Jeremiah 31 (BOGWICC)

1 “Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.” 2 Yehova akuti,“Anthu amene anapulumuka ku nkhondondinawakomera mtima mʼchipululu;pamene Aisraeli ankafuna kupumula.” 3 Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati,“Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire.Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani. 4 Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli;mudzasangalala poyimba tizitoliro tanu,ndipo mudzapita kukavina nawoanthu ovina mwachimwemwe. 5 Mudzalimanso minda ya mpesapa mapiri a Samariya;alimi adzadzala mphesandipo adzadya zipatso zake. 6 Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwulapa mapiri a Efereimu nati,‘Tiyeni tipite ku Ziyoni,kwa Yehova Mulungu wathu.’ ” 7 Yehova akuti,“Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo,fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse.Matamando anu amveke, ndipo munene kuti,‘Yehova wapulumutsa anthu akeotsala a Israeli.’ 8 Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto,ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezerandi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi.Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno. 9 Adzabwera akulira;koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza.Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzimʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo.Chifukwa ndine abambo ake a Israeli,ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba. 10 “Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja;‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsansondipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’ 11 Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakoboanawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu. 12 Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova.Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta,ana ankhosa ndi ana angʼombe.Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino,ndipo sadzamvanso chisoni. 13 Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala.Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo;ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo. 14 Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino,ndipo anthu anga adzakhuta ndi zabwino zanga,”akutero Yehova. 15 Yehova akuti,“Kulira kukumveka ku Rama,kulira kwakukulu,Rakele akulirira ana ake.Sakutonthozekachifukwa ana akewo palibe.” 16 Yehova akuti,“Leka kulirandi kukhetsa misozipakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,”akutero Yehova.“Iwo adzabwerako ku dziko la adani. 17 Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,”akutero Yehova.“Ana ako adzabwerera ku dziko lawo. 18 “Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti,‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva.Koma inu mwatiphunzitsa kumvera.Mutibweze kuti tithe kubwerera,chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga. 19 Popeza tatembenuka mtima,ndiye tikumva chisoni;popeza tazindikirandiye tikudziguguda pachifukwa.Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwachifukwa tinachimwa paubwana wathu.’ 20 Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,mwana amene Ine ndimakondwera naye?Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula,ndimamukumbukirabe.Kotero mtima wanga ukumufunabe;ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,”akutero Yehova. 21 “Muyike zizindikiro za mu msewu;muyimike zikwangwani.Yangʼanitsitsani msewuwo,njira imene mukuyendamo.Bwerera, iwe namwali wa Israeli,bwerera ku mizinda yako ija. 22 Udzakhala jenkha mpaka liti,iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika?Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.” 23 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’ 24 Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa. 25 Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.” 26 Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma. 27 “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachulukitsa anthu pamodzi ndi ziweto mʼdziko la Israeli ndi la Yuda. 28 Monga momwe ndinasamalira powazula, powagwetsa, powagumula, powawononga ndi powachita zoyipa, momwemonso ndidzasamala powamanga ndi powadzala” akutero Yehova. 29 “Mʼmasiku amenewo anthu sadzanenanso kuti,“Makolo adya mphesa zosapsa,koma mano a ana ndiye achita dziru. 30 Mʼmalo wake, munthu aliyense adzafa chifukwa cha tchimo lake. Iye amene adzadye mphesa zosapsazo ndiye amene mano ake adzachite dziru.” 31 “Masiku akubwera,” akutero Yehova,“pamene ndidzachita pangano latsopanondi Aisraelindiponso nyumba ya Yuda. 32 Silidzakhala ngati panganolimene ndinachita ndi makolo awopamene ndinawagwira padzanjanʼkuwatulutsa ku Igupto;chifukwa anaphwanya pangano langa,ngakhale ndinali mwamuna wawo,”akutero Yehova. 33 “Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeliatapita masiku amenewo,” akutero Yehova.“Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawondi kulilemba mʼmaganizo mwawo.Ine ndidzakhala Mulungu wawondipo iwo adzakhala anthu anga. 34 Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’chifukwa onse adzandidziwa Ine,kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”akutero Yehova.“Ndidzawakhululukira zoyipa zawondipo sindidzakumbukiranso machimo awo.” 35 Yehova akuti,Iye amene amakhazikitsa dzuwakuti liziwala masana,amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyeziziziwala usiku,amene amavundula nyanjakuti mafunde akokome,dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse: 36 Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga. 37 Yehova akuti,“Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo.Ngati patapezeka munthuamene angathe kupima zakuthambonʼkufufuza maziko a dziko lapansi.” 38 “Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya. 39 Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa. 40 Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”

In Other Versions

Jeremiah 31 in the ANGEFD

Jeremiah 31 in the ANTPNG2D

Jeremiah 31 in the AS21

Jeremiah 31 in the BAGH

Jeremiah 31 in the BBPNG

Jeremiah 31 in the BBT1E

Jeremiah 31 in the BDS

Jeremiah 31 in the BEV

Jeremiah 31 in the BHAD

Jeremiah 31 in the BIB

Jeremiah 31 in the BLPT

Jeremiah 31 in the BNT

Jeremiah 31 in the BNTABOOT

Jeremiah 31 in the BNTLV

Jeremiah 31 in the BOATCB

Jeremiah 31 in the BOATCB2

Jeremiah 31 in the BOBCV

Jeremiah 31 in the BOCNT

Jeremiah 31 in the BOECS

Jeremiah 31 in the BOHCB

Jeremiah 31 in the BOHCV

Jeremiah 31 in the BOHLNT

Jeremiah 31 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 31 in the BOICB

Jeremiah 31 in the BOILNTAP

Jeremiah 31 in the BOITCV

Jeremiah 31 in the BOKCV

Jeremiah 31 in the BOKCV2

Jeremiah 31 in the BOKHWOG

Jeremiah 31 in the BOKSSV

Jeremiah 31 in the BOLCB

Jeremiah 31 in the BOLCB2

Jeremiah 31 in the BOMCV

Jeremiah 31 in the BONAV

Jeremiah 31 in the BONCB

Jeremiah 31 in the BONLT

Jeremiah 31 in the BONUT2

Jeremiah 31 in the BOPLNT

Jeremiah 31 in the BOSCB

Jeremiah 31 in the BOSNC

Jeremiah 31 in the BOTLNT

Jeremiah 31 in the BOVCB

Jeremiah 31 in the BOYCB

Jeremiah 31 in the BPBB

Jeremiah 31 in the BPH

Jeremiah 31 in the BSB

Jeremiah 31 in the CCB

Jeremiah 31 in the CUV

Jeremiah 31 in the CUVS

Jeremiah 31 in the DBT

Jeremiah 31 in the DGDNT

Jeremiah 31 in the DHNT

Jeremiah 31 in the DNT

Jeremiah 31 in the ELBE

Jeremiah 31 in the EMTV

Jeremiah 31 in the ESV

Jeremiah 31 in the FBV

Jeremiah 31 in the FEB

Jeremiah 31 in the GGMNT

Jeremiah 31 in the GNT

Jeremiah 31 in the HARY

Jeremiah 31 in the HNT

Jeremiah 31 in the IRVA

Jeremiah 31 in the IRVB

Jeremiah 31 in the IRVG

Jeremiah 31 in the IRVH

Jeremiah 31 in the IRVK

Jeremiah 31 in the IRVM

Jeremiah 31 in the IRVM2

Jeremiah 31 in the IRVO

Jeremiah 31 in the IRVP

Jeremiah 31 in the IRVT

Jeremiah 31 in the IRVT2

Jeremiah 31 in the IRVU

Jeremiah 31 in the ISVN

Jeremiah 31 in the JSNT

Jeremiah 31 in the KAPI

Jeremiah 31 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 31 in the KBV

Jeremiah 31 in the KJV

Jeremiah 31 in the KNFD

Jeremiah 31 in the LBA

Jeremiah 31 in the LBLA

Jeremiah 31 in the LNT

Jeremiah 31 in the LSV

Jeremiah 31 in the MAAL

Jeremiah 31 in the MBV

Jeremiah 31 in the MBV2

Jeremiah 31 in the MHNT

Jeremiah 31 in the MKNFD

Jeremiah 31 in the MNG

Jeremiah 31 in the MNT

Jeremiah 31 in the MNT2

Jeremiah 31 in the MRS1T

Jeremiah 31 in the NAA

Jeremiah 31 in the NASB

Jeremiah 31 in the NBLA

Jeremiah 31 in the NBS

Jeremiah 31 in the NBVTP

Jeremiah 31 in the NET2

Jeremiah 31 in the NIV11

Jeremiah 31 in the NNT

Jeremiah 31 in the NNT2

Jeremiah 31 in the NNT3

Jeremiah 31 in the PDDPT

Jeremiah 31 in the PFNT

Jeremiah 31 in the RMNT

Jeremiah 31 in the SBIAS

Jeremiah 31 in the SBIBS

Jeremiah 31 in the SBIBS2

Jeremiah 31 in the SBICS

Jeremiah 31 in the SBIDS

Jeremiah 31 in the SBIGS

Jeremiah 31 in the SBIHS

Jeremiah 31 in the SBIIS

Jeremiah 31 in the SBIIS2

Jeremiah 31 in the SBIIS3

Jeremiah 31 in the SBIKS

Jeremiah 31 in the SBIKS2

Jeremiah 31 in the SBIMS

Jeremiah 31 in the SBIOS

Jeremiah 31 in the SBIPS

Jeremiah 31 in the SBISS

Jeremiah 31 in the SBITS

Jeremiah 31 in the SBITS2

Jeremiah 31 in the SBITS3

Jeremiah 31 in the SBITS4

Jeremiah 31 in the SBIUS

Jeremiah 31 in the SBIVS

Jeremiah 31 in the SBT

Jeremiah 31 in the SBT1E

Jeremiah 31 in the SCHL

Jeremiah 31 in the SNT

Jeremiah 31 in the SUSU

Jeremiah 31 in the SUSU2

Jeremiah 31 in the SYNO

Jeremiah 31 in the TBIAOTANT

Jeremiah 31 in the TBT1E

Jeremiah 31 in the TBT1E2

Jeremiah 31 in the TFTIP

Jeremiah 31 in the TFTU

Jeremiah 31 in the TGNTATF3T

Jeremiah 31 in the THAI

Jeremiah 31 in the TNFD

Jeremiah 31 in the TNT

Jeremiah 31 in the TNTIK

Jeremiah 31 in the TNTIL

Jeremiah 31 in the TNTIN

Jeremiah 31 in the TNTIP

Jeremiah 31 in the TNTIZ

Jeremiah 31 in the TOMA

Jeremiah 31 in the TTENT

Jeremiah 31 in the UBG

Jeremiah 31 in the UGV

Jeremiah 31 in the UGV2

Jeremiah 31 in the UGV3

Jeremiah 31 in the VBL

Jeremiah 31 in the VDCC

Jeremiah 31 in the YALU

Jeremiah 31 in the YAPE

Jeremiah 31 in the YBVTP

Jeremiah 31 in the ZBP