Psalms 11 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 1 Mwa Yehova ine ndimathawiramo.Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,“Thawira ku phiri lako ngati mbalame. 2 Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,pobisala pawo kuti alaseolungama mtima. 3 Tsono ngati maziko awonongeka,olungama angachite chiyani?” 4 Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;maso ake amawayesa. 5 Yehova amayesa olungama,koma moyo wake umadana ndi oyipa,amene amakonda zachiwawa. 6 Iye adzakhuthulira pa oyipamakala amoto ndi sulufule woyaka;mphepo yotentha idzakhala yowayenera. 7 Pakuti Yehova ndi wolungama,Iye amakonda chilungamo;ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.