Acts 2 (BOGWICC)

1 Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi. 2 Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala. 3 Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo. 4 Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa. 5 Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi. 6 Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana. 7 Mothedwa nzeru anafunsana kuti, “Kodi anthu onse amene akuyankhulawa si Agalileya? 8 Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo? 9 Apanti, Amedi ndi Aelami; okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, 10 ku Frugiya ndi Pamfiliya, ku Igupto ndi ku madera a ku Libiya kufupi ndi ku Kurene; alendo ochokera ku Roma, 11 Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.” 12 Modabwa ndi mothedwa nzeru anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Zimenezi zikutanthauzanji?” 13 Koma ena anawaseka nati, “Aledzera vinyo watsopano.” 14 Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena. 15 Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa! 16 Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti: 17 “ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsirizandidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera,anyamata anu adzaona masomphenya,nkhalamba zanu zidzalota maloto. 18 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi,ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo,ndipo iwo adzanenera. 19 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalengandi zizindikiro pa dziko lapansi pano,ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo. 20 Dzuwa lidzadetsedwandipo mwezi udzaoneka ngati magazilisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye. 21 Ndipo aliyense amene adzayitanapa dzina la Ambuye adzapulumuka.’ 22 “Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa. 23 Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. 24 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa. 25 Pakuti Davide ananena za Iye kuti,“ ‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse.Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja,Ine sindidzagwedezeka. 26 Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera;thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo. 27 Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda,kapena kulekerera Woyerayo kuti awole. 28 Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo;Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’ 29 “Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino. 30 Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu. 31 Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole. 32 Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi. 33 Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi. 34 Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti,“ ‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti:Khala kudzanja langa lamanja 35 mpaka nditasandutsa adani akokukhala chopondapo mapazi ako.’ 36 “Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.” 37 Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?” 38 Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39 Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.” 40 Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.” 41 Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo. 42 Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera. 43 Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. 44 Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. 45 Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. 46 Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona. 47 Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.

In Other Versions

Acts 2 in the ANGEFD

Acts 2 in the ANTPNG2D

Acts 2 in the AS21

Acts 2 in the BAGH

Acts 2 in the BBPNG

Acts 2 in the BBT1E

Acts 2 in the BDS

Acts 2 in the BEV

Acts 2 in the BHAD

Acts 2 in the BIB

Acts 2 in the BLPT

Acts 2 in the BNT

Acts 2 in the BNTABOOT

Acts 2 in the BNTLV

Acts 2 in the BOATCB

Acts 2 in the BOATCB2

Acts 2 in the BOBCV

Acts 2 in the BOCNT

Acts 2 in the BOECS

Acts 2 in the BOHCB

Acts 2 in the BOHCV

Acts 2 in the BOHLNT

Acts 2 in the BOHNTLTAL

Acts 2 in the BOICB

Acts 2 in the BOILNTAP

Acts 2 in the BOITCV

Acts 2 in the BOKCV

Acts 2 in the BOKCV2

Acts 2 in the BOKHWOG

Acts 2 in the BOKSSV

Acts 2 in the BOLCB

Acts 2 in the BOLCB2

Acts 2 in the BOMCV

Acts 2 in the BONAV

Acts 2 in the BONCB

Acts 2 in the BONLT

Acts 2 in the BONUT2

Acts 2 in the BOPLNT

Acts 2 in the BOSCB

Acts 2 in the BOSNC

Acts 2 in the BOTLNT

Acts 2 in the BOVCB

Acts 2 in the BOYCB

Acts 2 in the BPBB

Acts 2 in the BPH

Acts 2 in the BSB

Acts 2 in the CCB

Acts 2 in the CUV

Acts 2 in the CUVS

Acts 2 in the DBT

Acts 2 in the DGDNT

Acts 2 in the DHNT

Acts 2 in the DNT

Acts 2 in the ELBE

Acts 2 in the EMTV

Acts 2 in the ESV

Acts 2 in the FBV

Acts 2 in the FEB

Acts 2 in the GGMNT

Acts 2 in the GNT

Acts 2 in the HARY

Acts 2 in the HNT

Acts 2 in the IRVA

Acts 2 in the IRVB

Acts 2 in the IRVG

Acts 2 in the IRVH

Acts 2 in the IRVK

Acts 2 in the IRVM

Acts 2 in the IRVM2

Acts 2 in the IRVO

Acts 2 in the IRVP

Acts 2 in the IRVT

Acts 2 in the IRVT2

Acts 2 in the IRVU

Acts 2 in the ISVN

Acts 2 in the JSNT

Acts 2 in the KAPI

Acts 2 in the KBT1ETNIK

Acts 2 in the KBV

Acts 2 in the KJV

Acts 2 in the KNFD

Acts 2 in the LBA

Acts 2 in the LBLA

Acts 2 in the LNT

Acts 2 in the LSV

Acts 2 in the MAAL

Acts 2 in the MBV

Acts 2 in the MBV2

Acts 2 in the MHNT

Acts 2 in the MKNFD

Acts 2 in the MNG

Acts 2 in the MNT

Acts 2 in the MNT2

Acts 2 in the MRS1T

Acts 2 in the NAA

Acts 2 in the NASB

Acts 2 in the NBLA

Acts 2 in the NBS

Acts 2 in the NBVTP

Acts 2 in the NET2

Acts 2 in the NIV11

Acts 2 in the NNT

Acts 2 in the NNT2

Acts 2 in the NNT3

Acts 2 in the PDDPT

Acts 2 in the PFNT

Acts 2 in the RMNT

Acts 2 in the SBIAS

Acts 2 in the SBIBS

Acts 2 in the SBIBS2

Acts 2 in the SBICS

Acts 2 in the SBIDS

Acts 2 in the SBIGS

Acts 2 in the SBIHS

Acts 2 in the SBIIS

Acts 2 in the SBIIS2

Acts 2 in the SBIIS3

Acts 2 in the SBIKS

Acts 2 in the SBIKS2

Acts 2 in the SBIMS

Acts 2 in the SBIOS

Acts 2 in the SBIPS

Acts 2 in the SBISS

Acts 2 in the SBITS

Acts 2 in the SBITS2

Acts 2 in the SBITS3

Acts 2 in the SBITS4

Acts 2 in the SBIUS

Acts 2 in the SBIVS

Acts 2 in the SBT

Acts 2 in the SBT1E

Acts 2 in the SCHL

Acts 2 in the SNT

Acts 2 in the SUSU

Acts 2 in the SUSU2

Acts 2 in the SYNO

Acts 2 in the TBIAOTANT

Acts 2 in the TBT1E

Acts 2 in the TBT1E2

Acts 2 in the TFTIP

Acts 2 in the TFTU

Acts 2 in the TGNTATF3T

Acts 2 in the THAI

Acts 2 in the TNFD

Acts 2 in the TNT

Acts 2 in the TNTIK

Acts 2 in the TNTIL

Acts 2 in the TNTIN

Acts 2 in the TNTIP

Acts 2 in the TNTIZ

Acts 2 in the TOMA

Acts 2 in the TTENT

Acts 2 in the UBG

Acts 2 in the UGV

Acts 2 in the UGV2

Acts 2 in the UGV3

Acts 2 in the VBL

Acts 2 in the VDCC

Acts 2 in the YALU

Acts 2 in the YAPE

Acts 2 in the YBVTP

Acts 2 in the ZBP