Jeremiah 49 (BOGWICC)

1 Yehova ananena izi: Amoni,“Kodi Israeli alibe ana aamuna?Kapena alibe mlowamʼmalo?Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi? 2 Koma nthawi ikubwera,”akutero Yehova,“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondoku Raba, likulu la Amoni;ndipo malo awo opembedzera milungu yawoadzatenthedwa ndi moto.Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawokuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”akutero Yehova. 3 “Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake. 4 Chifukwa chiyani mukunyadirachigwa chanu,inu anthu osakhulupirikaamene munadalira chuma chanu nʼkumati:‘Ndani angandithire nkhondo?’ 5 Ndidzabweretsa zoopsa pa iwezochokera kwa onse amene akuzungulira,”akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse.“Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake.Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo. 6 “Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,”akutero Yehova. 7 Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu:“Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani?Kodi anzeru analeka kupereka uphungu?Kodi nzeru zawo zinatheratu? 8 Inu anthu a ku Dedani, thawani,bwererani ndi kukabisala ku makwalalachifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esaupopeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika. 9 Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inuakanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?Anthu akuba akanafika usikuakanangotengako zimene akuzifuna zokha? 10 Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau.Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo,kotero kuti sadzathanso kubisala.Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka.Palibe wonena kuti, 11 ‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza.Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ” 12 Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho. 13 Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.” 14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova:Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti,“Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu!Konzekerani nkhondo!” 15 “Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina.Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu. 16 Kuopseza kwako kwakunyenga;kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,iwe amene umakhala mʼmapangaa mʼmatanthwe ndi mʼmapiri.Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga,ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”akutero Yehova. 17 “Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha.Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawochifukwa cha kuwonongeka kwake. 18 Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora,pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,”akutero Yehova,“motero palibe munthuamene adzakhala mu Edomu. 19 “Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodanikupita ku malo a msipu wobiriwira,Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo.Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine.Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani?Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?” 20 Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehovandakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani.Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolondipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo. 21 Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera;kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira. 22 Taonani, mtundu wina udzachita kuwulukanʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomuidzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira. 23 Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa:“Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita manthachifukwa amva nkhani yoyipa.Mitima yawo yagwidwa ndi manthandipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika. 24 Anthu a ku Damasiko alefuka.Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawachifukwa agwidwa ndi mantha aakulu.Ali ndi nkhawa komanso manthangati za mayi pa nthawi yake yochira. 25 Mzinda wotchukandi wachikondwerero uja wasiyidwa! 26 Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa;ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,”akutero Yehova Wamphamvuzonse. 27 “Ndidzatentha malinga a Damasiko;moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.” 28 Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa:“Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara.Kawonongeni anthu a kummawako. 29 Landani matenti awo ndi nkhosa zawo,ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo.Mutengenso ngamira zawo.Anthu adzafuwula kwa iwo kuti,‘Kuli zoopsa mbali zonse!’ 30 “Thawani mofulumira!Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,”akutero Yehova.“Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu;wakonzekera zoti alimbane nanu. 31 “Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere,umene ukukhala mosatekeseka,”akutero Yehova,“mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo;anthu ake amakhala pa okha. 32 Ngamira zawo zidzafunkhidwa,ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa.Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali.Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,”akutero Yehova. 33 “Hazori adzasanduka bwinja,malo okhalamo nkhandwempaka muyaya.Palibe munthu amene adzayendemo.” 34 Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu: 35 Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu,umene uli chida chawo champhamvu. 36 Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamukuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga;ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi,ndipo sipadzakhala dzikolimene anthu a ku Elamu sadzafikako. 37 A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awokomanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo.Ndidzawagwetsera mkwiyo wangandipo adzakhala pa mavuto,”akutero Yehova.“Ndidzawapirikitsa ndi lupangampaka nditawatheratu. 38 Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamundipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,”akutero Yehova. 39 “Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezeraanthu a ku Elamu dziko lawo,”akutero Yehova.

In Other Versions

Jeremiah 49 in the ANGEFD

Jeremiah 49 in the ANTPNG2D

Jeremiah 49 in the AS21

Jeremiah 49 in the BAGH

Jeremiah 49 in the BBPNG

Jeremiah 49 in the BBT1E

Jeremiah 49 in the BDS

Jeremiah 49 in the BEV

Jeremiah 49 in the BHAD

Jeremiah 49 in the BIB

Jeremiah 49 in the BLPT

Jeremiah 49 in the BNT

Jeremiah 49 in the BNTABOOT

Jeremiah 49 in the BNTLV

Jeremiah 49 in the BOATCB

Jeremiah 49 in the BOATCB2

Jeremiah 49 in the BOBCV

Jeremiah 49 in the BOCNT

Jeremiah 49 in the BOECS

Jeremiah 49 in the BOHCB

Jeremiah 49 in the BOHCV

Jeremiah 49 in the BOHLNT

Jeremiah 49 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 49 in the BOICB

Jeremiah 49 in the BOILNTAP

Jeremiah 49 in the BOITCV

Jeremiah 49 in the BOKCV

Jeremiah 49 in the BOKCV2

Jeremiah 49 in the BOKHWOG

Jeremiah 49 in the BOKSSV

Jeremiah 49 in the BOLCB

Jeremiah 49 in the BOLCB2

Jeremiah 49 in the BOMCV

Jeremiah 49 in the BONAV

Jeremiah 49 in the BONCB

Jeremiah 49 in the BONLT

Jeremiah 49 in the BONUT2

Jeremiah 49 in the BOPLNT

Jeremiah 49 in the BOSCB

Jeremiah 49 in the BOSNC

Jeremiah 49 in the BOTLNT

Jeremiah 49 in the BOVCB

Jeremiah 49 in the BOYCB

Jeremiah 49 in the BPBB

Jeremiah 49 in the BPH

Jeremiah 49 in the BSB

Jeremiah 49 in the CCB

Jeremiah 49 in the CUV

Jeremiah 49 in the CUVS

Jeremiah 49 in the DBT

Jeremiah 49 in the DGDNT

Jeremiah 49 in the DHNT

Jeremiah 49 in the DNT

Jeremiah 49 in the ELBE

Jeremiah 49 in the EMTV

Jeremiah 49 in the ESV

Jeremiah 49 in the FBV

Jeremiah 49 in the FEB

Jeremiah 49 in the GGMNT

Jeremiah 49 in the GNT

Jeremiah 49 in the HARY

Jeremiah 49 in the HNT

Jeremiah 49 in the IRVA

Jeremiah 49 in the IRVB

Jeremiah 49 in the IRVG

Jeremiah 49 in the IRVH

Jeremiah 49 in the IRVK

Jeremiah 49 in the IRVM

Jeremiah 49 in the IRVM2

Jeremiah 49 in the IRVO

Jeremiah 49 in the IRVP

Jeremiah 49 in the IRVT

Jeremiah 49 in the IRVT2

Jeremiah 49 in the IRVU

Jeremiah 49 in the ISVN

Jeremiah 49 in the JSNT

Jeremiah 49 in the KAPI

Jeremiah 49 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 49 in the KBV

Jeremiah 49 in the KJV

Jeremiah 49 in the KNFD

Jeremiah 49 in the LBA

Jeremiah 49 in the LBLA

Jeremiah 49 in the LNT

Jeremiah 49 in the LSV

Jeremiah 49 in the MAAL

Jeremiah 49 in the MBV

Jeremiah 49 in the MBV2

Jeremiah 49 in the MHNT

Jeremiah 49 in the MKNFD

Jeremiah 49 in the MNG

Jeremiah 49 in the MNT

Jeremiah 49 in the MNT2

Jeremiah 49 in the MRS1T

Jeremiah 49 in the NAA

Jeremiah 49 in the NASB

Jeremiah 49 in the NBLA

Jeremiah 49 in the NBS

Jeremiah 49 in the NBVTP

Jeremiah 49 in the NET2

Jeremiah 49 in the NIV11

Jeremiah 49 in the NNT

Jeremiah 49 in the NNT2

Jeremiah 49 in the NNT3

Jeremiah 49 in the PDDPT

Jeremiah 49 in the PFNT

Jeremiah 49 in the RMNT

Jeremiah 49 in the SBIAS

Jeremiah 49 in the SBIBS

Jeremiah 49 in the SBIBS2

Jeremiah 49 in the SBICS

Jeremiah 49 in the SBIDS

Jeremiah 49 in the SBIGS

Jeremiah 49 in the SBIHS

Jeremiah 49 in the SBIIS

Jeremiah 49 in the SBIIS2

Jeremiah 49 in the SBIIS3

Jeremiah 49 in the SBIKS

Jeremiah 49 in the SBIKS2

Jeremiah 49 in the SBIMS

Jeremiah 49 in the SBIOS

Jeremiah 49 in the SBIPS

Jeremiah 49 in the SBISS

Jeremiah 49 in the SBITS

Jeremiah 49 in the SBITS2

Jeremiah 49 in the SBITS3

Jeremiah 49 in the SBITS4

Jeremiah 49 in the SBIUS

Jeremiah 49 in the SBIVS

Jeremiah 49 in the SBT

Jeremiah 49 in the SBT1E

Jeremiah 49 in the SCHL

Jeremiah 49 in the SNT

Jeremiah 49 in the SUSU

Jeremiah 49 in the SUSU2

Jeremiah 49 in the SYNO

Jeremiah 49 in the TBIAOTANT

Jeremiah 49 in the TBT1E

Jeremiah 49 in the TBT1E2

Jeremiah 49 in the TFTIP

Jeremiah 49 in the TFTU

Jeremiah 49 in the TGNTATF3T

Jeremiah 49 in the THAI

Jeremiah 49 in the TNFD

Jeremiah 49 in the TNT

Jeremiah 49 in the TNTIK

Jeremiah 49 in the TNTIL

Jeremiah 49 in the TNTIN

Jeremiah 49 in the TNTIP

Jeremiah 49 in the TNTIZ

Jeremiah 49 in the TOMA

Jeremiah 49 in the TTENT

Jeremiah 49 in the UBG

Jeremiah 49 in the UGV

Jeremiah 49 in the UGV2

Jeremiah 49 in the UGV3

Jeremiah 49 in the VBL

Jeremiah 49 in the VDCC

Jeremiah 49 in the YALU

Jeremiah 49 in the YAPE

Jeremiah 49 in the YBVTP

Jeremiah 49 in the ZBP