Ezekiel 7 (BOGWICC)
1 Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti:“Chimaliziro! Chimaliziro chafikaku ngodya zinayi za dziko. 3 Chimaliziro chili pa iwe tsopano.Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe.Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe akondi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako. 4 Ine sindidzakumvera chisonikapena kukuleka.Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipakomanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako.Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.” 5 “Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi:“Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo!Taona chikubwera! 6 Chimaliziro chafika!Chimaliziro chafika!Chiwonongeko chakugwera.Taona chafika! 7 Inu anthu okhala mʼdziko,chiwonongeko chakugwerani.Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri. 8 Ine ndili pafupi kukukwiyirani,ndipo ukali wanga udzathera pa iwe;Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe akondiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa. 9 Ine sindidzakumvera chisonikapena kukuleka.Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zakondiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’ 10 “Taona, tsikulo!Taona, lafika!Chiwonongeko chako chabwera.Ndodo yaphuka mphundu za maluwa.Kudzitama kwaphuka. 11 Chiwawa chasanduka ndodoyowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo.Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale.Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo.Palibiretu ndipo sipadzapezekamunthu wowalira maliro. 12 Nthawi yafika!Tsiku layandikira!Munthu wogula asakondwerendipo wogulitsa asamve chisoni,popeza ukali wanga uli pa gulu lonse. 13 Wogulitsa sadzazipezanso zinthuzimene anagulitsa kwa winachinkana onse awiri akanali ndi moyo,pakuti chilango chidzagwera onsewondipo sichingasinthike.Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyenseamene adzapulumutsa moyo wake. 14 “Lipenga lalira,ndipo zonse zakonzeka.Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo,pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse. 15 Ku bwalo kuli kumenyanandipo mʼkati muli mliri ndi njala.Anthu okhala ku midziadzafa ndi nkhondo.Iwo okhala ku mizindaadzafa ndi mliri ndi njala. 16 Onse amene adzapulumukandi kumakakhala ku mapiri,azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa.Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake. 17 Dzanja lililonse lidzalefuka,ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi. 18 Iwo adzavala zigudulindipo adzagwidwa ndi mantha.Adzakhala ndi nkhope zamanyazindipo mitu yawo adzameta mpala. 19 “Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewundipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa.Siliva ndi golide wawosizidzatha kuwapulumutsapa tsiku la ukali wa Yehova.Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala,kapena kukhala okhuta,pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo. 20 Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakakandipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina.Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsakukhala zowanyansa. 21 Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe.Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilandandi kudziyipitsa. 22 Ine ndidzawalekerera anthuwondipo adzayipitsa malo anga apamtima.Adzalowamo ngati mbalandi kuyipitsamo. 23 “Konzani maunyolo,chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawondipo mzinda wadzaza ndi chiwawa. 24 Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsakuti idzalande nyumba zawo.Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvupamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo. 25 Nkhawa ikadzawafikiraadzafunafuna mtendere koma osawupeza. 26 Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake,ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake.Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri.Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo,ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu. 27 Mfumu idzalira,kalonga adzagwidwa ndi mantha.Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha.Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo,ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”