Hebrews 10 (BOGWICC)
1 Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza. 2 Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo. 3 Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. 4 Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo. 5 Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,“Simunafune nsembe kapena zopereka,koma thupi munandikonzera. 6 Simunakondwere nazo nsembe zopserezandi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo. 7 Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ” 8 Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. 9 Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. 10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha. 11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa. 15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati, 16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawoatapita masiku amenewo,” akutero Yehova.“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.” 17 Ndipo akutinso:“Sindidzakumbukiranso konsemachimo awo ndi zolakwa zawo.” 18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo. 19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira. 26 Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. 27 Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu 28 Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. 29 Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? 30 Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” 31 Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo. 32 Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. 33 Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. 34 Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha. 35 Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu. 36 Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza. 37 Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi. 38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha,Ine sindidzakondwera naye. 39 Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.