Acts 3 (BOGWICC)
1 Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana. 2 Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo. 3 Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama. 4 Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” 5 Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo. 6 Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.” 7 Ndipo anamugwira dzanja lamanja, namuthandiza kuti ayimirire ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi akakolo ake analimba. 8 Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu. 9 Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu, 10 anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira. 11 Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni. 12 Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu? 13 Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule. 14 Koma inu munamukana Woyera ndi Wolungamayo ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wakupha anthu. 15 Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. 16 Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona. 17 “Tsopano abale ine ndikudziwa kuti inu munachita zimenezi mosadziwa, monga momwenso anachitira atsogoleri anu. 18 Koma umu ndi mmene Mulungu anakwaniritsira zimene zinanenedwa kale ndi aneneri onse, kuti Khristu adzamva zowawa. 19 Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye, 20 ndi kuti Iye atumize Yesu Khristu amene anasankhidwa chifukwa cha inu. 21 Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima. 22 Pakuti Mose anati, ‘Ambuye Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri monga ine kuchokera pakati pa anthu anu; mumvere zonse zimene iye akuwuzeni. 23 Aliyense amene sadzamvera mawu a mneneriyo, adzayenera kuchotsedwa pakati pa abale ake.’ 24 “Ndipo aneneri onse ambiri amene anayankhula kuyambira Samueli, ananeneratu za masiku ano. 25 Inu ndinu ana a aneneri ndiponso ana apangano limene Mulungu anachita ndi makolo anu. Iye anati kwa Abrahamu, ‘Anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako.’ 26 Pamene Mulungu anaukitsa mtumiki wake, anamutuma Iye poyamba kwa inu kuti akudalitseni pobweza aliyense wa inu ku zoyipa zake.”