Isaiah 54 (BOGWICC)

1 “Sangalala, iwe mayi wosabala,iwe amene sunabalepo mwana;imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe,iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambirikuposa mkazi wokwatiwa,”akutero Yehova. 2 Kulitsa malo omangapo tenti yako,tambasula kwambiri nsalu zake,usaleke;talikitsa zingwe zako,limbitsa zikhomo zako. 3 Pakuti udzasendeza malire ako kumanja ndi kumanzere;ndipo zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu inandipo zidzakhala mʼmizinda yawo yosiyidwa. 4 “Usachite mantha; sadzakunyozanso.Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso.Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wakondipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso. 5 Pakuti Mlengi wako ali ngati mwamuna wako,dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wanu;dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi. 6 Yehova wakuyitananso,uli ngati mkazi wosiyidwa ndi wodzaza ndi chisoni mu mtima,mkazi amene anakwatiwa pa unyamata wake kenaka nʼkukanidwa,”akutero Mulungu wako. 7 “Kwa kanthawi kochepa, Ine ndinakusiya,koma ndidzakutenganso chifukwa ndimakukonda kwambiri. 8 Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepandili wokwiya kwambiri.Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya,ndidzakuchitira chifundo,”akutero Yehova Mpulumutsi wako. 9 “Kwa ine zimenezi zili ngati mmene zinalili mʼnthawi ya Nowa.Monga ndinalumbira nthawi imeneyo kuti sindidzawononganso dziko lapansi ndi madzi.Kotero tsopano ndalumbira kuti sindidzakupseraninso mtima,sindidzakudzudzulaninso. 10 Ngakhale mapiri atagwedezekandi zitunda kusunthidwa,koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha.Pangano langa lamtendere silidzasintha,”akutero Yehova amene amakuchitira chifundo. 11 “Iwe mzinda wozunzika, wokunthidwa ndi namondwe ndiponso wopanda wokutonthoza,Ine ndidzakongoletsa miyala yako.Maziko ako ndidzamanga ndi miyala ya safiro. 12 Ndidzamanga nsanja zako zankhondo ndi miyala yokongola ya rubi.Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yonyezimira ngati moto,ndipo linga lako lonse lidzakhala la miyala yamtengowapatali. 13 Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka. 14 Udzakhazikika mʼchilungamo chenicheni:Sudzakhalanso wopanikizika,chifukwa sudzaopa kanthu kalikonse.Sudzakhalanso ndi manthachifukwa manthawo sadzafika pafupi ndi iwe. 15 Ngati wina adzakuthirani nkhondo, si ndine amene ndachititsa;aliyense amene adzalimbana nanu adzagonja chifukwa cha iwe. 16 “Taona, ndi Ine amene ndinalenga munthu wosula zitsuloamene amakoleza moto wamakalandi kusula zida zoti azigwiritse ntchito.Ndipo ndine amene ndinalenga munthu wosakaza kuti awononge; 17 palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke,ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa.Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova.Chipambano chawo chichokera kwa Ine,”akutero Yehova.

In Other Versions

Isaiah 54 in the ANGEFD

Isaiah 54 in the ANTPNG2D

Isaiah 54 in the AS21

Isaiah 54 in the BAGH

Isaiah 54 in the BBPNG

Isaiah 54 in the BBT1E

Isaiah 54 in the BDS

Isaiah 54 in the BEV

Isaiah 54 in the BHAD

Isaiah 54 in the BIB

Isaiah 54 in the BLPT

Isaiah 54 in the BNT

Isaiah 54 in the BNTABOOT

Isaiah 54 in the BNTLV

Isaiah 54 in the BOATCB

Isaiah 54 in the BOATCB2

Isaiah 54 in the BOBCV

Isaiah 54 in the BOCNT

Isaiah 54 in the BOECS

Isaiah 54 in the BOHCB

Isaiah 54 in the BOHCV

Isaiah 54 in the BOHLNT

Isaiah 54 in the BOHNTLTAL

Isaiah 54 in the BOICB

Isaiah 54 in the BOILNTAP

Isaiah 54 in the BOITCV

Isaiah 54 in the BOKCV

Isaiah 54 in the BOKCV2

Isaiah 54 in the BOKHWOG

Isaiah 54 in the BOKSSV

Isaiah 54 in the BOLCB

Isaiah 54 in the BOLCB2

Isaiah 54 in the BOMCV

Isaiah 54 in the BONAV

Isaiah 54 in the BONCB

Isaiah 54 in the BONLT

Isaiah 54 in the BONUT2

Isaiah 54 in the BOPLNT

Isaiah 54 in the BOSCB

Isaiah 54 in the BOSNC

Isaiah 54 in the BOTLNT

Isaiah 54 in the BOVCB

Isaiah 54 in the BOYCB

Isaiah 54 in the BPBB

Isaiah 54 in the BPH

Isaiah 54 in the BSB

Isaiah 54 in the CCB

Isaiah 54 in the CUV

Isaiah 54 in the CUVS

Isaiah 54 in the DBT

Isaiah 54 in the DGDNT

Isaiah 54 in the DHNT

Isaiah 54 in the DNT

Isaiah 54 in the ELBE

Isaiah 54 in the EMTV

Isaiah 54 in the ESV

Isaiah 54 in the FBV

Isaiah 54 in the FEB

Isaiah 54 in the GGMNT

Isaiah 54 in the GNT

Isaiah 54 in the HARY

Isaiah 54 in the HNT

Isaiah 54 in the IRVA

Isaiah 54 in the IRVB

Isaiah 54 in the IRVG

Isaiah 54 in the IRVH

Isaiah 54 in the IRVK

Isaiah 54 in the IRVM

Isaiah 54 in the IRVM2

Isaiah 54 in the IRVO

Isaiah 54 in the IRVP

Isaiah 54 in the IRVT

Isaiah 54 in the IRVT2

Isaiah 54 in the IRVU

Isaiah 54 in the ISVN

Isaiah 54 in the JSNT

Isaiah 54 in the KAPI

Isaiah 54 in the KBT1ETNIK

Isaiah 54 in the KBV

Isaiah 54 in the KJV

Isaiah 54 in the KNFD

Isaiah 54 in the LBA

Isaiah 54 in the LBLA

Isaiah 54 in the LNT

Isaiah 54 in the LSV

Isaiah 54 in the MAAL

Isaiah 54 in the MBV

Isaiah 54 in the MBV2

Isaiah 54 in the MHNT

Isaiah 54 in the MKNFD

Isaiah 54 in the MNG

Isaiah 54 in the MNT

Isaiah 54 in the MNT2

Isaiah 54 in the MRS1T

Isaiah 54 in the NAA

Isaiah 54 in the NASB

Isaiah 54 in the NBLA

Isaiah 54 in the NBS

Isaiah 54 in the NBVTP

Isaiah 54 in the NET2

Isaiah 54 in the NIV11

Isaiah 54 in the NNT

Isaiah 54 in the NNT2

Isaiah 54 in the NNT3

Isaiah 54 in the PDDPT

Isaiah 54 in the PFNT

Isaiah 54 in the RMNT

Isaiah 54 in the SBIAS

Isaiah 54 in the SBIBS

Isaiah 54 in the SBIBS2

Isaiah 54 in the SBICS

Isaiah 54 in the SBIDS

Isaiah 54 in the SBIGS

Isaiah 54 in the SBIHS

Isaiah 54 in the SBIIS

Isaiah 54 in the SBIIS2

Isaiah 54 in the SBIIS3

Isaiah 54 in the SBIKS

Isaiah 54 in the SBIKS2

Isaiah 54 in the SBIMS

Isaiah 54 in the SBIOS

Isaiah 54 in the SBIPS

Isaiah 54 in the SBISS

Isaiah 54 in the SBITS

Isaiah 54 in the SBITS2

Isaiah 54 in the SBITS3

Isaiah 54 in the SBITS4

Isaiah 54 in the SBIUS

Isaiah 54 in the SBIVS

Isaiah 54 in the SBT

Isaiah 54 in the SBT1E

Isaiah 54 in the SCHL

Isaiah 54 in the SNT

Isaiah 54 in the SUSU

Isaiah 54 in the SUSU2

Isaiah 54 in the SYNO

Isaiah 54 in the TBIAOTANT

Isaiah 54 in the TBT1E

Isaiah 54 in the TBT1E2

Isaiah 54 in the TFTIP

Isaiah 54 in the TFTU

Isaiah 54 in the TGNTATF3T

Isaiah 54 in the THAI

Isaiah 54 in the TNFD

Isaiah 54 in the TNT

Isaiah 54 in the TNTIK

Isaiah 54 in the TNTIL

Isaiah 54 in the TNTIN

Isaiah 54 in the TNTIP

Isaiah 54 in the TNTIZ

Isaiah 54 in the TOMA

Isaiah 54 in the TTENT

Isaiah 54 in the UBG

Isaiah 54 in the UGV

Isaiah 54 in the UGV2

Isaiah 54 in the UGV3

Isaiah 54 in the VBL

Isaiah 54 in the VDCC

Isaiah 54 in the YALU

Isaiah 54 in the YAPE

Isaiah 54 in the YBVTP

Isaiah 54 in the ZBP