Revelation 3 (BOGWICC)
1 “Lembera mngelo wampingo wa ku Sarde kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene amasunga mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri. Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zako; umadziwika kuti ndiwe wamoyo koma ndiwe wakufa. 2 Dzuka! Limbitsa zimene zatsalira zomwe zatsala pangʼono kufa, pakuti ndaona kuti ntchito zako nʼzosakwanira pamaso pa Mulungu. 3 Choncho, kumbukira zimene unalandira ndi kumva; uzisunge ndipo ulape. Koma ngati sudzuka, ndidzabwera ngati mbala ndipo sudzadziwa nthawi imene ndidzabwere kwanu. 4 Komabe uli ndi anthu angapo mu Sarde amene sanadetse zovala zawo. Amenewa adzayenda ndi Ine atavala zoyera popeza ndi oyenera kutero. 5 Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake. 6 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.” 7 “Lembera mngelo wampingo wa ku Filadefiya kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi woyera ndi woonadi, amene ali ndi kiyi ya Davide. Iye akatsekula palibe amene angatseke; ndipo akatseka palibe amene angatsekule. 8 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa ntchito zako. Taona, ndakutsekulira pa khomo ndipo palibe wina amene angatseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa komabe wasunga mawu anga ndipo sunandikane. 9 Amene ndi mpingo wa Satana, amene amadzitcha kuti ndi Ayuda pamene sali choncho, koma ndi onama, ndidzawabweretsa kwa inu ndi kuwagwetsa pansi pa mapazi anu kuti adzazindikire kuti ndimakukondani. 10 Popeza mwasunga mawu anga woti mupirire ndipo mwawugwira mtima, Inenso ndidzakupulumutsani nthawi ya mayesero imene idzabwera pa dziko lonse lapansi kuyesa onse okhala pa dziko lapansi. 11 Ine ndikubwera msanga. Gwiritsitsa chimene uli nacho kuti wina angakulande chipewa chako chaufumu. 12 Iye amene adzapambane ndidzamusandutsa mzati wa mʼNyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso. Pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano, umene ukubwera pansi kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga; ndipo pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano. 13 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.’ ” 14 “Lembera mngelo wampingo wa ku Laodikaya kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa Ameni, mboni yokhulupirika ndi yoona, gwero la zolengedwa zonse za Mulungu. 15 Ine ndimadziwa ntchito zako, kuti sindiwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha! 16 Tsono popeza ndiwe wofunda chabe, sindiwe wotentha kapena wozizira, ndatsala pangʼono kuti ndikulavule mʼkamwa mwanga. 17 Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche. 18 Ndikukulangiza kuti ugule kwa Ine golide woyengedwa ndi moto kuti ukhale wolemera. Ugule zovala zoyera kuti uvale ndi kuphimba umaliseche wako wochititsa manyaziwo. Ndiponso ugule kwa Ine mankhwala a mʼmaso kuti uwone. 19 Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa. 20 Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo. 21 Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu. 22 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”
In Other Versions
Revelation 3 in the ANGEFD
Revelation 3 in the ANTPNG2D
Revelation 3 in the AS21
Revelation 3 in the BAGH
Revelation 3 in the BBPNG
Revelation 3 in the BBT1E
Revelation 3 in the BDS
Revelation 3 in the BEV
Revelation 3 in the BHAD
Revelation 3 in the BIB
Revelation 3 in the BLPT
Revelation 3 in the BNT
Revelation 3 in the BNTABOOT
Revelation 3 in the BNTLV
Revelation 3 in the BOATCB
Revelation 3 in the BOATCB2
Revelation 3 in the BOBCV
Revelation 3 in the BOCNT
Revelation 3 in the BOECS
Revelation 3 in the BOHCB
Revelation 3 in the BOHCV
Revelation 3 in the BOHLNT
Revelation 3 in the BOHNTLTAL
Revelation 3 in the BOICB
Revelation 3 in the BOILNTAP
Revelation 3 in the BOITCV
Revelation 3 in the BOKCV
Revelation 3 in the BOKCV2
Revelation 3 in the BOKHWOG
Revelation 3 in the BOKSSV
Revelation 3 in the BOLCB
Revelation 3 in the BOLCB2
Revelation 3 in the BOMCV
Revelation 3 in the BONAV
Revelation 3 in the BONCB
Revelation 3 in the BONLT
Revelation 3 in the BONUT2
Revelation 3 in the BOPLNT
Revelation 3 in the BOSCB
Revelation 3 in the BOSNC
Revelation 3 in the BOTLNT
Revelation 3 in the BOVCB
Revelation 3 in the BOYCB
Revelation 3 in the BPBB
Revelation 3 in the BPH
Revelation 3 in the BSB
Revelation 3 in the CCB
Revelation 3 in the CUV
Revelation 3 in the CUVS
Revelation 3 in the DBT
Revelation 3 in the DGDNT
Revelation 3 in the DHNT
Revelation 3 in the DNT
Revelation 3 in the ELBE
Revelation 3 in the EMTV
Revelation 3 in the ESV
Revelation 3 in the FBV
Revelation 3 in the FEB
Revelation 3 in the GGMNT
Revelation 3 in the GNT
Revelation 3 in the HARY
Revelation 3 in the HNT
Revelation 3 in the IRVA
Revelation 3 in the IRVB
Revelation 3 in the IRVG
Revelation 3 in the IRVH
Revelation 3 in the IRVK
Revelation 3 in the IRVM
Revelation 3 in the IRVM2
Revelation 3 in the IRVO
Revelation 3 in the IRVP
Revelation 3 in the IRVT
Revelation 3 in the IRVT2
Revelation 3 in the IRVU
Revelation 3 in the ISVN
Revelation 3 in the JSNT
Revelation 3 in the KAPI
Revelation 3 in the KBT1ETNIK
Revelation 3 in the KBV
Revelation 3 in the KJV
Revelation 3 in the KNFD
Revelation 3 in the LBA
Revelation 3 in the LBLA
Revelation 3 in the LNT
Revelation 3 in the LSV
Revelation 3 in the MAAL
Revelation 3 in the MBV
Revelation 3 in the MBV2
Revelation 3 in the MHNT
Revelation 3 in the MKNFD
Revelation 3 in the MNG
Revelation 3 in the MNT
Revelation 3 in the MNT2
Revelation 3 in the MRS1T
Revelation 3 in the NAA
Revelation 3 in the NASB
Revelation 3 in the NBLA
Revelation 3 in the NBS
Revelation 3 in the NBVTP
Revelation 3 in the NET2
Revelation 3 in the NIV11
Revelation 3 in the NNT
Revelation 3 in the NNT2
Revelation 3 in the NNT3
Revelation 3 in the PDDPT
Revelation 3 in the PFNT
Revelation 3 in the RMNT
Revelation 3 in the SBIAS
Revelation 3 in the SBIBS
Revelation 3 in the SBIBS2
Revelation 3 in the SBICS
Revelation 3 in the SBIDS
Revelation 3 in the SBIGS
Revelation 3 in the SBIHS
Revelation 3 in the SBIIS
Revelation 3 in the SBIIS2
Revelation 3 in the SBIIS3
Revelation 3 in the SBIKS
Revelation 3 in the SBIKS2
Revelation 3 in the SBIMS
Revelation 3 in the SBIOS
Revelation 3 in the SBIPS
Revelation 3 in the SBISS
Revelation 3 in the SBITS
Revelation 3 in the SBITS2
Revelation 3 in the SBITS3
Revelation 3 in the SBITS4
Revelation 3 in the SBIUS
Revelation 3 in the SBIVS
Revelation 3 in the SBT
Revelation 3 in the SBT1E
Revelation 3 in the SCHL
Revelation 3 in the SNT
Revelation 3 in the SUSU
Revelation 3 in the SUSU2
Revelation 3 in the SYNO
Revelation 3 in the TBIAOTANT
Revelation 3 in the TBT1E
Revelation 3 in the TBT1E2
Revelation 3 in the TFTIP
Revelation 3 in the TFTU
Revelation 3 in the TGNTATF3T
Revelation 3 in the THAI
Revelation 3 in the TNFD
Revelation 3 in the TNT
Revelation 3 in the TNTIK
Revelation 3 in the TNTIL
Revelation 3 in the TNTIN
Revelation 3 in the TNTIP
Revelation 3 in the TNTIZ
Revelation 3 in the TOMA
Revelation 3 in the TTENT
Revelation 3 in the UBG
Revelation 3 in the UGV
Revelation 3 in the UGV2
Revelation 3 in the UGV3
Revelation 3 in the VBL
Revelation 3 in the VDCC
Revelation 3 in the YALU
Revelation 3 in the YAPE
Revelation 3 in the YBVTP
Revelation 3 in the ZBP