Romans 2 (BOGWICC)

1 Choncho, iwe amene umaweruza munthu wina, ulibe pokanira pakuti nthawi iliyonse pamene uweruza wina ukudzitsutsa wekha chifukwa iwe amene umaweruzawe umachitanso zinthu zomwezo. 2 Tsopano ife tikudziwa kuti chiweruzo cha Mulungu, chotsutsa amene amachita zinthu zotere, nʼchokhazikika pa choonadi. 3 Kodi ukuganiza kuti udzathawa chiweruzo cha Mulungu iwe munthu wamba, pamene uweruza ena, iwe ndi kumachitanso zomwezo? 4 Kodi kapena ukupeputsa kukoma mtima kwa Mulungu, kuleza mtima kwake ndi kupirira kwake? Kodi sukuzindikira kuti kukoma mtima kwakeko, nʼkofuna kuti iweyo ulape machimo ako? 5 Koma pakuti ndiwe wosamvera ndi wa mtima wosafuna kulapa, ukudzisungira chilango pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu, pamene chiweruzo cholungama cha Mulungu chidzaonetsedwa. 6 Mulungu adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. 7 Iye adzapereka moyo wosatha kwa amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pochita ntchito zabwino mopirira. 8 Koma Mulungu adzakhuthulira mkwiyo ndi ukali wake pa amene amachita zofuna zawo ndi kukana choonadi nʼkumatsatira zoyipa. 9 Masautso ndi zowawa zidzagwera munthu aliyense amene amachita zonyansa, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. 10 Koma ulemerero, ulemu ndi mtendere zidzakhala kwa aliyense amene amachita zabwino, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. 11 Pajatu Mulungu alibe tsankho. 12 Onse amene amachimwa osadziwa Malamulo, adzawonongeka ngakhale kuti sadziwa Malamulowo. Ndipo onse amene amachimwa akudziwa Malamulo adzaweruzidwa potsata Malamulowo. 13 Pakuti si amene amangomva Malamulo amene amakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma ndi okhawo amene amachita zili mʼMalamulomo amene adzatchedwa olungama. 14 Ndithu, pamene a mitundu ina, amene alibe Malamulo, koma mwachikhalidwe chawo amachita zimene zili mʼMalamulo, iwowo ndi Malamulo pa iwo okha, ngakhale kuti alibe Malamulowo. 15 Ntchito zawo zimaonetsa kuti Malamulowo alembedwa mʼmitima mwawo. Chikumbumtima chawonso chimawachitira umboni pakuti maganizo awo amawatsutsa kapena kuwavomereza. 16 Izi zidzachitika pa tsiku limene Mulungu adzaweruza zinsinsi za anthu kudzera mwa Yesu Khristu, monga momwe Uthenga wanga Wabwino unenera. 17 Koma iweyo, amene umadzitcha kuti ndiwe Myuda, umadalira Malamulo, ndipo umanyadira ubale wako ndi Mulungu, 18 ngati umadziwa chifuniro chake, ndi kudziwa zoyenera kuchita chifukwa unaphunzitsidwa ndi Malamulo; 19 ngati umadziwadi kuti ndiwe mtsogoleri wa osaona, nyale yowunikira amene ali mu mdima, 20 mlangizi wa anthu opusa, mphunzitsi wa makanda, chifukwa umadziwa kuti mʼMalamulo uli nayo nzeru yonse ndi choonadi, 21 tsono, iwe amene umaphunzitsa ena, sudziphunzitsa wekha kodi? Kodi iwe amene umalalikira kuti anthu asabe, umabanso? 22 Kodi iwe amene umanena kuti anthu asachite chigololo, umachitanso chigololo? Kodi iwe amene umanyasidwa ndi mafano, umalandanso za mʼnyumba zopembedzera mafanowo? 23 Kodi iwe amene umadzitama ndi Malamulo, umamuchititsa manyazi Mulungu posamvera Malamulowo? 24 Monga kwalembedwa, “Dzina la Mulungu likuchitidwa chipongwe pakati pa a mitundu ina chifukwa cha inu.” 25 Mdulidwe umakhala ndi phindu ngati usunga Malamulo, koma ngati sumvera Malamulo, iweyo umakhala ngati kuti sunachite mdulidwe. 26 Ngati amene sanachite mdulidwe achita zomwe zili mʼMalamulo, kodi sadzatengedwa ngati ochita mdulidwe? 27 Munthu amene sanachite mdulidwe mʼthupi koma amamvera Malamulo adzakutsutsa iwe wosamvera Malamulowe, ngakhale kuti uli nawo Malamulo olembedwawo. 28 Myuda weniweni si amene angooneka ngati Myuda pamaso pa anthu, ndipo mdulidwe weniweni si umene umangochitika mʼthupi pamaso pa anthu. 29 Ayi, Myuda weniweni ndi amene ali Myuda mu mtima mwake, ndipo mdulidwe weniweni ndi wa mtima, wochitika ndi Mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ayi.

In Other Versions

Romans 2 in the ANGEFD

Romans 2 in the ANTPNG2D

Romans 2 in the AS21

Romans 2 in the BAGH

Romans 2 in the BBPNG

Romans 2 in the BBT1E

Romans 2 in the BDS

Romans 2 in the BEV

Romans 2 in the BHAD

Romans 2 in the BIB

Romans 2 in the BLPT

Romans 2 in the BNT

Romans 2 in the BNTABOOT

Romans 2 in the BNTLV

Romans 2 in the BOATCB

Romans 2 in the BOATCB2

Romans 2 in the BOBCV

Romans 2 in the BOCNT

Romans 2 in the BOECS

Romans 2 in the BOHCB

Romans 2 in the BOHCV

Romans 2 in the BOHLNT

Romans 2 in the BOHNTLTAL

Romans 2 in the BOICB

Romans 2 in the BOILNTAP

Romans 2 in the BOITCV

Romans 2 in the BOKCV

Romans 2 in the BOKCV2

Romans 2 in the BOKHWOG

Romans 2 in the BOKSSV

Romans 2 in the BOLCB

Romans 2 in the BOLCB2

Romans 2 in the BOMCV

Romans 2 in the BONAV

Romans 2 in the BONCB

Romans 2 in the BONLT

Romans 2 in the BONUT2

Romans 2 in the BOPLNT

Romans 2 in the BOSCB

Romans 2 in the BOSNC

Romans 2 in the BOTLNT

Romans 2 in the BOVCB

Romans 2 in the BOYCB

Romans 2 in the BPBB

Romans 2 in the BPH

Romans 2 in the BSB

Romans 2 in the CCB

Romans 2 in the CUV

Romans 2 in the CUVS

Romans 2 in the DBT

Romans 2 in the DGDNT

Romans 2 in the DHNT

Romans 2 in the DNT

Romans 2 in the ELBE

Romans 2 in the EMTV

Romans 2 in the ESV

Romans 2 in the FBV

Romans 2 in the FEB

Romans 2 in the GGMNT

Romans 2 in the GNT

Romans 2 in the HARY

Romans 2 in the HNT

Romans 2 in the IRVA

Romans 2 in the IRVB

Romans 2 in the IRVG

Romans 2 in the IRVH

Romans 2 in the IRVK

Romans 2 in the IRVM

Romans 2 in the IRVM2

Romans 2 in the IRVO

Romans 2 in the IRVP

Romans 2 in the IRVT

Romans 2 in the IRVT2

Romans 2 in the IRVU

Romans 2 in the ISVN

Romans 2 in the JSNT

Romans 2 in the KAPI

Romans 2 in the KBT1ETNIK

Romans 2 in the KBV

Romans 2 in the KJV

Romans 2 in the KNFD

Romans 2 in the LBA

Romans 2 in the LBLA

Romans 2 in the LNT

Romans 2 in the LSV

Romans 2 in the MAAL

Romans 2 in the MBV

Romans 2 in the MBV2

Romans 2 in the MHNT

Romans 2 in the MKNFD

Romans 2 in the MNG

Romans 2 in the MNT

Romans 2 in the MNT2

Romans 2 in the MRS1T

Romans 2 in the NAA

Romans 2 in the NASB

Romans 2 in the NBLA

Romans 2 in the NBS

Romans 2 in the NBVTP

Romans 2 in the NET2

Romans 2 in the NIV11

Romans 2 in the NNT

Romans 2 in the NNT2

Romans 2 in the NNT3

Romans 2 in the PDDPT

Romans 2 in the PFNT

Romans 2 in the RMNT

Romans 2 in the SBIAS

Romans 2 in the SBIBS

Romans 2 in the SBIBS2

Romans 2 in the SBICS

Romans 2 in the SBIDS

Romans 2 in the SBIGS

Romans 2 in the SBIHS

Romans 2 in the SBIIS

Romans 2 in the SBIIS2

Romans 2 in the SBIIS3

Romans 2 in the SBIKS

Romans 2 in the SBIKS2

Romans 2 in the SBIMS

Romans 2 in the SBIOS

Romans 2 in the SBIPS

Romans 2 in the SBISS

Romans 2 in the SBITS

Romans 2 in the SBITS2

Romans 2 in the SBITS3

Romans 2 in the SBITS4

Romans 2 in the SBIUS

Romans 2 in the SBIVS

Romans 2 in the SBT

Romans 2 in the SBT1E

Romans 2 in the SCHL

Romans 2 in the SNT

Romans 2 in the SUSU

Romans 2 in the SUSU2

Romans 2 in the SYNO

Romans 2 in the TBIAOTANT

Romans 2 in the TBT1E

Romans 2 in the TBT1E2

Romans 2 in the TFTIP

Romans 2 in the TFTU

Romans 2 in the TGNTATF3T

Romans 2 in the THAI

Romans 2 in the TNFD

Romans 2 in the TNT

Romans 2 in the TNTIK

Romans 2 in the TNTIL

Romans 2 in the TNTIN

Romans 2 in the TNTIP

Romans 2 in the TNTIZ

Romans 2 in the TOMA

Romans 2 in the TTENT

Romans 2 in the UBG

Romans 2 in the UGV

Romans 2 in the UGV2

Romans 2 in the UGV3

Romans 2 in the VBL

Romans 2 in the VDCC

Romans 2 in the YALU

Romans 2 in the YAPE

Romans 2 in the YBVTP

Romans 2 in the ZBP