Jeremiah 10 (BOGWICC)
1 Inu Aisraeli, imvani zimene Yehova akunena. 2 Yehova akuti,“Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu inakapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga,ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha. 3 Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe.Iwo amakadula mtengo ku nkhalangondipo mmisiri amawusema ndi sompho. 4 Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide;kenaka amachikhomerera ndi misomalikuti chisagwedezeke. 5 Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka.Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwendipo ayenera kunyamulidwapopeza sangathe nʼkuyenda komwe.Musachite nawo manthapopeza sangathe kukuchitani choyipandiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.” 6 Palibe wofanana nanu, Inu Yehova;Inu ndinu wamkulu,ndipo dzina lanu lili ndi mphamvu yayikulu. 7 Ndani amene angaleke kukuopani,inu Mfumu ya mitundu ya anthu?Chimenechi ndicho chokuyenerani.Pakati pa anthu anzeru onse komanso mafumu onsea mitundu ya anthu,palibe wina wofanana nanu. 8 Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru;malangizo awo amawatenga kuchokera kwa mafano achabechabe opanga ndi mitengo. 9 Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisindipo golide amachokera naye ku Ufazi.Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide.Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo.Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso. 10 Koma Yehova ndiye Mulungu woona;Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya.Akakwiya, dziko limagwedezeka;anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo. 11 “Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ” 12 Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zakendipo anayala thambo mwaluso lake. 13 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba;Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvulandi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene osungirako. 14 Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.Mafano akewo ndi abodza;alibe moyo mʼkati mwawo. 15 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa. 16 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonsekuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. 17 Sonkhanitsani katundu wanu,inu amene mukukhala mʼlinga la ankhondo. 18 Pakuti Yehova akuti,“Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onseamene akukhala mʼdziko lino;adzakhala pa mavutompaka adzamvetsa.” 19 Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga!Chilonda changa nʼchachikulu!”Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi,choncho ndingolipirira.” 20 Tenti yanga yawonongeka,zingwe zake zonse zaduka.Ana anga andisiya ndipo kulibenso.Palibenso amene adzandimangire tenti,kapena kufunyulula nsalu yake. 21 Abusa ndi opusandipo sanapemphe nzeru kwa Yehova;choncho palibe chimene anapindulandipo nkhosa zawo zonse zabalalika. 22 Tamvani! kukubwera mphekesera,phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto!Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda,malo okhala nkhandwe. 23 Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake;munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake. 24 Inu Yehova, langizeni, komatu mwachilungamo,osati ndi mkwiyo wanu,mungandiwononge kotheratu. 25 Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani,ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba.Iwo aja anasakaza Yakobo;amusakaza kotheratundipo awononga dziko lake.
In Other Versions
Jeremiah 10 in the ANGEFD
Jeremiah 10 in the ANTPNG2D
Jeremiah 10 in the AS21
Jeremiah 10 in the BAGH
Jeremiah 10 in the BBPNG
Jeremiah 10 in the BBT1E
Jeremiah 10 in the BDS
Jeremiah 10 in the BEV
Jeremiah 10 in the BHAD
Jeremiah 10 in the BIB
Jeremiah 10 in the BLPT
Jeremiah 10 in the BNT
Jeremiah 10 in the BNTABOOT
Jeremiah 10 in the BNTLV
Jeremiah 10 in the BOATCB
Jeremiah 10 in the BOATCB2
Jeremiah 10 in the BOBCV
Jeremiah 10 in the BOCNT
Jeremiah 10 in the BOECS
Jeremiah 10 in the BOHCB
Jeremiah 10 in the BOHCV
Jeremiah 10 in the BOHLNT
Jeremiah 10 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 10 in the BOICB
Jeremiah 10 in the BOILNTAP
Jeremiah 10 in the BOITCV
Jeremiah 10 in the BOKCV
Jeremiah 10 in the BOKCV2
Jeremiah 10 in the BOKHWOG
Jeremiah 10 in the BOKSSV
Jeremiah 10 in the BOLCB
Jeremiah 10 in the BOLCB2
Jeremiah 10 in the BOMCV
Jeremiah 10 in the BONAV
Jeremiah 10 in the BONCB
Jeremiah 10 in the BONLT
Jeremiah 10 in the BONUT2
Jeremiah 10 in the BOPLNT
Jeremiah 10 in the BOSCB
Jeremiah 10 in the BOSNC
Jeremiah 10 in the BOTLNT
Jeremiah 10 in the BOVCB
Jeremiah 10 in the BOYCB
Jeremiah 10 in the BPBB
Jeremiah 10 in the BPH
Jeremiah 10 in the BSB
Jeremiah 10 in the CCB
Jeremiah 10 in the CUV
Jeremiah 10 in the CUVS
Jeremiah 10 in the DBT
Jeremiah 10 in the DGDNT
Jeremiah 10 in the DHNT
Jeremiah 10 in the DNT
Jeremiah 10 in the ELBE
Jeremiah 10 in the EMTV
Jeremiah 10 in the ESV
Jeremiah 10 in the FBV
Jeremiah 10 in the FEB
Jeremiah 10 in the GGMNT
Jeremiah 10 in the GNT
Jeremiah 10 in the HARY
Jeremiah 10 in the HNT
Jeremiah 10 in the IRVA
Jeremiah 10 in the IRVB
Jeremiah 10 in the IRVG
Jeremiah 10 in the IRVH
Jeremiah 10 in the IRVK
Jeremiah 10 in the IRVM
Jeremiah 10 in the IRVM2
Jeremiah 10 in the IRVO
Jeremiah 10 in the IRVP
Jeremiah 10 in the IRVT
Jeremiah 10 in the IRVT2
Jeremiah 10 in the IRVU
Jeremiah 10 in the ISVN
Jeremiah 10 in the JSNT
Jeremiah 10 in the KAPI
Jeremiah 10 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 10 in the KBV
Jeremiah 10 in the KJV
Jeremiah 10 in the KNFD
Jeremiah 10 in the LBA
Jeremiah 10 in the LBLA
Jeremiah 10 in the LNT
Jeremiah 10 in the LSV
Jeremiah 10 in the MAAL
Jeremiah 10 in the MBV
Jeremiah 10 in the MBV2
Jeremiah 10 in the MHNT
Jeremiah 10 in the MKNFD
Jeremiah 10 in the MNG
Jeremiah 10 in the MNT
Jeremiah 10 in the MNT2
Jeremiah 10 in the MRS1T
Jeremiah 10 in the NAA
Jeremiah 10 in the NASB
Jeremiah 10 in the NBLA
Jeremiah 10 in the NBS
Jeremiah 10 in the NBVTP
Jeremiah 10 in the NET2
Jeremiah 10 in the NIV11
Jeremiah 10 in the NNT
Jeremiah 10 in the NNT2
Jeremiah 10 in the NNT3
Jeremiah 10 in the PDDPT
Jeremiah 10 in the PFNT
Jeremiah 10 in the RMNT
Jeremiah 10 in the SBIAS
Jeremiah 10 in the SBIBS
Jeremiah 10 in the SBIBS2
Jeremiah 10 in the SBICS
Jeremiah 10 in the SBIDS
Jeremiah 10 in the SBIGS
Jeremiah 10 in the SBIHS
Jeremiah 10 in the SBIIS
Jeremiah 10 in the SBIIS2
Jeremiah 10 in the SBIIS3
Jeremiah 10 in the SBIKS
Jeremiah 10 in the SBIKS2
Jeremiah 10 in the SBIMS
Jeremiah 10 in the SBIOS
Jeremiah 10 in the SBIPS
Jeremiah 10 in the SBISS
Jeremiah 10 in the SBITS
Jeremiah 10 in the SBITS2
Jeremiah 10 in the SBITS3
Jeremiah 10 in the SBITS4
Jeremiah 10 in the SBIUS
Jeremiah 10 in the SBIVS
Jeremiah 10 in the SBT
Jeremiah 10 in the SBT1E
Jeremiah 10 in the SCHL
Jeremiah 10 in the SNT
Jeremiah 10 in the SUSU
Jeremiah 10 in the SUSU2
Jeremiah 10 in the SYNO
Jeremiah 10 in the TBIAOTANT
Jeremiah 10 in the TBT1E
Jeremiah 10 in the TBT1E2
Jeremiah 10 in the TFTIP
Jeremiah 10 in the TFTU
Jeremiah 10 in the TGNTATF3T
Jeremiah 10 in the THAI
Jeremiah 10 in the TNFD
Jeremiah 10 in the TNT
Jeremiah 10 in the TNTIK
Jeremiah 10 in the TNTIL
Jeremiah 10 in the TNTIN
Jeremiah 10 in the TNTIP
Jeremiah 10 in the TNTIZ
Jeremiah 10 in the TOMA
Jeremiah 10 in the TTENT
Jeremiah 10 in the UBG
Jeremiah 10 in the UGV
Jeremiah 10 in the UGV2
Jeremiah 10 in the UGV3
Jeremiah 10 in the VBL
Jeremiah 10 in the VDCC
Jeremiah 10 in the YALU
Jeremiah 10 in the YAPE
Jeremiah 10 in the YBVTP
Jeremiah 10 in the ZBP