Jeremiah 50 (BOGWICC)
1 Uthenga umene Yehova anayankhula ndi mneneri Yeremiya wonena za mzinda wa Babuloni ndi anthu ake ndi uwu: 2 “Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina,kweza mbendera ndipo ulengeze;usabise kanthu, koma uwawuze kuti,‘Babuloni wagwa;mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi,nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha.Milungu yake yagwidwa ndi manthandipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’ 3 Mtundu wa anthu wochokera kumpoto wadzathira nkhondo Babulonindi kusandutsa bwinja dziko lake.Kumeneko sikudzakhalansomunthu kapena nyama. 4 “Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”akutero Yehova,“anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yudaonse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna. 5 Adzafunsa njira ya ku Ziyonindi kuyamba ulendo wopita kumeneko.Iwo adzadzipereka kwa Yehovapochita naye pangano lamuyayalimene silidzayiwalika. 6 “Anthu anga ali ngati nkhosa zotayika;abusa awoanawasocheretsa mʼmapiri.Iwo anayendayenda mʼmapiri ndi mʼzitundampaka kuyiwala kwawo. 7 Aliyense amene anawapeza anawawononga;adani awo anati, ‘Ife si olakwa,chifukwa iwo anachimwira Yehova, amene ali mpumulo wawo weniwenindi amene makolo awo anamukhulupirira.’ 8 “Thawaniko ku Babuloni;chokani mʼdziko la Ababuloni.Muyambe inu kutuluka ngati atonde amene amatsogolera ziweto. 9 Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu inandi kubwera nalo kuchokera kumpotokudzamenyana ndi Babuloni.Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni.Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso,yosapita padera. 10 Motero Ababuloni adzafunkhidwa;ndipo onse omufunkha adzakhuta,”akutero Yehova. 11 “Inu Ababuloni, munawononga anthu anga osankhika.Ndiye pano mukukondwa, mukusangalala.Mukulumphalumpha mokondwa ngati mwana wangʼombe wopuntha tirigundiponso mukulira monyada ngati ngʼombe zazimuna. 12 Koma mzinda wanu udzachititsidwa manyazi kwambiri.Mzinda umene uli ngati mayi wanu udzanyazitsidwa.Babuloni adzasanduka chitsirizira cha anthu onse.Mzinda wawo udzakhala ngati thengo, ngati dziko lowuma lachipululu. 13 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova Babuloni adzakhala wopanda anthundipo adzakhala chipululu chokhachokha.Onse odutsa kumeneko adzachita mantha ndipo azidzangotsonyachifukwa cha chiwonongeko chake chachikulu. 14 “Inu okoka uta,konzekani kuti muthire nkhondo mzinda wa Babuloni mbali zonse.Muponyereni mivi yanu yonsechifukwa anachimwira Yehova. 15 Mufuwulireni mbali zonse pakuti wagonja.Nsanja zake zagwa.Malinga ake agwetsedwa.Kumeneku ndiko kulipsira kwa Yehova.Mulipsireni,mumuchite zomwe iye anachitira anthu ena. 16 Chotsani ku Babuloni munthu wofesa mbewu aliyense,ndiponso wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthawi yokolola.Poona lupanga la ozunza anzawo,aliyense adzabwerera kwa anthu ake;adzathawira ku dziko la kwawo. 17 “Aisraeli ali ngati nkhosa zomwe zabalalikapothamangitsidwa ndi mikango.Mfumu ya ku Asiriya ndiye inayamba kuwapha Aisraeliwo.Wotsiriza anali Nebukadinezaramfumu ya ku Babuloniamene anachita ngati kuphwanya mafupa ake.” 18 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,“Ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi dziko lakemonga momwe ndinalangira mfumu ya ku Asiriya. 19 Koma ndidzabwezera Israeli ku msipu wakendipo adzadya mʼminda ya ku Karimeli ndi Basani;adzadya nakhuta ku mapiria ku Efereimu ndi Giliyadi. 20 Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”akutero Yehova,“anthu adzafunafuna zolakwa za Israelikoma sadzapeza nʼchimodzi chomwe,ndipo adzafufuza machimo a Yuda,koma sadzapeza ndi limodzi lomwe,chifukwa otsala amene ndawasiya ndidzawakhululukira. 21 “Lithireni nkhondo dziko la Merataimundi anthu okhala ku Pekodi.Muwaphe ndi lupanga ndi kuwawonongeratu,”akutero Yehova.“Chitani zonse monga momwe ndakulamulani. 22 Mʼdziko muli phokoso la nkhondo,phokoso la chiwonongeko chachikulu! 23 Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekerauja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi.Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa manthapakati pa mitundu ina! 24 Ndinakutchera msampha, iwe Babuloni,ndipo wakodwamo iwe wosazindikira kanthu;unapezeka ndiponso unakodwachifukwa unalimbana ndi Yehova. 25 Yehova watsekula nyumba ya zida zakendipo watulutsa zida za ukali wake,pakuti Ambuye Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ntchito yoti agwiremʼdziko la Ababuloni. 26 Mumenyane naye Babuloni mbali zonse.Anthu ake muwawunjikengati milu ya tirigu.Muwawononge kotheratundipo pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe. 27 Iphani ankhondo ake onse.Onse aphedwe ndithu.Tsoka lawagwerapakuti tsiku lawo lachilango lafika. 28 Tikumva anthu othawa nkhondo ochokera ku Babuloniakulengeza mu Yerusalemuza kulipsira kwa Yehova Mulungu wathu.Iye akulipsira chifukwa chowononga Nyumba yake. 29 “Itanani anthu oponya mivi kudzathira nkhondo Babuloni.Muyitanenso onse amene amakoka mauta.Mangani misasa ya nkhondo momuzungulira;musalole munthu aliyense kuthawa.Muchiteni monga momweiye anachitira anthu ena.Iyeyu ananyozaYehova, Woyera wa Israeli. 30 Nʼchifukwa chake, anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo ake;ankhondo ake onse adzaphedwa tsiku limenelo,”akutero Yehova. 31 “Taona, ndikukuthira nkhondo, iwe wodzikuzawe,”akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,“chifukwa tsiku lako lafika,nthawi yoti ndikulange yakwana. 32 Wodzikuzawe udzapunthwa nʼkugwandipo palibe amene adzakudzutse;ndidzayatsa moto mʼmizinda yakeumene udzanyeketsa onse amene amuzungulira.” 33 Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Anthu a ku Israeli akuzunzidwa,pamodzi ndi anthu a ku Yuda,ndipo onse amene anawagwira ukapolo awagwiritsitsa,akukana kuwamasula. 34 Koma Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu;dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.Iye adzawateteza molimba pa mlandu wawonʼcholinga choti abweretse mtendere mʼdziko lawo,koma adzavutitsa okhala ku Babuloni.” 35 Yehova akuti,“Imfa yalunjika pa Ababuloni,pa akuluakulu akendi pa anthu ake a nzeru! 36 Imfa yalunjika pa aneneri abodzakuti asanduke zitsiru.Imfa yalunjika pa ankhondo akekuti agwidwe ndi mantha aakulu. 37 Imfa ilunjike pa akavalo ake ndi magaleta ake.Ilunjikanso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pawokuti asanduke ngati akazi.Chiwonongeko chilunjikenso pa chuma chakekuti chidzafunkhidwe. 38 Chilala chilunjike pa madzi akekuti aphwe.Babuloni ndi dziko la mafano,ndipo anthu afika poyaluka nawo mafanowo. 39 “Nʼchifukwa chake nyama zakuthengo ndi afisi zidzakhala kumenekondipo kudzakhalanso akadzidzi.Kumeneko sikudzapezekako anthu,ndithu anthu sadzakhalako pa mibado yonse. 40 Monga momwe Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomorapamodzi ndi mizinda yonse yozungulira,”akutero Yehova,“momwemonso palibe amene adzakhale kumeneko;anthu sadzayendanso mʼmenemo. 41 “Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto;mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri,wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi. 42 Atenga mauta ndi mikondo;ndi anthu ankhanza ndipo alibe chifundo.Phokoso lawo likumveka ngati mkokomo wa nyanja.Akwera pa akavalo awo,ndipo akonzekera kudzakuthira nkhondoiwe Babuloni. 43 Mfumu ya ku Babuloni yamva za mbiri yawo,ndipo yalobodokeratu.Ikuda nkhawa,ikumva ululu ngati wa mayi pa nthawi yake yochira. 44 Taonani, monga mkango wochokera ku nkhalango ya ku Yorodanikupita ku msipu wobiriwira,momwemonso ine ndidzapirikitsa Babuloni mʼdziko lake mwadzidzidzi.Pambuyo pake ndidzawayikira wowalamulira amene ndamufuna Ine.Wofanana nane ndani ndipo ndani amene angalimbane nane?Ndi mtsogoleri wa dziko uti amene anganditengere ku bwalo la milandu?” 45 Nʼchifukwa chake imvani.Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Babuloni.Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolondipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo. 46 Akadzagwa Babuloni padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera,ndipo kulira kwawo kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.