Hebrews 13 (BOGWICC)
1 Pitirizani kukondana monga abale. 2 Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa. 3 Muzikumbukira amene ali mʼndende ngati kuti inunso ndi omangidwa, ndiponso amene akusautsidwa ngati inunso mukuvutika. 4 Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga. 5 Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati,“Sadzakusiyani,kapena kukutayani konse.” 6 Kotero ife tikunena molimba mtima kuti,“Ambuye ndiye mthandizi wanga;sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?” 7 Muzikumbukira atsogoleri anu, amene amakulalikirani Mawu a Mulungu. Ganizirani zamoyo wawo ndipo tsatirani chikhulupiriro chawo. 8 Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse. 9 Musasocheretsedwe ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo. Nʼkwabwino kuti mitima yathu ilimbikitsidwe ndi chisomo osati ndi chakudya, chimene sichipindulitsa iwo amene amachidya. 10 Ife tili ndi guwa lansembe, ndipo ansembe otumikira mʼtenti cha Ayuda, saloledwa kudya zochokera pamenepo. 11 Mkulu wa ansembe amatenga magazi kukapereka nsembe chifukwa cha machimo, koma nyamayo imawotchedwa kunja kwa msasa. 12 Nʼchifukwa chakenso Yesu anafera kunja kwa mzinda kuti ayeretse anthu ake kudzera mʼmagazi ake. 13 Tiyeni tsono, tipite kwa iye kunja kwa msasa, titasenza chitonzo chake. 14 Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera. 15 Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake. 16 Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere. 17 Muzimvera atsogoleri anu ndi kugonjera ulamuliro wawo, iwo amakuyangʼanirani monga anthu amene adzayenera kufotokoza za ntchito yawo pamaso pa Mulungu. Muziwamvera kuti agwire ntchito yawo ndi chimwemwe osati molemedwa pakuti izi sizingakupindulireni. 18 Mutipempherere ifenso. Pakuti tikutsimikiza kuti tili ndi chikumbumtima changwiro ndipo timafuna kuchita zinthu zonse mwaulemu. 19 Ine ndikukupemphani kuti mundipempherere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. 20 Mulungu wamtendere, amene kudzera mʼmagazi a pangano lamuyaya anaukitsa Ambuye athu Yesu kwa akufa, amene ndi Mʼbusa wamkulu, 21 akupatseni chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake ndipo Mulungu achite mwa ife, chimene chingamukomere kudzera mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ku nthawi zanthawi, Ameni. 22 Ndikukupemphani abale kuti mulandire mawu anga achilimbikitso, pakuti ndakulemberani mwachidule. 23 Ine ndikufuna kuti inu mudziwe kuti mʼbale wathu Timoteyo wamasulidwa. Ngati iye angafike msanga ndibwera naye kudzakuonani. 24 Mupereke moni kwa atsogoleri anu onse ndiponso kwa anthu onse a Mulungu. Abale ochokera ku Italiya akupereka moni. 25 Chisomo chikhale ndi inu nonse.
In Other Versions
Hebrews 13 in the ANGEFD
Hebrews 13 in the ANTPNG2D
Hebrews 13 in the AS21
Hebrews 13 in the BAGH
Hebrews 13 in the BBPNG
Hebrews 13 in the BBT1E
Hebrews 13 in the BDS
Hebrews 13 in the BEV
Hebrews 13 in the BHAD
Hebrews 13 in the BIB
Hebrews 13 in the BLPT
Hebrews 13 in the BNT
Hebrews 13 in the BNTABOOT
Hebrews 13 in the BNTLV
Hebrews 13 in the BOATCB
Hebrews 13 in the BOATCB2
Hebrews 13 in the BOBCV
Hebrews 13 in the BOCNT
Hebrews 13 in the BOECS
Hebrews 13 in the BOHCB
Hebrews 13 in the BOHCV
Hebrews 13 in the BOHLNT
Hebrews 13 in the BOHNTLTAL
Hebrews 13 in the BOICB
Hebrews 13 in the BOILNTAP
Hebrews 13 in the BOITCV
Hebrews 13 in the BOKCV
Hebrews 13 in the BOKCV2
Hebrews 13 in the BOKHWOG
Hebrews 13 in the BOKSSV
Hebrews 13 in the BOLCB
Hebrews 13 in the BOLCB2
Hebrews 13 in the BOMCV
Hebrews 13 in the BONAV
Hebrews 13 in the BONCB
Hebrews 13 in the BONLT
Hebrews 13 in the BONUT2
Hebrews 13 in the BOPLNT
Hebrews 13 in the BOSCB
Hebrews 13 in the BOSNC
Hebrews 13 in the BOTLNT
Hebrews 13 in the BOVCB
Hebrews 13 in the BOYCB
Hebrews 13 in the BPBB
Hebrews 13 in the BPH
Hebrews 13 in the BSB
Hebrews 13 in the CCB
Hebrews 13 in the CUV
Hebrews 13 in the CUVS
Hebrews 13 in the DBT
Hebrews 13 in the DGDNT
Hebrews 13 in the DHNT
Hebrews 13 in the DNT
Hebrews 13 in the ELBE
Hebrews 13 in the EMTV
Hebrews 13 in the ESV
Hebrews 13 in the FBV
Hebrews 13 in the FEB
Hebrews 13 in the GGMNT
Hebrews 13 in the GNT
Hebrews 13 in the HARY
Hebrews 13 in the HNT
Hebrews 13 in the IRVA
Hebrews 13 in the IRVB
Hebrews 13 in the IRVG
Hebrews 13 in the IRVH
Hebrews 13 in the IRVK
Hebrews 13 in the IRVM
Hebrews 13 in the IRVM2
Hebrews 13 in the IRVO
Hebrews 13 in the IRVP
Hebrews 13 in the IRVT
Hebrews 13 in the IRVT2
Hebrews 13 in the IRVU
Hebrews 13 in the ISVN
Hebrews 13 in the JSNT
Hebrews 13 in the KAPI
Hebrews 13 in the KBT1ETNIK
Hebrews 13 in the KBV
Hebrews 13 in the KJV
Hebrews 13 in the KNFD
Hebrews 13 in the LBA
Hebrews 13 in the LBLA
Hebrews 13 in the LNT
Hebrews 13 in the LSV
Hebrews 13 in the MAAL
Hebrews 13 in the MBV
Hebrews 13 in the MBV2
Hebrews 13 in the MHNT
Hebrews 13 in the MKNFD
Hebrews 13 in the MNG
Hebrews 13 in the MNT
Hebrews 13 in the MNT2
Hebrews 13 in the MRS1T
Hebrews 13 in the NAA
Hebrews 13 in the NASB
Hebrews 13 in the NBLA
Hebrews 13 in the NBS
Hebrews 13 in the NBVTP
Hebrews 13 in the NET2
Hebrews 13 in the NIV11
Hebrews 13 in the NNT
Hebrews 13 in the NNT2
Hebrews 13 in the NNT3
Hebrews 13 in the PDDPT
Hebrews 13 in the PFNT
Hebrews 13 in the RMNT
Hebrews 13 in the SBIAS
Hebrews 13 in the SBIBS
Hebrews 13 in the SBIBS2
Hebrews 13 in the SBICS
Hebrews 13 in the SBIDS
Hebrews 13 in the SBIGS
Hebrews 13 in the SBIHS
Hebrews 13 in the SBIIS
Hebrews 13 in the SBIIS2
Hebrews 13 in the SBIIS3
Hebrews 13 in the SBIKS
Hebrews 13 in the SBIKS2
Hebrews 13 in the SBIMS
Hebrews 13 in the SBIOS
Hebrews 13 in the SBIPS
Hebrews 13 in the SBISS
Hebrews 13 in the SBITS
Hebrews 13 in the SBITS2
Hebrews 13 in the SBITS3
Hebrews 13 in the SBITS4
Hebrews 13 in the SBIUS
Hebrews 13 in the SBIVS
Hebrews 13 in the SBT
Hebrews 13 in the SBT1E
Hebrews 13 in the SCHL
Hebrews 13 in the SNT
Hebrews 13 in the SUSU
Hebrews 13 in the SUSU2
Hebrews 13 in the SYNO
Hebrews 13 in the TBIAOTANT
Hebrews 13 in the TBT1E
Hebrews 13 in the TBT1E2
Hebrews 13 in the TFTIP
Hebrews 13 in the TFTU
Hebrews 13 in the TGNTATF3T
Hebrews 13 in the THAI
Hebrews 13 in the TNFD
Hebrews 13 in the TNT
Hebrews 13 in the TNTIK
Hebrews 13 in the TNTIL
Hebrews 13 in the TNTIN
Hebrews 13 in the TNTIP
Hebrews 13 in the TNTIZ
Hebrews 13 in the TOMA
Hebrews 13 in the TTENT
Hebrews 13 in the UBG
Hebrews 13 in the UGV
Hebrews 13 in the UGV2
Hebrews 13 in the UGV3
Hebrews 13 in the VBL
Hebrews 13 in the VDCC
Hebrews 13 in the YALU
Hebrews 13 in the YAPE
Hebrews 13 in the YBVTP
Hebrews 13 in the ZBP