Psalms 127 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni. 1 Yehova akapanda kumanga nyumba,omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.Yehova akapanda kulondera mzinda,mlonda akanangolondera pachabe. 2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawandi kusagona msanga madzulo,kuvutikira chakudya choti mudye,pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda. 3 Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,ana ndi mphotho yochokera kwa Iye. 4 Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanjamwa munthu wankhondo. 5 Wodala munthuamene motengera mivi mwake mwadzaza.Iwo sadzachititsidwa manyazipamene alimbana ndi adani awo pa zipata.