Ezekiel 27 (BOGWICC)

1 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira Turo. 3 Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti,“Iwe Turo, umanena kuti,‘Ndine wokongola kwambiri.’ 4 Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja;amisiri ako anakukongoletsa kwambiri. 5 Anakupanga ndi matabwaa payini ochokera ku Seniri;anatenga mikungudza ya ku Lebanonikupangira mlongoti wako. 6 Ndi mitengo ya thundu ya ku Basanianapanga zopalasira zako;ndi matabwa a mitengo ya payini yochokera ku zilumba za Kitimu.Pakuti anapanga thandala lako pakati pa matabwawo panali minyanga ya njovu. 7 Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako,ndipo inakhala ngati mbendera.Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepozochokera ku zilumba za Elisa. 8 Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako.Anthu aluso ako, iwe Turo, anali mwa iwe ndiwo amene ankakuyendetsa. 9 Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako,ngati okonza zibowo zako.Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa akeankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda. 10 “Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Putianali asilikali mʼgulu lako la nkhondo.Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo zankhondo pa makoma ako,kubweretsa kwa iwe ulemerero. 11 Anthu a ku Arivadi ndi Helekiankalondera mbali zonse za mpanda wako;anthu a ku Gamadianali mu nsanja zako,Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse.Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri. 12 “Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako. 13 “Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako. 14 “Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako. 15 “Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo. 16 “Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako. 17 “Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako. 18 “Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari. 19 Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako. 20 “Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo. 21 “Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi. 22 “Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako. 23 “Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda. 24 Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba. 25 “Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinalizonyamula malonda ako.Motero iwe uli ngati sitima yapamadziyodzaza ndi katundu wolemera. 26 Anthu opalasa ako amakupititsapa nyanja yozama.Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyolapakati pa nyanja. 27 Chuma chako, katundu wako, malonda ako,okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi,anthu ako amalonda ndi asilikali ako onsendiponso aliyense amene ali mʼmenemoadzamira mʼnyanjatsiku limene udzawonongeka. 28 Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezekachifukwa cha kufuwula kwa oyendetsa sitimawo. 29 Onse amene amapalasa sitima zapamadzi,adzatuluka mʼsitima zawo;oyendetsa ndi onse owongolera sitima zapamadziadzayimirira mʼmbali mwa nyanja. 30 Iwo akufuwula,kukulira iwe kwambiri;akudzithira fumbi kumutu,ndi kudzigubuduza pa phulusa. 31 Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwendipo akuvala ziguduli.Akukulira iweyondi mitima yowawa kwambiri. 32 Akuyimba nyimboyokudandaulira nʼkumati:‘Ndani anawonongedwapo ngati Turopakati pa nyanja?’ 33 Pamene malonda ako ankawoloka nyanjaunakhutitsa mitundu yambiri ya anthu.Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chakokomanso ndi malonda ako. 34 Koma tsopano wathyokera mʼnyanja,pansi penipeni pa nyanja.Katundu wako ndi onse amene anali naweamira pamodzi nawe. 35 Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanjaaopsedwa ndi zimene zakuchitikira.Mafumu awo akuchita manthandipo nkhope zangoti khululu. 36 Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola.Watha mochititsa manthandipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.”

In Other Versions

Ezekiel 27 in the ANGEFD

Ezekiel 27 in the ANTPNG2D

Ezekiel 27 in the AS21

Ezekiel 27 in the BAGH

Ezekiel 27 in the BBPNG

Ezekiel 27 in the BBT1E

Ezekiel 27 in the BDS

Ezekiel 27 in the BEV

Ezekiel 27 in the BHAD

Ezekiel 27 in the BIB

Ezekiel 27 in the BLPT

Ezekiel 27 in the BNT

Ezekiel 27 in the BNTABOOT

Ezekiel 27 in the BNTLV

Ezekiel 27 in the BOATCB

Ezekiel 27 in the BOATCB2

Ezekiel 27 in the BOBCV

Ezekiel 27 in the BOCNT

Ezekiel 27 in the BOECS

Ezekiel 27 in the BOHCB

Ezekiel 27 in the BOHCV

Ezekiel 27 in the BOHLNT

Ezekiel 27 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 27 in the BOICB

Ezekiel 27 in the BOILNTAP

Ezekiel 27 in the BOITCV

Ezekiel 27 in the BOKCV

Ezekiel 27 in the BOKCV2

Ezekiel 27 in the BOKHWOG

Ezekiel 27 in the BOKSSV

Ezekiel 27 in the BOLCB

Ezekiel 27 in the BOLCB2

Ezekiel 27 in the BOMCV

Ezekiel 27 in the BONAV

Ezekiel 27 in the BONCB

Ezekiel 27 in the BONLT

Ezekiel 27 in the BONUT2

Ezekiel 27 in the BOPLNT

Ezekiel 27 in the BOSCB

Ezekiel 27 in the BOSNC

Ezekiel 27 in the BOTLNT

Ezekiel 27 in the BOVCB

Ezekiel 27 in the BOYCB

Ezekiel 27 in the BPBB

Ezekiel 27 in the BPH

Ezekiel 27 in the BSB

Ezekiel 27 in the CCB

Ezekiel 27 in the CUV

Ezekiel 27 in the CUVS

Ezekiel 27 in the DBT

Ezekiel 27 in the DGDNT

Ezekiel 27 in the DHNT

Ezekiel 27 in the DNT

Ezekiel 27 in the ELBE

Ezekiel 27 in the EMTV

Ezekiel 27 in the ESV

Ezekiel 27 in the FBV

Ezekiel 27 in the FEB

Ezekiel 27 in the GGMNT

Ezekiel 27 in the GNT

Ezekiel 27 in the HARY

Ezekiel 27 in the HNT

Ezekiel 27 in the IRVA

Ezekiel 27 in the IRVB

Ezekiel 27 in the IRVG

Ezekiel 27 in the IRVH

Ezekiel 27 in the IRVK

Ezekiel 27 in the IRVM

Ezekiel 27 in the IRVM2

Ezekiel 27 in the IRVO

Ezekiel 27 in the IRVP

Ezekiel 27 in the IRVT

Ezekiel 27 in the IRVT2

Ezekiel 27 in the IRVU

Ezekiel 27 in the ISVN

Ezekiel 27 in the JSNT

Ezekiel 27 in the KAPI

Ezekiel 27 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 27 in the KBV

Ezekiel 27 in the KJV

Ezekiel 27 in the KNFD

Ezekiel 27 in the LBA

Ezekiel 27 in the LBLA

Ezekiel 27 in the LNT

Ezekiel 27 in the LSV

Ezekiel 27 in the MAAL

Ezekiel 27 in the MBV

Ezekiel 27 in the MBV2

Ezekiel 27 in the MHNT

Ezekiel 27 in the MKNFD

Ezekiel 27 in the MNG

Ezekiel 27 in the MNT

Ezekiel 27 in the MNT2

Ezekiel 27 in the MRS1T

Ezekiel 27 in the NAA

Ezekiel 27 in the NASB

Ezekiel 27 in the NBLA

Ezekiel 27 in the NBS

Ezekiel 27 in the NBVTP

Ezekiel 27 in the NET2

Ezekiel 27 in the NIV11

Ezekiel 27 in the NNT

Ezekiel 27 in the NNT2

Ezekiel 27 in the NNT3

Ezekiel 27 in the PDDPT

Ezekiel 27 in the PFNT

Ezekiel 27 in the RMNT

Ezekiel 27 in the SBIAS

Ezekiel 27 in the SBIBS

Ezekiel 27 in the SBIBS2

Ezekiel 27 in the SBICS

Ezekiel 27 in the SBIDS

Ezekiel 27 in the SBIGS

Ezekiel 27 in the SBIHS

Ezekiel 27 in the SBIIS

Ezekiel 27 in the SBIIS2

Ezekiel 27 in the SBIIS3

Ezekiel 27 in the SBIKS

Ezekiel 27 in the SBIKS2

Ezekiel 27 in the SBIMS

Ezekiel 27 in the SBIOS

Ezekiel 27 in the SBIPS

Ezekiel 27 in the SBISS

Ezekiel 27 in the SBITS

Ezekiel 27 in the SBITS2

Ezekiel 27 in the SBITS3

Ezekiel 27 in the SBITS4

Ezekiel 27 in the SBIUS

Ezekiel 27 in the SBIVS

Ezekiel 27 in the SBT

Ezekiel 27 in the SBT1E

Ezekiel 27 in the SCHL

Ezekiel 27 in the SNT

Ezekiel 27 in the SUSU

Ezekiel 27 in the SUSU2

Ezekiel 27 in the SYNO

Ezekiel 27 in the TBIAOTANT

Ezekiel 27 in the TBT1E

Ezekiel 27 in the TBT1E2

Ezekiel 27 in the TFTIP

Ezekiel 27 in the TFTU

Ezekiel 27 in the TGNTATF3T

Ezekiel 27 in the THAI

Ezekiel 27 in the TNFD

Ezekiel 27 in the TNT

Ezekiel 27 in the TNTIK

Ezekiel 27 in the TNTIL

Ezekiel 27 in the TNTIN

Ezekiel 27 in the TNTIP

Ezekiel 27 in the TNTIZ

Ezekiel 27 in the TOMA

Ezekiel 27 in the TTENT

Ezekiel 27 in the UBG

Ezekiel 27 in the UGV

Ezekiel 27 in the UGV2

Ezekiel 27 in the UGV3

Ezekiel 27 in the VBL

Ezekiel 27 in the VDCC

Ezekiel 27 in the YALU

Ezekiel 27 in the YAPE

Ezekiel 27 in the YBVTP

Ezekiel 27 in the ZBP