Revelation 9 (BOGWICC)

1 Mngelo wachisanu anayimba lipenga lake, ndipo ndinaona nyenyezi ikugwa pa dziko lapansi kuchokera ku thambo. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi ya ku chidzenje chakuya. 2 Nyenyeziyo itatsekula pa chidzenje chakuyacho panatuluka utsi ngati wochokera mʼngʼanjo yayikulu. Dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsi ochokera mʼdzenjemo. 3 Ndipo mʼkati mwa utsimo munatuluka dzombe kukalowa mʼdziko lapansi ndipo linapatsidwa mphamvu zoluma ngati za zinkhanira pa dziko lapansi. 4 Dzombelo linalamulidwa kuti lisawononge udzu wa pa dziko lapansi, kapena chomera chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu okhawo amene analibe chizindikiro cha Mulungu pa mphumi zawo. 5 Silinapatsidwe mphamvu yowapha koma yowazunza kwa miyezi isanu. Ndipo ululu umene anthuwo anawumva unali ngati wa chinkhanira chikaluma munthu. 6 Masiku amenewo anthu adzafunafuna imfa koma sadzayipeza. Adzalakalaka kufa koma imfa izidzawathawa. 7 Dzombe linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali ngati zipewa zaufumu zagolide ndipo nkhope zawo ngati za anthu. 8 Tsitsi lawo linali ngati la amayi, mano awo ngati a mikango. 9 Dzombelo linavala za pachifuwa zachitsulo. Phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta ankhondo ambiri okokedwa ndi akavalo othamangira ku nkhondo. 10 Linali ndi michira ngati zinkhanira ndi mbola. Mʼmichira yake munali mphamvu yozunza nayo anthu kwa miyezi isanu. 11 Mfumu yawo inali mngelo wolamulira Chidzenje chakuya chija. Mʼchihebri dzina lake ndi Abadoni ndipo mʼChigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, Wowononga). 12 Tsoka loyamba lapita; matsoka ena awiri akubwerabe. 13 Mngelo wachisanu ndi chimodzi anayimba lipenga lake, ndipo ndinamva liwu lochokera ku ngodya zinayi za guwa lansembe lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu. 14 Liwulo linati kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi amene anali ndi lipenga uja, “Masula angelo anayi amene anamangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.” 15 Ndipo anamasulidwadi angelo anayi aja amene anasungidwa kukonzekera ora ili, tsiku ili, mwezi uwu ndi chaka ichi kuti aphe limodzi la magawo atatu a anthu. 16 Ndinamva chiwerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali 200 miliyoni. 17 Akavalo ndi okwerapo amene ndinaona mʼmasomphenya anga ankaoneka motere: Zovala za pachifukwa pawo zinali zofiira ngati moto, zobiriwira ngati utsi, ndi zachikasu ngati miyala ya sulufule. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango ndipo mʼkamwa mwawo munkatuluka moto, utsi ndi sulufule. 18 Gawo limodzi la magawo atatu a anthu linaphedwa ndi miliri yamoto, utsi ndi sulufule zimene zinkachoka mʼkamwa mwawo. 19 Mphamvu za akavalowo inali mʼkamwa mwawo ndi mʼmichira mwawo; pakuti michira yawo inali ngati njoka; ndi mitu imene inkalumira. 20 Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula. 21 Sanalapenso kuleka zakupha, zamatsenga awo, zachigololo zawo kapena umbava wawo.

In Other Versions

Revelation 9 in the ANGEFD

Revelation 9 in the ANTPNG2D

Revelation 9 in the AS21

Revelation 9 in the BAGH

Revelation 9 in the BBPNG

Revelation 9 in the BBT1E

Revelation 9 in the BDS

Revelation 9 in the BEV

Revelation 9 in the BHAD

Revelation 9 in the BIB

Revelation 9 in the BLPT

Revelation 9 in the BNT

Revelation 9 in the BNTABOOT

Revelation 9 in the BNTLV

Revelation 9 in the BOATCB

Revelation 9 in the BOATCB2

Revelation 9 in the BOBCV

Revelation 9 in the BOCNT

Revelation 9 in the BOECS

Revelation 9 in the BOHCB

Revelation 9 in the BOHCV

Revelation 9 in the BOHLNT

Revelation 9 in the BOHNTLTAL

Revelation 9 in the BOICB

Revelation 9 in the BOILNTAP

Revelation 9 in the BOITCV

Revelation 9 in the BOKCV

Revelation 9 in the BOKCV2

Revelation 9 in the BOKHWOG

Revelation 9 in the BOKSSV

Revelation 9 in the BOLCB

Revelation 9 in the BOLCB2

Revelation 9 in the BOMCV

Revelation 9 in the BONAV

Revelation 9 in the BONCB

Revelation 9 in the BONLT

Revelation 9 in the BONUT2

Revelation 9 in the BOPLNT

Revelation 9 in the BOSCB

Revelation 9 in the BOSNC

Revelation 9 in the BOTLNT

Revelation 9 in the BOVCB

Revelation 9 in the BOYCB

Revelation 9 in the BPBB

Revelation 9 in the BPH

Revelation 9 in the BSB

Revelation 9 in the CCB

Revelation 9 in the CUV

Revelation 9 in the CUVS

Revelation 9 in the DBT

Revelation 9 in the DGDNT

Revelation 9 in the DHNT

Revelation 9 in the DNT

Revelation 9 in the ELBE

Revelation 9 in the EMTV

Revelation 9 in the ESV

Revelation 9 in the FBV

Revelation 9 in the FEB

Revelation 9 in the GGMNT

Revelation 9 in the GNT

Revelation 9 in the HARY

Revelation 9 in the HNT

Revelation 9 in the IRVA

Revelation 9 in the IRVB

Revelation 9 in the IRVG

Revelation 9 in the IRVH

Revelation 9 in the IRVK

Revelation 9 in the IRVM

Revelation 9 in the IRVM2

Revelation 9 in the IRVO

Revelation 9 in the IRVP

Revelation 9 in the IRVT

Revelation 9 in the IRVT2

Revelation 9 in the IRVU

Revelation 9 in the ISVN

Revelation 9 in the JSNT

Revelation 9 in the KAPI

Revelation 9 in the KBT1ETNIK

Revelation 9 in the KBV

Revelation 9 in the KJV

Revelation 9 in the KNFD

Revelation 9 in the LBA

Revelation 9 in the LBLA

Revelation 9 in the LNT

Revelation 9 in the LSV

Revelation 9 in the MAAL

Revelation 9 in the MBV

Revelation 9 in the MBV2

Revelation 9 in the MHNT

Revelation 9 in the MKNFD

Revelation 9 in the MNG

Revelation 9 in the MNT

Revelation 9 in the MNT2

Revelation 9 in the MRS1T

Revelation 9 in the NAA

Revelation 9 in the NASB

Revelation 9 in the NBLA

Revelation 9 in the NBS

Revelation 9 in the NBVTP

Revelation 9 in the NET2

Revelation 9 in the NIV11

Revelation 9 in the NNT

Revelation 9 in the NNT2

Revelation 9 in the NNT3

Revelation 9 in the PDDPT

Revelation 9 in the PFNT

Revelation 9 in the RMNT

Revelation 9 in the SBIAS

Revelation 9 in the SBIBS

Revelation 9 in the SBIBS2

Revelation 9 in the SBICS

Revelation 9 in the SBIDS

Revelation 9 in the SBIGS

Revelation 9 in the SBIHS

Revelation 9 in the SBIIS

Revelation 9 in the SBIIS2

Revelation 9 in the SBIIS3

Revelation 9 in the SBIKS

Revelation 9 in the SBIKS2

Revelation 9 in the SBIMS

Revelation 9 in the SBIOS

Revelation 9 in the SBIPS

Revelation 9 in the SBISS

Revelation 9 in the SBITS

Revelation 9 in the SBITS2

Revelation 9 in the SBITS3

Revelation 9 in the SBITS4

Revelation 9 in the SBIUS

Revelation 9 in the SBIVS

Revelation 9 in the SBT

Revelation 9 in the SBT1E

Revelation 9 in the SCHL

Revelation 9 in the SNT

Revelation 9 in the SUSU

Revelation 9 in the SUSU2

Revelation 9 in the SYNO

Revelation 9 in the TBIAOTANT

Revelation 9 in the TBT1E

Revelation 9 in the TBT1E2

Revelation 9 in the TFTIP

Revelation 9 in the TFTU

Revelation 9 in the TGNTATF3T

Revelation 9 in the THAI

Revelation 9 in the TNFD

Revelation 9 in the TNT

Revelation 9 in the TNTIK

Revelation 9 in the TNTIL

Revelation 9 in the TNTIN

Revelation 9 in the TNTIP

Revelation 9 in the TNTIZ

Revelation 9 in the TOMA

Revelation 9 in the TTENT

Revelation 9 in the UBG

Revelation 9 in the UGV

Revelation 9 in the UGV2

Revelation 9 in the UGV3

Revelation 9 in the VBL

Revelation 9 in the VDCC

Revelation 9 in the YALU

Revelation 9 in the YAPE

Revelation 9 in the YBVTP

Revelation 9 in the ZBP