Proverbs 1 (BOGWICC)

1 Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli: 2 Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo;kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama; 3 kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru,akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera. 4 Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera,achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira. 5 Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake,ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso, 6 kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo,mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko. 7 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo. 8 Mwana wanga, mvera malangizo a abambo akondipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako. 9 Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pakondiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako. 10 Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopausamawamvere. 11 Akadzati, “Tiye kuno;tikabisale kuti tiphe anthu,tikabisalire anthu osalakwa; 12 tiwameze amoyo ngati manda,ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje. 13 Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatalindi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda; 14 Bwera, chita nafe maere,ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.” 15 Mwana wanga, usayende nawo pamodzi,usatsagane nawo mʼnjira zawozo. 16 Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha,amathamangira kukhetsa magazi. 17 Nʼkopanda phindu kutchera msamphambalame zikuona! 18 Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe;amangodzitchera okha msampha! 19 Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza;chumacho chimapha mwiniwake. 20 Nzeru ikufuwula mu msewu,ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika; 21 ikufuwula pa mphambano ya misewu,ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti, 22 “Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti?Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti?Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti? 23 Tamverani mawu anga a chidzudzulo.Ine ndikukuwuzani maganizo angandi kukudziwitsani mawu anga. 24 Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera.Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala. 25 Uphungu wanga munawunyoza.Kudzudzula kwanga simunakusamale. 26 Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto;ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho. 27 Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe,tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu,mavuto ndi masautso akadzakugwerani. 28 “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha;mudzandifunafuna, koma simudzandipeza. 29 Popeza iwo anadana ndi chidziwitsondipo sanasankhe kuopa Yehova, 30 popeza iwo sanasamale malangizo angandipo ananyoza chidzudzulo changa. 31 Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awondi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena. 32 Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo,ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo. 33 Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata;adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”

In Other Versions

Proverbs 1 in the ANGEFD

Proverbs 1 in the ANTPNG2D

Proverbs 1 in the AS21

Proverbs 1 in the BAGH

Proverbs 1 in the BBPNG

Proverbs 1 in the BBT1E

Proverbs 1 in the BDS

Proverbs 1 in the BEV

Proverbs 1 in the BHAD

Proverbs 1 in the BIB

Proverbs 1 in the BLPT

Proverbs 1 in the BNT

Proverbs 1 in the BNTABOOT

Proverbs 1 in the BNTLV

Proverbs 1 in the BOATCB

Proverbs 1 in the BOATCB2

Proverbs 1 in the BOBCV

Proverbs 1 in the BOCNT

Proverbs 1 in the BOECS

Proverbs 1 in the BOHCB

Proverbs 1 in the BOHCV

Proverbs 1 in the BOHLNT

Proverbs 1 in the BOHNTLTAL

Proverbs 1 in the BOICB

Proverbs 1 in the BOILNTAP

Proverbs 1 in the BOITCV

Proverbs 1 in the BOKCV

Proverbs 1 in the BOKCV2

Proverbs 1 in the BOKHWOG

Proverbs 1 in the BOKSSV

Proverbs 1 in the BOLCB

Proverbs 1 in the BOLCB2

Proverbs 1 in the BOMCV

Proverbs 1 in the BONAV

Proverbs 1 in the BONCB

Proverbs 1 in the BONLT

Proverbs 1 in the BONUT2

Proverbs 1 in the BOPLNT

Proverbs 1 in the BOSCB

Proverbs 1 in the BOSNC

Proverbs 1 in the BOTLNT

Proverbs 1 in the BOVCB

Proverbs 1 in the BOYCB

Proverbs 1 in the BPBB

Proverbs 1 in the BPH

Proverbs 1 in the BSB

Proverbs 1 in the CCB

Proverbs 1 in the CUV

Proverbs 1 in the CUVS

Proverbs 1 in the DBT

Proverbs 1 in the DGDNT

Proverbs 1 in the DHNT

Proverbs 1 in the DNT

Proverbs 1 in the ELBE

Proverbs 1 in the EMTV

Proverbs 1 in the ESV

Proverbs 1 in the FBV

Proverbs 1 in the FEB

Proverbs 1 in the GGMNT

Proverbs 1 in the GNT

Proverbs 1 in the HARY

Proverbs 1 in the HNT

Proverbs 1 in the IRVA

Proverbs 1 in the IRVB

Proverbs 1 in the IRVG

Proverbs 1 in the IRVH

Proverbs 1 in the IRVK

Proverbs 1 in the IRVM

Proverbs 1 in the IRVM2

Proverbs 1 in the IRVO

Proverbs 1 in the IRVP

Proverbs 1 in the IRVT

Proverbs 1 in the IRVT2

Proverbs 1 in the IRVU

Proverbs 1 in the ISVN

Proverbs 1 in the JSNT

Proverbs 1 in the KAPI

Proverbs 1 in the KBT1ETNIK

Proverbs 1 in the KBV

Proverbs 1 in the KJV

Proverbs 1 in the KNFD

Proverbs 1 in the LBA

Proverbs 1 in the LBLA

Proverbs 1 in the LNT

Proverbs 1 in the LSV

Proverbs 1 in the MAAL

Proverbs 1 in the MBV

Proverbs 1 in the MBV2

Proverbs 1 in the MHNT

Proverbs 1 in the MKNFD

Proverbs 1 in the MNG

Proverbs 1 in the MNT

Proverbs 1 in the MNT2

Proverbs 1 in the MRS1T

Proverbs 1 in the NAA

Proverbs 1 in the NASB

Proverbs 1 in the NBLA

Proverbs 1 in the NBS

Proverbs 1 in the NBVTP

Proverbs 1 in the NET2

Proverbs 1 in the NIV11

Proverbs 1 in the NNT

Proverbs 1 in the NNT2

Proverbs 1 in the NNT3

Proverbs 1 in the PDDPT

Proverbs 1 in the PFNT

Proverbs 1 in the RMNT

Proverbs 1 in the SBIAS

Proverbs 1 in the SBIBS

Proverbs 1 in the SBIBS2

Proverbs 1 in the SBICS

Proverbs 1 in the SBIDS

Proverbs 1 in the SBIGS

Proverbs 1 in the SBIHS

Proverbs 1 in the SBIIS

Proverbs 1 in the SBIIS2

Proverbs 1 in the SBIIS3

Proverbs 1 in the SBIKS

Proverbs 1 in the SBIKS2

Proverbs 1 in the SBIMS

Proverbs 1 in the SBIOS

Proverbs 1 in the SBIPS

Proverbs 1 in the SBISS

Proverbs 1 in the SBITS

Proverbs 1 in the SBITS2

Proverbs 1 in the SBITS3

Proverbs 1 in the SBITS4

Proverbs 1 in the SBIUS

Proverbs 1 in the SBIVS

Proverbs 1 in the SBT

Proverbs 1 in the SBT1E

Proverbs 1 in the SCHL

Proverbs 1 in the SNT

Proverbs 1 in the SUSU

Proverbs 1 in the SUSU2

Proverbs 1 in the SYNO

Proverbs 1 in the TBIAOTANT

Proverbs 1 in the TBT1E

Proverbs 1 in the TBT1E2

Proverbs 1 in the TFTIP

Proverbs 1 in the TFTU

Proverbs 1 in the TGNTATF3T

Proverbs 1 in the THAI

Proverbs 1 in the TNFD

Proverbs 1 in the TNT

Proverbs 1 in the TNTIK

Proverbs 1 in the TNTIL

Proverbs 1 in the TNTIN

Proverbs 1 in the TNTIP

Proverbs 1 in the TNTIZ

Proverbs 1 in the TOMA

Proverbs 1 in the TTENT

Proverbs 1 in the UBG

Proverbs 1 in the UGV

Proverbs 1 in the UGV2

Proverbs 1 in the UGV3

Proverbs 1 in the VBL

Proverbs 1 in the VDCC

Proverbs 1 in the YALU

Proverbs 1 in the YAPE

Proverbs 1 in the YBVTP

Proverbs 1 in the ZBP