Zephaniah 1 (BOGWICC)

1 Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda. 2 “Ndidzawononga kotheratu zinthu zonsepa dziko lapansi,”akutero Yehova. 3 “Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe;ndidzawononga mbalame zamlengalengandi nsomba za mʼnyanja.Ndidzawononga anthu oyipa,ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,”akutero Yehova. 4 Ndidzatambasula dzanja langa pa Yudandi onse okhala mu Yerusalemu.Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala,mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano: 5 amene amagwada pa madenga a nyumba zawokupembedza zolengedwa zamumlengalenga,amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova,komanso mʼdzina la Moleki, 6 amene abwerera mʼmbuyo osatsata Yehova,osafunafuna kapena kupempha nzeru kwa Yehova. 7 Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova,chifukwa tsiku la Yehova layandikira.Yehova wakonzekera kupereka nsembe;wapatula iwo amene wawayitana. 8 Pa tsiku la nsembe ya Yehovandidzalanga akalongandi ana aamuna a mfumundi onse amene amavalazovala zachilendo. 9 Pa tsiku limenelo ndidzalangaonse amene safuna kuponda pa chiwundo,amene amadzaza nyumba ya ambuye awondi chiwawa ndi chinyengo. 10 “Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova,“Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba,kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano,ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri. 11 Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika;a malonda anu onse adzapululidwa,ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa. 12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyalendi kulanga onse amene sakulabadira,amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa,amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse,chabwino kaya choyipa.’ 13 Chuma chawo chidzafunkhidwa,nyumba zawo zidzagwetsedwa.Adzamanga nyumba,koma osakhalamo;adzadzala minda ya mpesakoma sadzamwako vinyo wake.” 14 Tsiku lalikulu la Yehova layandikira,layandikira ndipo lifika msanga.Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa,ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri. 15 Tsiku limenelo lidzakhala la ukali,tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni,tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko,tsiku la mdima ndi lachisoni,tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani. 16 Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo,tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwandi nsanja za pa ngodya. 17 Ndidzabweretsa msautso pa anthundipo adzayenda ngati anthu osaona,chifukwa achimwira Yehova,magazi awo adzamwazika ngati fumbindi mnofu wawo ngati ndowe. 18 Ngakhale siliva wawo kapena golide wawosadzatha kuwapulumutsapa tsiku la ukali wa Yehova.Dziko lonse lapansi lidzanyekamʼmoto wa nsanje yakechifukwa adzakantha modzidzimutsaonse okhala pa dziko lapansi.

In Other Versions

Zephaniah 1 in the ANGEFD

Zephaniah 1 in the ANTPNG2D

Zephaniah 1 in the AS21

Zephaniah 1 in the BAGH

Zephaniah 1 in the BBPNG

Zephaniah 1 in the BBT1E

Zephaniah 1 in the BDS

Zephaniah 1 in the BEV

Zephaniah 1 in the BHAD

Zephaniah 1 in the BIB

Zephaniah 1 in the BLPT

Zephaniah 1 in the BNT

Zephaniah 1 in the BNTABOOT

Zephaniah 1 in the BNTLV

Zephaniah 1 in the BOATCB

Zephaniah 1 in the BOATCB2

Zephaniah 1 in the BOBCV

Zephaniah 1 in the BOCNT

Zephaniah 1 in the BOECS

Zephaniah 1 in the BOHCB

Zephaniah 1 in the BOHCV

Zephaniah 1 in the BOHLNT

Zephaniah 1 in the BOHNTLTAL

Zephaniah 1 in the BOICB

Zephaniah 1 in the BOILNTAP

Zephaniah 1 in the BOITCV

Zephaniah 1 in the BOKCV

Zephaniah 1 in the BOKCV2

Zephaniah 1 in the BOKHWOG

Zephaniah 1 in the BOKSSV

Zephaniah 1 in the BOLCB

Zephaniah 1 in the BOLCB2

Zephaniah 1 in the BOMCV

Zephaniah 1 in the BONAV

Zephaniah 1 in the BONCB

Zephaniah 1 in the BONLT

Zephaniah 1 in the BONUT2

Zephaniah 1 in the BOPLNT

Zephaniah 1 in the BOSCB

Zephaniah 1 in the BOSNC

Zephaniah 1 in the BOTLNT

Zephaniah 1 in the BOVCB

Zephaniah 1 in the BOYCB

Zephaniah 1 in the BPBB

Zephaniah 1 in the BPH

Zephaniah 1 in the BSB

Zephaniah 1 in the CCB

Zephaniah 1 in the CUV

Zephaniah 1 in the CUVS

Zephaniah 1 in the DBT

Zephaniah 1 in the DGDNT

Zephaniah 1 in the DHNT

Zephaniah 1 in the DNT

Zephaniah 1 in the ELBE

Zephaniah 1 in the EMTV

Zephaniah 1 in the ESV

Zephaniah 1 in the FBV

Zephaniah 1 in the FEB

Zephaniah 1 in the GGMNT

Zephaniah 1 in the GNT

Zephaniah 1 in the HARY

Zephaniah 1 in the HNT

Zephaniah 1 in the IRVA

Zephaniah 1 in the IRVB

Zephaniah 1 in the IRVG

Zephaniah 1 in the IRVH

Zephaniah 1 in the IRVK

Zephaniah 1 in the IRVM

Zephaniah 1 in the IRVM2

Zephaniah 1 in the IRVO

Zephaniah 1 in the IRVP

Zephaniah 1 in the IRVT

Zephaniah 1 in the IRVT2

Zephaniah 1 in the IRVU

Zephaniah 1 in the ISVN

Zephaniah 1 in the JSNT

Zephaniah 1 in the KAPI

Zephaniah 1 in the KBT1ETNIK

Zephaniah 1 in the KBV

Zephaniah 1 in the KJV

Zephaniah 1 in the KNFD

Zephaniah 1 in the LBA

Zephaniah 1 in the LBLA

Zephaniah 1 in the LNT

Zephaniah 1 in the LSV

Zephaniah 1 in the MAAL

Zephaniah 1 in the MBV

Zephaniah 1 in the MBV2

Zephaniah 1 in the MHNT

Zephaniah 1 in the MKNFD

Zephaniah 1 in the MNG

Zephaniah 1 in the MNT

Zephaniah 1 in the MNT2

Zephaniah 1 in the MRS1T

Zephaniah 1 in the NAA

Zephaniah 1 in the NASB

Zephaniah 1 in the NBLA

Zephaniah 1 in the NBS

Zephaniah 1 in the NBVTP

Zephaniah 1 in the NET2

Zephaniah 1 in the NIV11

Zephaniah 1 in the NNT

Zephaniah 1 in the NNT2

Zephaniah 1 in the NNT3

Zephaniah 1 in the PDDPT

Zephaniah 1 in the PFNT

Zephaniah 1 in the RMNT

Zephaniah 1 in the SBIAS

Zephaniah 1 in the SBIBS

Zephaniah 1 in the SBIBS2

Zephaniah 1 in the SBICS

Zephaniah 1 in the SBIDS

Zephaniah 1 in the SBIGS

Zephaniah 1 in the SBIHS

Zephaniah 1 in the SBIIS

Zephaniah 1 in the SBIIS2

Zephaniah 1 in the SBIIS3

Zephaniah 1 in the SBIKS

Zephaniah 1 in the SBIKS2

Zephaniah 1 in the SBIMS

Zephaniah 1 in the SBIOS

Zephaniah 1 in the SBIPS

Zephaniah 1 in the SBISS

Zephaniah 1 in the SBITS

Zephaniah 1 in the SBITS2

Zephaniah 1 in the SBITS3

Zephaniah 1 in the SBITS4

Zephaniah 1 in the SBIUS

Zephaniah 1 in the SBIVS

Zephaniah 1 in the SBT

Zephaniah 1 in the SBT1E

Zephaniah 1 in the SCHL

Zephaniah 1 in the SNT

Zephaniah 1 in the SUSU

Zephaniah 1 in the SUSU2

Zephaniah 1 in the SYNO

Zephaniah 1 in the TBIAOTANT

Zephaniah 1 in the TBT1E

Zephaniah 1 in the TBT1E2

Zephaniah 1 in the TFTIP

Zephaniah 1 in the TFTU

Zephaniah 1 in the TGNTATF3T

Zephaniah 1 in the THAI

Zephaniah 1 in the TNFD

Zephaniah 1 in the TNT

Zephaniah 1 in the TNTIK

Zephaniah 1 in the TNTIL

Zephaniah 1 in the TNTIN

Zephaniah 1 in the TNTIP

Zephaniah 1 in the TNTIZ

Zephaniah 1 in the TOMA

Zephaniah 1 in the TTENT

Zephaniah 1 in the UBG

Zephaniah 1 in the UGV

Zephaniah 1 in the UGV2

Zephaniah 1 in the UGV3

Zephaniah 1 in the VBL

Zephaniah 1 in the VDCC

Zephaniah 1 in the YALU

Zephaniah 1 in the YAPE

Zephaniah 1 in the YBVTP

Zephaniah 1 in the ZBP