPNG2D

Numbers 23 in the AS21

Numbers 23 in the BAGH

Numbers 23 in the BBPNG

Numbers 23 in the BBT1E

Numbers 23 in the BDS

Numbers 23 in the BEV

Numbers 23 in the BHAD

Numbers 23 in the BIB

Numbers 23 in the BLPT

Numbers 23 in the BNT

Numbers 23 in the BNTABOOT

Numbers 23 in the BNTLV

Numbers 23 in the BOATCB

Numbers 23 in the BOATCB2

Numbers 23 in the BOBCV

Numbers 23 in the BOCNT

Numbers 23 in the BOECS

Numbers 23 in the BOHCB

Numbers 23 in the BOHCV

Numbers 23 in the BOHLNT

Numbers 23 in the BOHNTLTAL

Numbers 23 in the BOICB

Numbers 23 in the BOILNTAP

Numbers 23 in the BOITCV

Numbers 23 in the BOKCV

Numbers 23 in the BOKCV2

Numbers 23 in the BOKHWOG

Numbers 23 in the BOKSSV

Numbers 23 in the BOLCB

Numbers 23 in the BOLCB2

Numbers 23 in the BOMCV

Numbers 23 in the BONAV

Numbers 23 in the BONCB

Numbers 23 in the BONLT

Numbers 23 in the BONUT2

Numbers 23 in the BOPLNT

Numbers 23 in the BOSCB

Numbers 23 in the BOSNC

Numbers 23 in the BOTLNT

Numbers 23 in the BOVCB

Numbers 23 in the BOYCB

Numbers 23 in the BPBB

Numbers 23 in the BPH

Numbers 23 in the BSB

Numbers 23 in the CCB

Numbers 23 in the CUV

Numbers 23 in the CUVS

Numbers 23 in the DBT

Numbers 23 in the DGDNT

Numbers 23 in the DHNT

Numbers 23 in the DNT

Numbers 23 in the ELBE

Numbers 23 in the EMTV

Numbers 23 in the ESV

Numbers 23 in the FBV

Numbers 23 in the FEB

Numbers 23 in the GGMNT

Numbers 23 in the GNT

Numbers 23 in the HARY

Numbers 23 in the HNT

Numbers 23 in the IRVA

Numbers 23 in the IRVB

Numbers 23 in the IRVG

Numbers 23 in the IRVH

Numbers 23 in the IRVK

Numbers 23 in the IRVM

Numbers 23 in the IRVM2

Numbers 23 in the IRVO

Numbers 23 in the IRVP

Numbers 23 in the IRVT

Numbers 23 in the IRVT2

Numbers 23 in the IRVU

Numbers 23 in the ISVN

Numbers 23 in the JSNT

Numbers 23 in the KAPI

Numbers 23 in the KBT1ETNIK

Numbers 23 in the KBV

Numbers 23 in the KJV

Numbers 23 in the KNFD

Numbers 23 in the LBA

Numbers 23 in the LBLA

Numbers 23 in the LNT

Numbers 23 in the LSV

Numbers 23 in the MAAL

Numbers 23 in the MBV

Numbers 23 in the MBV2

Numbers 23 in the MHNT

Numbers 23 in the MKNFD

Numbers 23 in the MNG

Numbers 23 in the MNT

Numbers 23 in the MNT2

Numbers 23 in the MRS1T

Numbers 23 in the NAA

Numbers 23 in the NASB

Numbers 23 in the NBLA

Numbers 23 in the NBS

Numbers 23 in the NBVTP

Numbers 23 in the NET2

Numbers 23 in the NIV11

Numbers 23 in the NNT

Numbers 23 in the NNT2

Numbers 23 in the NNT3

Numbers 23 in the PDDPT

Numbers 23 in the PFNT

Numbers 23 in the RMNT

Numbers 23 in the SBIAS

Numbers 23 in the SBIBS

Numbers 23 in the SBIBS2

Numbers 23 in the SBICS

Numbers 23 in the SBIDS

Numbers 23 in the SBIGS

Numbers 23 in the SBIHS

Numbers 23 in the SBIIS

Numbers 23 in the SBIIS2

Numbers 23 in the SBIIS3

Numbers 23 in the SBIKS

Numbers 23 in the SBIKS2

Numbers 23 in the SBIMS

Numbers 23 in the SBIOS

Numbers 23 in the SBIPS

Numbers 23 in the SBISS

Numbers 23 in the SBITS

Numbers 23 in the SBITS2

Numbers 23 in the SBITS3

Numbers 23 in the SBITS4

Numbers 23 in the SBIUS

Numbers 23 in the SBIVS

Numbers 23 in the SBT

Numbers 23 in the SBT1E

Numbers 23 in the SCHL

Numbers 23 in the SNT

Numbers 23 in the SUSU

Numbers 23 in the SUSU2

Numbers 23 in the SYNO

Numbers 23 in the TBIAOTANT

Numbers 23 in the TBT1E

Numbers 23 in the TBT1E2

Numbers 23 in the TFTIP

Numbers 23 in the TFTU

Numbers 23 in the TGNTATF3T

Numbers 23 in the THAI

Numbers 23 in the TNFD

Numbers 23 in the TNT

Numbers 23 in the TNTIK

Numbers 23 in the TNTIL

Numbers 23 in the TNTIN

Numbers 23 in the TNTIP

Numbers 23 in the TNTIZ

Numbers 23 in the TOMA

Numbers 23 in the TTENT

Numbers 23 in the UBG

Numbers 23 in the UGV

Numbers 23 in the UGV2

Numbers 23 in the UGV3

Numbers 23 in the VBL

Numbers 23 in the VDCC

Numbers 23 in the YALU

Numbers 23 in the YAPE

Numbers 23 in the YBVTP

Numbers 23 in the ZBP