Isaiah 59 (BOGWICC)
1 Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa,kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve. 2 Koma zoyipa zanu zakulekanitsanindi Mulungu wanu;ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu,kotero Iye sadzamva. 3 Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi.Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu.Pakamwa panu payankhula zabodza,ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa. 4 Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama,palibe amene akupita ku mlandu moona mtima.Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza;amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa. 5 Iwo amayikira mazira a mambandipo amaluka ukonde wakangawude.Aliyense amene adzadya mazira awo adzafa,ndipo ngati dzira limodzi lasweka limatulutsa mphiri. 6 Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala;ndipo chimene apangacho sangachifunde.Ntchito zawo ndi zoyipa,ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo. 7 Amathamangira kukachita zoyipa;sachedwa kupha anthu osalakwa.Maganizo awo ndi maganizo oyipa;kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko. 8 Iwo sadziwa kuchita za mtendere;zonse zimene amachita nʼzopanda chilungamo.Njira zawo zonse nʼzokhotakhota;aliyense oyenda mʼnjira zimenezo sadzapeza mtendere. 9 Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira;ndipo chipulumutso sichitifikira.Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha;tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani. 10 Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona,kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso.Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku;timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa. 11 Tonse timabangula ngati zimbalangondo:Timalira modandaula ngati nkhunda.Tinayembekezera kuweruza kolungama; koma sitikupeza.Timayembekezera chipulumutso koma chimakhala nafe kutali.” 12 Pakuti zolakwa zathu nʼzochuluka pamaso panu,ndipo machimo athu akutsutsana nafe.Zolakwa zathu zili ndi ife nthawi zonsendipo tikuvomereza machimo athu: 13 Tawukira ndi kumukana Yehova.Tafulatira Mulungu wathu,pa kupondereza anzathu ndi kupandukira Yehova,ndi pa kuyankhula mabodza amene tawaganiza mʼmitima mwathu. 14 Motero kuweruza kolungama kwalekekandipo choonadi chili kutali ndi ife;kukhulupirika sikukupezekanso mʼmabwalo a milandu,ndipo kuona mtima sikukupezekanso mʼmenemo. 15 Choonadi sichikupezeka kumeneko,ndipo wina akakana kuchita nawo zoyipa amapeza mavuto. Yehova anaziona zimenezi ndipo zinamunyansakuti panalibe chiweruzo cholungama. 16 Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe,Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera;Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza,ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake; 17 Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa,ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso;anavala kulipsira ngati chovalandipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda. 18 Iye adzawabwezera chilango adani a anthu akemolingana ndi zimene anachita,adzaonetsa ukali kwa adani akendi kubwezera chilango odana naye.Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali. 19 Choncho akadzabwera ngati madzioyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho.Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawaadzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake. 20 “Mpulumutsi adzabwera ku Ziyonikudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,”akutero Yehova. 21 Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,”akutero Yehova.
In Other Versions
Isaiah 59 in the ANGEFD
Isaiah 59 in the ANTPNG2D
Isaiah 59 in the AS21
Isaiah 59 in the BAGH
Isaiah 59 in the BBPNG
Isaiah 59 in the BBT1E
Isaiah 59 in the BDS
Isaiah 59 in the BEV
Isaiah 59 in the BHAD
Isaiah 59 in the BIB
Isaiah 59 in the BLPT
Isaiah 59 in the BNT
Isaiah 59 in the BNTABOOT
Isaiah 59 in the BNTLV
Isaiah 59 in the BOATCB
Isaiah 59 in the BOATCB2
Isaiah 59 in the BOBCV
Isaiah 59 in the BOCNT
Isaiah 59 in the BOECS
Isaiah 59 in the BOHCB
Isaiah 59 in the BOHCV
Isaiah 59 in the BOHLNT
Isaiah 59 in the BOHNTLTAL
Isaiah 59 in the BOICB
Isaiah 59 in the BOILNTAP
Isaiah 59 in the BOITCV
Isaiah 59 in the BOKCV
Isaiah 59 in the BOKCV2
Isaiah 59 in the BOKHWOG
Isaiah 59 in the BOKSSV
Isaiah 59 in the BOLCB
Isaiah 59 in the BOLCB2
Isaiah 59 in the BOMCV
Isaiah 59 in the BONAV
Isaiah 59 in the BONCB
Isaiah 59 in the BONLT
Isaiah 59 in the BONUT2
Isaiah 59 in the BOPLNT
Isaiah 59 in the BOSCB
Isaiah 59 in the BOSNC
Isaiah 59 in the BOTLNT
Isaiah 59 in the BOVCB
Isaiah 59 in the BOYCB
Isaiah 59 in the BPBB
Isaiah 59 in the BPH
Isaiah 59 in the BSB
Isaiah 59 in the CCB
Isaiah 59 in the CUV
Isaiah 59 in the CUVS
Isaiah 59 in the DBT
Isaiah 59 in the DGDNT
Isaiah 59 in the DHNT
Isaiah 59 in the DNT
Isaiah 59 in the ELBE
Isaiah 59 in the EMTV
Isaiah 59 in the ESV
Isaiah 59 in the FBV
Isaiah 59 in the FEB
Isaiah 59 in the GGMNT
Isaiah 59 in the GNT
Isaiah 59 in the HARY
Isaiah 59 in the HNT
Isaiah 59 in the IRVA
Isaiah 59 in the IRVB
Isaiah 59 in the IRVG
Isaiah 59 in the IRVH
Isaiah 59 in the IRVK
Isaiah 59 in the IRVM
Isaiah 59 in the IRVM2
Isaiah 59 in the IRVO
Isaiah 59 in the IRVP
Isaiah 59 in the IRVT
Isaiah 59 in the IRVT2
Isaiah 59 in the IRVU
Isaiah 59 in the ISVN
Isaiah 59 in the JSNT
Isaiah 59 in the KAPI
Isaiah 59 in the KBT1ETNIK
Isaiah 59 in the KBV
Isaiah 59 in the KJV
Isaiah 59 in the KNFD
Isaiah 59 in the LBA
Isaiah 59 in the LBLA
Isaiah 59 in the LNT
Isaiah 59 in the LSV
Isaiah 59 in the MAAL
Isaiah 59 in the MBV
Isaiah 59 in the MBV2
Isaiah 59 in the MHNT
Isaiah 59 in the MKNFD
Isaiah 59 in the MNG
Isaiah 59 in the MNT
Isaiah 59 in the MNT2
Isaiah 59 in the MRS1T
Isaiah 59 in the NAA
Isaiah 59 in the NASB
Isaiah 59 in the NBLA
Isaiah 59 in the NBS
Isaiah 59 in the NBVTP
Isaiah 59 in the NET2
Isaiah 59 in the NIV11
Isaiah 59 in the NNT
Isaiah 59 in the NNT2
Isaiah 59 in the NNT3
Isaiah 59 in the PDDPT
Isaiah 59 in the PFNT
Isaiah 59 in the RMNT
Isaiah 59 in the SBIAS
Isaiah 59 in the SBIBS
Isaiah 59 in the SBIBS2
Isaiah 59 in the SBICS
Isaiah 59 in the SBIDS
Isaiah 59 in the SBIGS
Isaiah 59 in the SBIHS
Isaiah 59 in the SBIIS
Isaiah 59 in the SBIIS2
Isaiah 59 in the SBIIS3
Isaiah 59 in the SBIKS
Isaiah 59 in the SBIKS2
Isaiah 59 in the SBIMS
Isaiah 59 in the SBIOS
Isaiah 59 in the SBIPS
Isaiah 59 in the SBISS
Isaiah 59 in the SBITS
Isaiah 59 in the SBITS2
Isaiah 59 in the SBITS3
Isaiah 59 in the SBITS4
Isaiah 59 in the SBIUS
Isaiah 59 in the SBIVS
Isaiah 59 in the SBT
Isaiah 59 in the SBT1E
Isaiah 59 in the SCHL
Isaiah 59 in the SNT
Isaiah 59 in the SUSU
Isaiah 59 in the SUSU2
Isaiah 59 in the SYNO
Isaiah 59 in the TBIAOTANT
Isaiah 59 in the TBT1E
Isaiah 59 in the TBT1E2
Isaiah 59 in the TFTIP
Isaiah 59 in the TFTU
Isaiah 59 in the TGNTATF3T
Isaiah 59 in the THAI
Isaiah 59 in the TNFD
Isaiah 59 in the TNT
Isaiah 59 in the TNTIK
Isaiah 59 in the TNTIL
Isaiah 59 in the TNTIN
Isaiah 59 in the TNTIP
Isaiah 59 in the TNTIZ
Isaiah 59 in the TOMA
Isaiah 59 in the TTENT
Isaiah 59 in the UBG
Isaiah 59 in the UGV
Isaiah 59 in the UGV2
Isaiah 59 in the UGV3
Isaiah 59 in the VBL
Isaiah 59 in the VDCC
Isaiah 59 in the YALU
Isaiah 59 in the YAPE
Isaiah 59 in the YBVTP
Isaiah 59 in the ZBP