Isaiah 63 (BOGWICC)
1 Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu,atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira?Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola,akuyenda mwa mphamvu zake? “Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamondiponso wamphamvu zopulumutsa.” 2 Nanga bwanji zovala zanu zili psuu,ngati za munthu wofinya mphesa? 3 “Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa,palibe ndi mmodzi yemwe anali nane.Ndinawapondereza ndili wokwiyandipo ndinawapondereza ndili ndi ukali;magazi awo anadothera pa zovala zanga,ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira. 4 Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga;ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika. 5 Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza.Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza;choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga,ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa. 6 Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya;ndipo ndinawasakazandipo ndinathira magazi awo pansi.” 7 Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova,ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa.Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira.Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwakeYehova wachitira nyumba ya Israelizinthu zabwino zambiri. 8 Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga,ana anga amene sadzandinyenga Ine.”Choncho anawapulumutsa. 9 Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse,ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa.Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa,anawanyamula ndikuwatengakuyambira kale lomwe. 10 Komabe iwo anawukirandi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera.Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawondipo Iye mwini anamenyana nawo. 11 Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana,masiku a Mose mtumiki wake;ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja,pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo?Ali kuti Iye amene anayikaMzimu Woyera pakati pawo? 12 Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsandi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose?Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona,kuti dzina lake limveke mpaka muyaya, 13 amene anawayendetsa pa nyanja yozama?Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu,iwo sanapunthwe; 14 Mzimu Woyera unawapumulitsangati mmene ngʼombe zimapumulira.Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anukuti dzina lanu lilemekezeke.” 15 Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka,wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife.Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti?Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu. 16 Koma Inu ndinu Atate athu,ngakhale Abrahamu satidziwakapena Israeli kutivomereza ife;Inu Yehova, ndinu Atate athu,kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu. 17 Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu?Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso?Bwererani chifukwa cha atumiki anu;mafuko a anthu amene ali cholowa chanu. 18 Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa,adani athu anasakaza malo anu opatulika. 19 Ife tili ngati anthu amenesimunawalamulirepongati iwo amene sanakhalepo anthu anu.
In Other Versions
Isaiah 63 in the ANGEFD
Isaiah 63 in the ANTPNG2D
Isaiah 63 in the AS21
Isaiah 63 in the BAGH
Isaiah 63 in the BBPNG
Isaiah 63 in the BBT1E
Isaiah 63 in the BDS
Isaiah 63 in the BEV
Isaiah 63 in the BHAD
Isaiah 63 in the BIB
Isaiah 63 in the BLPT
Isaiah 63 in the BNT
Isaiah 63 in the BNTABOOT
Isaiah 63 in the BNTLV
Isaiah 63 in the BOATCB
Isaiah 63 in the BOATCB2
Isaiah 63 in the BOBCV
Isaiah 63 in the BOCNT
Isaiah 63 in the BOECS
Isaiah 63 in the BOHCB
Isaiah 63 in the BOHCV
Isaiah 63 in the BOHLNT
Isaiah 63 in the BOHNTLTAL
Isaiah 63 in the BOICB
Isaiah 63 in the BOILNTAP
Isaiah 63 in the BOITCV
Isaiah 63 in the BOKCV
Isaiah 63 in the BOKCV2
Isaiah 63 in the BOKHWOG
Isaiah 63 in the BOKSSV
Isaiah 63 in the BOLCB
Isaiah 63 in the BOLCB2
Isaiah 63 in the BOMCV
Isaiah 63 in the BONAV
Isaiah 63 in the BONCB
Isaiah 63 in the BONLT
Isaiah 63 in the BONUT2
Isaiah 63 in the BOPLNT
Isaiah 63 in the BOSCB
Isaiah 63 in the BOSNC
Isaiah 63 in the BOTLNT
Isaiah 63 in the BOVCB
Isaiah 63 in the BOYCB
Isaiah 63 in the BPBB
Isaiah 63 in the BPH
Isaiah 63 in the BSB
Isaiah 63 in the CCB
Isaiah 63 in the CUV
Isaiah 63 in the CUVS
Isaiah 63 in the DBT
Isaiah 63 in the DGDNT
Isaiah 63 in the DHNT
Isaiah 63 in the DNT
Isaiah 63 in the ELBE
Isaiah 63 in the EMTV
Isaiah 63 in the ESV
Isaiah 63 in the FBV
Isaiah 63 in the FEB
Isaiah 63 in the GGMNT
Isaiah 63 in the GNT
Isaiah 63 in the HARY
Isaiah 63 in the HNT
Isaiah 63 in the IRVA
Isaiah 63 in the IRVB
Isaiah 63 in the IRVG
Isaiah 63 in the IRVH
Isaiah 63 in the IRVK
Isaiah 63 in the IRVM
Isaiah 63 in the IRVM2
Isaiah 63 in the IRVO
Isaiah 63 in the IRVP
Isaiah 63 in the IRVT
Isaiah 63 in the IRVT2
Isaiah 63 in the IRVU
Isaiah 63 in the ISVN
Isaiah 63 in the JSNT
Isaiah 63 in the KAPI
Isaiah 63 in the KBT1ETNIK
Isaiah 63 in the KBV
Isaiah 63 in the KJV
Isaiah 63 in the KNFD
Isaiah 63 in the LBA
Isaiah 63 in the LBLA
Isaiah 63 in the LNT
Isaiah 63 in the LSV
Isaiah 63 in the MAAL
Isaiah 63 in the MBV
Isaiah 63 in the MBV2
Isaiah 63 in the MHNT
Isaiah 63 in the MKNFD
Isaiah 63 in the MNG
Isaiah 63 in the MNT
Isaiah 63 in the MNT2
Isaiah 63 in the MRS1T
Isaiah 63 in the NAA
Isaiah 63 in the NASB
Isaiah 63 in the NBLA
Isaiah 63 in the NBS
Isaiah 63 in the NBVTP
Isaiah 63 in the NET2
Isaiah 63 in the NIV11
Isaiah 63 in the NNT
Isaiah 63 in the NNT2
Isaiah 63 in the NNT3
Isaiah 63 in the PDDPT
Isaiah 63 in the PFNT
Isaiah 63 in the RMNT
Isaiah 63 in the SBIAS
Isaiah 63 in the SBIBS
Isaiah 63 in the SBIBS2
Isaiah 63 in the SBICS
Isaiah 63 in the SBIDS
Isaiah 63 in the SBIGS
Isaiah 63 in the SBIHS
Isaiah 63 in the SBIIS
Isaiah 63 in the SBIIS2
Isaiah 63 in the SBIIS3
Isaiah 63 in the SBIKS
Isaiah 63 in the SBIKS2
Isaiah 63 in the SBIMS
Isaiah 63 in the SBIOS
Isaiah 63 in the SBIPS
Isaiah 63 in the SBISS
Isaiah 63 in the SBITS
Isaiah 63 in the SBITS2
Isaiah 63 in the SBITS3
Isaiah 63 in the SBITS4
Isaiah 63 in the SBIUS
Isaiah 63 in the SBIVS
Isaiah 63 in the SBT
Isaiah 63 in the SBT1E
Isaiah 63 in the SCHL
Isaiah 63 in the SNT
Isaiah 63 in the SUSU
Isaiah 63 in the SUSU2
Isaiah 63 in the SYNO
Isaiah 63 in the TBIAOTANT
Isaiah 63 in the TBT1E
Isaiah 63 in the TBT1E2
Isaiah 63 in the TFTIP
Isaiah 63 in the TFTU
Isaiah 63 in the TGNTATF3T
Isaiah 63 in the THAI
Isaiah 63 in the TNFD
Isaiah 63 in the TNT
Isaiah 63 in the TNTIK
Isaiah 63 in the TNTIL
Isaiah 63 in the TNTIN
Isaiah 63 in the TNTIP
Isaiah 63 in the TNTIZ
Isaiah 63 in the TOMA
Isaiah 63 in the TTENT
Isaiah 63 in the UBG
Isaiah 63 in the UGV
Isaiah 63 in the UGV2
Isaiah 63 in the UGV3
Isaiah 63 in the VBL
Isaiah 63 in the VDCC
Isaiah 63 in the YALU
Isaiah 63 in the YAPE
Isaiah 63 in the YBVTP
Isaiah 63 in the ZBP