Isaiah 29 (BOGWICC)

1 Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli,mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo!Papite chaka chimodzi kapena ziwirindipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu. 2 Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arielindipo kudzakhala kulira ndi kudandaula,mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe. 3 Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo;ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondondi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe. 4 Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka,mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi,adzamveka ngati a mzukwa.Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi. 5 Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti.Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo.Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka, 6 Yehova Wamphamvuzonse adzabwerandi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu,kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa. 7 Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arielinʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga,chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto,gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku. 8 Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya,koma podzuka ali nayobe njala;kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa,koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa.Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonsechikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni. 9 Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa.Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya,ledzerani, koma osati ndi vinyo,dzandirani, koma osati ndi mowa. 10 Yehova wakugonetsani tulo tofa nato.Watseka maso anu, inu aneneri;waphimba mitu yanu, inu alosi. 11 Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.” 12 Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.” 13 Ambuye akuti,“Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa. 14 Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirirakuwachitira ntchito zodabwitsa;nzeru za anthu anzeru zidzatha,luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.” 15 Tsoka kwa amene amayesetsakubisira Yehova maganizo awo,amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti,“Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?” 16 Inu mumazondotsa zinthungati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya.Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti“Sunandipange ndi iwe?”Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti,“Iwe sudziwa chilichonse?” 17 Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde,ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango? 18 Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku,ndipo anthu osaona ameneankakhala mu mdima adzapenya. 19 Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova;ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli. 20 Koma anthu ankhanza adzazimirira,oseka anzawo sadzaonekanso,ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa. 21 Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa,kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandundi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo. 22 Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti,“Anthu anga sadzachitanso manyazi;nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi. 23 Akadzaona ana awo ndintchito ya manja anga pakati pawo,adzatamanda dzina langa loyera;adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo,ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli. 24 Anthu opusa adzapeza nzeru;onyinyirika adzalandira malangizo.”

In Other Versions

Isaiah 29 in the ANGEFD

Isaiah 29 in the ANTPNG2D

Isaiah 29 in the AS21

Isaiah 29 in the BAGH

Isaiah 29 in the BBPNG

Isaiah 29 in the BBT1E

Isaiah 29 in the BDS

Isaiah 29 in the BEV

Isaiah 29 in the BHAD

Isaiah 29 in the BIB

Isaiah 29 in the BLPT

Isaiah 29 in the BNT

Isaiah 29 in the BNTABOOT

Isaiah 29 in the BNTLV

Isaiah 29 in the BOATCB

Isaiah 29 in the BOATCB2

Isaiah 29 in the BOBCV

Isaiah 29 in the BOCNT

Isaiah 29 in the BOECS

Isaiah 29 in the BOHCB

Isaiah 29 in the BOHCV

Isaiah 29 in the BOHLNT

Isaiah 29 in the BOHNTLTAL

Isaiah 29 in the BOICB

Isaiah 29 in the BOILNTAP

Isaiah 29 in the BOITCV

Isaiah 29 in the BOKCV

Isaiah 29 in the BOKCV2

Isaiah 29 in the BOKHWOG

Isaiah 29 in the BOKSSV

Isaiah 29 in the BOLCB

Isaiah 29 in the BOLCB2

Isaiah 29 in the BOMCV

Isaiah 29 in the BONAV

Isaiah 29 in the BONCB

Isaiah 29 in the BONLT

Isaiah 29 in the BONUT2

Isaiah 29 in the BOPLNT

Isaiah 29 in the BOSCB

Isaiah 29 in the BOSNC

Isaiah 29 in the BOTLNT

Isaiah 29 in the BOVCB

Isaiah 29 in the BOYCB

Isaiah 29 in the BPBB

Isaiah 29 in the BPH

Isaiah 29 in the BSB

Isaiah 29 in the CCB

Isaiah 29 in the CUV

Isaiah 29 in the CUVS

Isaiah 29 in the DBT

Isaiah 29 in the DGDNT

Isaiah 29 in the DHNT

Isaiah 29 in the DNT

Isaiah 29 in the ELBE

Isaiah 29 in the EMTV

Isaiah 29 in the ESV

Isaiah 29 in the FBV

Isaiah 29 in the FEB

Isaiah 29 in the GGMNT

Isaiah 29 in the GNT

Isaiah 29 in the HARY

Isaiah 29 in the HNT

Isaiah 29 in the IRVA

Isaiah 29 in the IRVB

Isaiah 29 in the IRVG

Isaiah 29 in the IRVH

Isaiah 29 in the IRVK

Isaiah 29 in the IRVM

Isaiah 29 in the IRVM2

Isaiah 29 in the IRVO

Isaiah 29 in the IRVP

Isaiah 29 in the IRVT

Isaiah 29 in the IRVT2

Isaiah 29 in the IRVU

Isaiah 29 in the ISVN

Isaiah 29 in the JSNT

Isaiah 29 in the KAPI

Isaiah 29 in the KBT1ETNIK

Isaiah 29 in the KBV

Isaiah 29 in the KJV

Isaiah 29 in the KNFD

Isaiah 29 in the LBA

Isaiah 29 in the LBLA

Isaiah 29 in the LNT

Isaiah 29 in the LSV

Isaiah 29 in the MAAL

Isaiah 29 in the MBV

Isaiah 29 in the MBV2

Isaiah 29 in the MHNT

Isaiah 29 in the MKNFD

Isaiah 29 in the MNG

Isaiah 29 in the MNT

Isaiah 29 in the MNT2

Isaiah 29 in the MRS1T

Isaiah 29 in the NAA

Isaiah 29 in the NASB

Isaiah 29 in the NBLA

Isaiah 29 in the NBS

Isaiah 29 in the NBVTP

Isaiah 29 in the NET2

Isaiah 29 in the NIV11

Isaiah 29 in the NNT

Isaiah 29 in the NNT2

Isaiah 29 in the NNT3

Isaiah 29 in the PDDPT

Isaiah 29 in the PFNT

Isaiah 29 in the RMNT

Isaiah 29 in the SBIAS

Isaiah 29 in the SBIBS

Isaiah 29 in the SBIBS2

Isaiah 29 in the SBICS

Isaiah 29 in the SBIDS

Isaiah 29 in the SBIGS

Isaiah 29 in the SBIHS

Isaiah 29 in the SBIIS

Isaiah 29 in the SBIIS2

Isaiah 29 in the SBIIS3

Isaiah 29 in the SBIKS

Isaiah 29 in the SBIKS2

Isaiah 29 in the SBIMS

Isaiah 29 in the SBIOS

Isaiah 29 in the SBIPS

Isaiah 29 in the SBISS

Isaiah 29 in the SBITS

Isaiah 29 in the SBITS2

Isaiah 29 in the SBITS3

Isaiah 29 in the SBITS4

Isaiah 29 in the SBIUS

Isaiah 29 in the SBIVS

Isaiah 29 in the SBT

Isaiah 29 in the SBT1E

Isaiah 29 in the SCHL

Isaiah 29 in the SNT

Isaiah 29 in the SUSU

Isaiah 29 in the SUSU2

Isaiah 29 in the SYNO

Isaiah 29 in the TBIAOTANT

Isaiah 29 in the TBT1E

Isaiah 29 in the TBT1E2

Isaiah 29 in the TFTIP

Isaiah 29 in the TFTU

Isaiah 29 in the TGNTATF3T

Isaiah 29 in the THAI

Isaiah 29 in the TNFD

Isaiah 29 in the TNT

Isaiah 29 in the TNTIK

Isaiah 29 in the TNTIL

Isaiah 29 in the TNTIN

Isaiah 29 in the TNTIP

Isaiah 29 in the TNTIZ

Isaiah 29 in the TOMA

Isaiah 29 in the TTENT

Isaiah 29 in the UBG

Isaiah 29 in the UGV

Isaiah 29 in the UGV2

Isaiah 29 in the UGV3

Isaiah 29 in the VBL

Isaiah 29 in the VDCC

Isaiah 29 in the YALU

Isaiah 29 in the YAPE

Isaiah 29 in the YBVTP

Isaiah 29 in the ZBP