Jeremiah 3 (BOGWICC)

1 “Ngati munthu asudzula mkazi wakendipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.Komabe bwerera kwa ine,”akutero Yehova. 2 “Tayangʼana ku zitunda zowuma.Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanundi ntchito zanu zoyipa. 3 Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe. 4 Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanenakuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga, 5 kodi mudzandikwiyira nthawi zonse?Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’Umu ndimo mmene umayankhulira,koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.” 6 Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko. 7 Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi. 8 Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo. 9 Chiwerewere cha Israeli chinali chochititsa manyazi kotero kuti chinayipitsa dziko lonse. Anachita chigololo popembedza mafano a miyala ndi mitengo. 10 Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akutero Yehova. 11 Yehova anandiwuza kuti, “Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda. 12 Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti,“ ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova.‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale,pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova.‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale. 13 Ungovomera kulakwa kwakokuti unawukira Yehova Mulungu wako.Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendopansi pa mtengo uliwonse wogudira,ndiponso kuti sunandimvere,’ ”akutero Yehova. 14 “Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse. 15 Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha. 16 Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,”akutero Yehova. 17 Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa. 18 Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa. 19 “Ine mwini ndinati,“ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana angandikukupatsani dziko labwino kwambiri,cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’ndi kuti simudzaleka kunditsata. 20 Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,”akutero Yehova. 21 Mawu akumveka pa magomo,Aisraeli akulira ndi kupempha chifundochifukwa anatsata njira zoyipandi kuyiwala Yehova Mulungu wawo. 22 Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika;ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.” “Inde, tidzabwerera kwa Inupakuti ndinu Yehova Mulungu wathu. 23 Ndithu kupembedza pa magomokomanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu.Zoonadi chipulumutso cha Israelichili mwa Yehova Mulungu wathu basi. 24 Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindula ntchito za makolo athu,nkhosa ndi ngʼombe zawo,ana awo aamuna ndi aakazi. 25 Tilekeni tigone pansi mwa manyazi,ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe.Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu,ife pamodzi ndi makolo athukuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero linositinamvere Yehova Mulungu wathu.”

In Other Versions

Jeremiah 3 in the ANGEFD

Jeremiah 3 in the ANTPNG2D

Jeremiah 3 in the AS21

Jeremiah 3 in the BAGH

Jeremiah 3 in the BBPNG

Jeremiah 3 in the BBT1E

Jeremiah 3 in the BDS

Jeremiah 3 in the BEV

Jeremiah 3 in the BHAD

Jeremiah 3 in the BIB

Jeremiah 3 in the BLPT

Jeremiah 3 in the BNT

Jeremiah 3 in the BNTABOOT

Jeremiah 3 in the BNTLV

Jeremiah 3 in the BOATCB

Jeremiah 3 in the BOATCB2

Jeremiah 3 in the BOBCV

Jeremiah 3 in the BOCNT

Jeremiah 3 in the BOECS

Jeremiah 3 in the BOHCB

Jeremiah 3 in the BOHCV

Jeremiah 3 in the BOHLNT

Jeremiah 3 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 3 in the BOICB

Jeremiah 3 in the BOILNTAP

Jeremiah 3 in the BOITCV

Jeremiah 3 in the BOKCV

Jeremiah 3 in the BOKCV2

Jeremiah 3 in the BOKHWOG

Jeremiah 3 in the BOKSSV

Jeremiah 3 in the BOLCB

Jeremiah 3 in the BOLCB2

Jeremiah 3 in the BOMCV

Jeremiah 3 in the BONAV

Jeremiah 3 in the BONCB

Jeremiah 3 in the BONLT

Jeremiah 3 in the BONUT2

Jeremiah 3 in the BOPLNT

Jeremiah 3 in the BOSCB

Jeremiah 3 in the BOSNC

Jeremiah 3 in the BOTLNT

Jeremiah 3 in the BOVCB

Jeremiah 3 in the BOYCB

Jeremiah 3 in the BPBB

Jeremiah 3 in the BPH

Jeremiah 3 in the BSB

Jeremiah 3 in the CCB

Jeremiah 3 in the CUV

Jeremiah 3 in the CUVS

Jeremiah 3 in the DBT

Jeremiah 3 in the DGDNT

Jeremiah 3 in the DHNT

Jeremiah 3 in the DNT

Jeremiah 3 in the ELBE

Jeremiah 3 in the EMTV

Jeremiah 3 in the ESV

Jeremiah 3 in the FBV

Jeremiah 3 in the FEB

Jeremiah 3 in the GGMNT

Jeremiah 3 in the GNT

Jeremiah 3 in the HARY

Jeremiah 3 in the HNT

Jeremiah 3 in the IRVA

Jeremiah 3 in the IRVB

Jeremiah 3 in the IRVG

Jeremiah 3 in the IRVH

Jeremiah 3 in the IRVK

Jeremiah 3 in the IRVM

Jeremiah 3 in the IRVM2

Jeremiah 3 in the IRVO

Jeremiah 3 in the IRVP

Jeremiah 3 in the IRVT

Jeremiah 3 in the IRVT2

Jeremiah 3 in the IRVU

Jeremiah 3 in the ISVN

Jeremiah 3 in the JSNT

Jeremiah 3 in the KAPI

Jeremiah 3 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 3 in the KBV

Jeremiah 3 in the KJV

Jeremiah 3 in the KNFD

Jeremiah 3 in the LBA

Jeremiah 3 in the LBLA

Jeremiah 3 in the LNT

Jeremiah 3 in the LSV

Jeremiah 3 in the MAAL

Jeremiah 3 in the MBV

Jeremiah 3 in the MBV2

Jeremiah 3 in the MHNT

Jeremiah 3 in the MKNFD

Jeremiah 3 in the MNG

Jeremiah 3 in the MNT

Jeremiah 3 in the MNT2

Jeremiah 3 in the MRS1T

Jeremiah 3 in the NAA

Jeremiah 3 in the NASB

Jeremiah 3 in the NBLA

Jeremiah 3 in the NBS

Jeremiah 3 in the NBVTP

Jeremiah 3 in the NET2

Jeremiah 3 in the NIV11

Jeremiah 3 in the NNT

Jeremiah 3 in the NNT2

Jeremiah 3 in the NNT3

Jeremiah 3 in the PDDPT

Jeremiah 3 in the PFNT

Jeremiah 3 in the RMNT

Jeremiah 3 in the SBIAS

Jeremiah 3 in the SBIBS

Jeremiah 3 in the SBIBS2

Jeremiah 3 in the SBICS

Jeremiah 3 in the SBIDS

Jeremiah 3 in the SBIGS

Jeremiah 3 in the SBIHS

Jeremiah 3 in the SBIIS

Jeremiah 3 in the SBIIS2

Jeremiah 3 in the SBIIS3

Jeremiah 3 in the SBIKS

Jeremiah 3 in the SBIKS2

Jeremiah 3 in the SBIMS

Jeremiah 3 in the SBIOS

Jeremiah 3 in the SBIPS

Jeremiah 3 in the SBISS

Jeremiah 3 in the SBITS

Jeremiah 3 in the SBITS2

Jeremiah 3 in the SBITS3

Jeremiah 3 in the SBITS4

Jeremiah 3 in the SBIUS

Jeremiah 3 in the SBIVS

Jeremiah 3 in the SBT

Jeremiah 3 in the SBT1E

Jeremiah 3 in the SCHL

Jeremiah 3 in the SNT

Jeremiah 3 in the SUSU

Jeremiah 3 in the SUSU2

Jeremiah 3 in the SYNO

Jeremiah 3 in the TBIAOTANT

Jeremiah 3 in the TBT1E

Jeremiah 3 in the TBT1E2

Jeremiah 3 in the TFTIP

Jeremiah 3 in the TFTU

Jeremiah 3 in the TGNTATF3T

Jeremiah 3 in the THAI

Jeremiah 3 in the TNFD

Jeremiah 3 in the TNT

Jeremiah 3 in the TNTIK

Jeremiah 3 in the TNTIL

Jeremiah 3 in the TNTIN

Jeremiah 3 in the TNTIP

Jeremiah 3 in the TNTIZ

Jeremiah 3 in the TOMA

Jeremiah 3 in the TTENT

Jeremiah 3 in the UBG

Jeremiah 3 in the UGV

Jeremiah 3 in the UGV2

Jeremiah 3 in the UGV3

Jeremiah 3 in the VBL

Jeremiah 3 in the VDCC

Jeremiah 3 in the YALU

Jeremiah 3 in the YAPE

Jeremiah 3 in the YBVTP

Jeremiah 3 in the ZBP