Jeremiah 51 (BOGWICC)

1 Yehova akuti,“Taonani, ndidzadzutsa mphepo yowonongakuti iwononge Babuloni pamodzi ndi anthu a ku Lebi Kamai. 2 Ndidzatuma alendo ku Babulonikudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu.Iwo adzalimbana naye ku mbali zonsepa tsiku la masautso ake. 3 Okoka uta musawalekererekapena wonyadira chovala chawo chankhondo.Musawasiye anyamata ake kuti akhale ndi moyo;koma muwononge ankhondo ake kotheratu. 4 Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babulonilomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe. 5 Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiyendi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse,koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimopamaso pa Woyerayo wa Israeli. 6 “Thawaniko ku Babuloni!Aliyense apulumutse moyo wake!Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake.Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange;Yehova adzamulipsira. 7 Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova;kuti aledzeretse dziko lonse lapansi.Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake;nʼchifukwa chake tsopano inachita misala. 8 Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka.Mulireni!Mfunireni mankhwala opha ululu wake;mwina iye nʼkuchira.” 9 Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni,koma sanachire;tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo,pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga,wafika mpaka kumwamba.’ 10 “ ‘Yehova waonetsa poyera kuti ndife osalakwa;tiyeni tilengeze mu Ziyonizimene Yehova Mulungu wathu wachita.’ 11 “Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi,popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni.Motero adzalipsira Ababulonichifukwa chowononga Nyumba yake.Ndiye Yehova akuti,‘Nolani mivi, tengani zishango.’ 12 Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni!Limbitsani oteteza,ikani alonda pa malo awo,konzekerani kulalira.Pakuti Yehova watsimikizandipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni. 13 Inu muli ndi mitsinje yambirindi chuma chambiri.Koma chimaliziro chanu chafika,moyo wanu watha. 14 Yehova Wamphamvuzonse analumbira pali Iye mwini kuti:Ndidzakutumizira adani ochuluka ngati dzombe,kuti adzakuthire nkhondo ndipo adzafuwula kuonetsa kuti apambana. 15 “Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zakendipo anayala thambo mwaluso lake. 16 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba.Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvulandi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira. 17 “Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.Mafano akewo ndi abodza;alibe moyo mʼkati mwawo. 18 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa. 19 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse,kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. 20 “Iwe Babuloni ndi ndodo yanga,chida changa chankhondo.Ndi iwe ndimaphwanya mitundu ya anthu,ndi iwe ndimawononga maufumu, 21 ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo,ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake. 22 Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi,ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata,ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali. 23 Ndi iwe ndimaphwanya mʼbusa ndi ziweto,ndi iwe ndimaphwanya mlimi ndi ngʼombe,ndi iwe ndimaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri a ankhondo. 24 “Inu mukuona ndidzalanga Babuloni ndi onse amene amakhala mʼdziko la Babuloni chifukwa cha zolakwa zonse anachita ku Ziyoni,” akutero Yehova. 25 “Taonani, ndikukuzenga mlandu, iwe phiri lowononga,amene umawononga dziko lonse lapansi,”akutero Yehova.“Ndidzatambalitsa dzanja langa pofuna kukulanga,kukugubuduzira pansi kuchokera pa matanthwe ako,ndi kukusandutsa kukhala phiri lopserera. 26 Palibe ngakhale ndi mwala wako umodzi umene anthu adzawutengakuti awugwiritse ntchito kumangira nyumba,chifukwa iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,”akutero Yehova. 27 “Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko!Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu!Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo;itanani maufumu awa:Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo.Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye;tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe. 28 Konzekeretsani mitundu ya anthu.Amenewa ndiwo mafumu a Amedi,abwanamkubwa awo, atsogoleri a ankhondo,ndiponso ankhondo a mayiko amene amawalamulira, kuti idzathire nkhondo Babuloni. 29 Dziko likunjenjemera ndi kunthunthumira,chifukwa zidzachitikadi zimene Yehova wakonzera Babuloni;kusakaza dziko la Babulonikuti musapezeke wokhalamo. 30 Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo;iwo angokhala mʼmalinga awo.Mphamvu zawo zatheratu;ndipo akhala ngati akazi.Malo ake wokhala atenthedwa;mipiringidzo ya zipata zake yathyoka. 31 Othamanga akungopezanapezana,amithenga akungotsatanatsatanakudzawuza mfumu ya ku Babulonikuti alande mzinda wake wonse. 32 Madooko onse alandidwa,malo onse obisalamo alonda atenthedwa ndi moto,ndipo ankhondo onse asokonezeka.” 33 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,“Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigupa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti,Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.” 34 A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga,watiphwanya,ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu.Watimeza ngati ngʼona,wakhuta ndi zakudya zathu zokoma,kenaka nʼkutilavula.” 35 Anthu a ku Ziyoni anene kuti,“Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.”Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti,“Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.” 36 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,“Taona, ndidzakumenyera nkhondondi kukulipsirira;ndidzawumitsa nyanja yakendipo akasupe ake adzaphwa. 37 Motero Babuloni adzasanduka mulu wa nyumba zogumuka,malo okhala nkhandwe,malo ochititsa mantha ndi onyozedwa,malo wopanda aliyense wokhalamo. 38 Anthu ake onse adzabangula ngati mkango,adzadzuma ngati ana amkango. 39 Ngati achita dyerandiye ndidzawakonzera madyererondi kuwaledzeretsa,kotero kuti adzasangalala,kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,”akutero Yehova. 40 “Ine ndidzawatengakuti akaphedwe ngati ana ankhosa onenepa,ngati nkhosa zazimuna ndi mbuzi. 41 “Ndithu Babuloni walandidwa,mzinda umene dziko lonse lapansi limanyadira wagwidwa!Taonani, mmene Babuloni wasandukira chinthu chochititsa manthapakati pa mitundu ya anthu! 42 Nyanja yakwera ndi kumiza Babuloni;mafunde ake okokoma aphimba Babuloni. 43 Mizinda yake yasanduka bwinja,dziko lowuma ndi lachipululu,dziko losakhalamo wina aliyense,dziko losayendamo munthu aliyense. 44 Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni,ndidzamusanzitsa zimene anameza.Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye.Malinga a Babuloni agwa. 45 “Tulukani mʼBabuloni anthu anga!Pulumutsani miyoyo yanu!Thawani mkwiyo woopsa wa Yehova. 46 Musataye mtima kapena kuchita manthapamene mphekesera zikumveka mʼdziko mwanu.Chaka ndi chaka pamabuka mphekeseraza ziwawa mʼdziko lapansi,ndiponso yakuti mfumu yakuti ikuthira nkhondo mfumu ina. 47 Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithupamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni;dziko lake lonse lidzachita manyazindi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake. 48 Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemozidzayimba mokondwa chifukwa cha kugwa kwa Babuloni.Anthu owononga ochokera kumpotoadzamuthira nkhondo,”akutero Yehova. 49 “Babuloni anapha anthu ambiri pa dziko lapansi.Tsono, nawo anthu a ku Babuloni ayenera kuphedwachifukwa anapha anthu a ku Yerusalemu. 50 Inu amene munapulumuka ku nkhondo ya Babuloni,chokani pano ndipo musazengereze!Kumbukirani Yehova ngakhale muli ku mayiko akutali,ganizirani za Yerusalemu.” 51 Inu mukuti, “Tikuchita manyazi,chifukwa tanyozedwandipo nkhope zathu zili ndi manyazi,chifukwa anthu achilendo alowamalo opatulika a Nyumba ya Yehova.” 52 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,“Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake,ndipo mʼdziko lake lonseanthu ovulala adzabuwula. 53 Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalengandi kulimbitsa nsanja zake,ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,”akutero Yehova. 54 “Imvani mfuwu wolira kuchokera ku Babuloni.Imvani phokoso lachiwonongeko chachikulukuchokera mʼdziko la Babuloni. 55 Pakuti Yehova akuwononga Babuloni,ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu.Mfuwu wa adani ukumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri.Phokoso lawo likunka likwererakwerera. 56 Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni,ankhondo ake agwidwa,ndipo mauta awo athyoka.Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango;adzabwezera kwathunthu. 57 Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake,abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo;adzagona kwamuyaya osadzukanso,”akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. 58 Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwandipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa;mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe.Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.” 59 Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo. 60 Yeremiya anali atalemba mʼbuku za masautso onse amene adzafike pa Babuloni ndi zina zonse zokhudza Babuloni. 61 Yeremiya anawuza Seraya kuti, “Ukakafika ku Babuloni, ukaonetsetse kuti wawawerengera anthu onse mawu onsewa. 62 Ndipo ukanene kuti, ‘Inu Yehova, mwanena kuti mudzawononga malo ano, kotero kuti simudzatsala munthu kapena nyama mʼdziko muno; lidzakhala chipululu mpaka muyaya.’ 63 Ukakatha kuwerenga bukuli, ukalimangirire ku mwala ndipo ukaliponye pakati pa mtsinje wa Yufurate. 64 Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene adzamirire Babuloni ndipo sadzadzukanso chifukwa cha masautso amene adzamugwere.’ ” Mawu a Yeremiya athera pamenepa.

In Other Versions

Jeremiah 51 in the ANGEFD

Jeremiah 51 in the ANTPNG2D

Jeremiah 51 in the AS21

Jeremiah 51 in the BAGH

Jeremiah 51 in the BBPNG

Jeremiah 51 in the BBT1E

Jeremiah 51 in the BDS

Jeremiah 51 in the BEV

Jeremiah 51 in the BHAD

Jeremiah 51 in the BIB

Jeremiah 51 in the BLPT

Jeremiah 51 in the BNT

Jeremiah 51 in the BNTABOOT

Jeremiah 51 in the BNTLV

Jeremiah 51 in the BOATCB

Jeremiah 51 in the BOATCB2

Jeremiah 51 in the BOBCV

Jeremiah 51 in the BOCNT

Jeremiah 51 in the BOECS

Jeremiah 51 in the BOHCB

Jeremiah 51 in the BOHCV

Jeremiah 51 in the BOHLNT

Jeremiah 51 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 51 in the BOICB

Jeremiah 51 in the BOILNTAP

Jeremiah 51 in the BOITCV

Jeremiah 51 in the BOKCV

Jeremiah 51 in the BOKCV2

Jeremiah 51 in the BOKHWOG

Jeremiah 51 in the BOKSSV

Jeremiah 51 in the BOLCB

Jeremiah 51 in the BOLCB2

Jeremiah 51 in the BOMCV

Jeremiah 51 in the BONAV

Jeremiah 51 in the BONCB

Jeremiah 51 in the BONLT

Jeremiah 51 in the BONUT2

Jeremiah 51 in the BOPLNT

Jeremiah 51 in the BOSCB

Jeremiah 51 in the BOSNC

Jeremiah 51 in the BOTLNT

Jeremiah 51 in the BOVCB

Jeremiah 51 in the BOYCB

Jeremiah 51 in the BPBB

Jeremiah 51 in the BPH

Jeremiah 51 in the BSB

Jeremiah 51 in the CCB

Jeremiah 51 in the CUV

Jeremiah 51 in the CUVS

Jeremiah 51 in the DBT

Jeremiah 51 in the DGDNT

Jeremiah 51 in the DHNT

Jeremiah 51 in the DNT

Jeremiah 51 in the ELBE

Jeremiah 51 in the EMTV

Jeremiah 51 in the ESV

Jeremiah 51 in the FBV

Jeremiah 51 in the FEB

Jeremiah 51 in the GGMNT

Jeremiah 51 in the GNT

Jeremiah 51 in the HARY

Jeremiah 51 in the HNT

Jeremiah 51 in the IRVA

Jeremiah 51 in the IRVB

Jeremiah 51 in the IRVG

Jeremiah 51 in the IRVH

Jeremiah 51 in the IRVK

Jeremiah 51 in the IRVM

Jeremiah 51 in the IRVM2

Jeremiah 51 in the IRVO

Jeremiah 51 in the IRVP

Jeremiah 51 in the IRVT

Jeremiah 51 in the IRVT2

Jeremiah 51 in the IRVU

Jeremiah 51 in the ISVN

Jeremiah 51 in the JSNT

Jeremiah 51 in the KAPI

Jeremiah 51 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 51 in the KBV

Jeremiah 51 in the KJV

Jeremiah 51 in the KNFD

Jeremiah 51 in the LBA

Jeremiah 51 in the LBLA

Jeremiah 51 in the LNT

Jeremiah 51 in the LSV

Jeremiah 51 in the MAAL

Jeremiah 51 in the MBV

Jeremiah 51 in the MBV2

Jeremiah 51 in the MHNT

Jeremiah 51 in the MKNFD

Jeremiah 51 in the MNG

Jeremiah 51 in the MNT

Jeremiah 51 in the MNT2

Jeremiah 51 in the MRS1T

Jeremiah 51 in the NAA

Jeremiah 51 in the NASB

Jeremiah 51 in the NBLA

Jeremiah 51 in the NBS

Jeremiah 51 in the NBVTP

Jeremiah 51 in the NET2

Jeremiah 51 in the NIV11

Jeremiah 51 in the NNT

Jeremiah 51 in the NNT2

Jeremiah 51 in the NNT3

Jeremiah 51 in the PDDPT

Jeremiah 51 in the PFNT

Jeremiah 51 in the RMNT

Jeremiah 51 in the SBIAS

Jeremiah 51 in the SBIBS

Jeremiah 51 in the SBIBS2

Jeremiah 51 in the SBICS

Jeremiah 51 in the SBIDS

Jeremiah 51 in the SBIGS

Jeremiah 51 in the SBIHS

Jeremiah 51 in the SBIIS

Jeremiah 51 in the SBIIS2

Jeremiah 51 in the SBIIS3

Jeremiah 51 in the SBIKS

Jeremiah 51 in the SBIKS2

Jeremiah 51 in the SBIMS

Jeremiah 51 in the SBIOS

Jeremiah 51 in the SBIPS

Jeremiah 51 in the SBISS

Jeremiah 51 in the SBITS

Jeremiah 51 in the SBITS2

Jeremiah 51 in the SBITS3

Jeremiah 51 in the SBITS4

Jeremiah 51 in the SBIUS

Jeremiah 51 in the SBIVS

Jeremiah 51 in the SBT

Jeremiah 51 in the SBT1E

Jeremiah 51 in the SCHL

Jeremiah 51 in the SNT

Jeremiah 51 in the SUSU

Jeremiah 51 in the SUSU2

Jeremiah 51 in the SYNO

Jeremiah 51 in the TBIAOTANT

Jeremiah 51 in the TBT1E

Jeremiah 51 in the TBT1E2

Jeremiah 51 in the TFTIP

Jeremiah 51 in the TFTU

Jeremiah 51 in the TGNTATF3T

Jeremiah 51 in the THAI

Jeremiah 51 in the TNFD

Jeremiah 51 in the TNT

Jeremiah 51 in the TNTIK

Jeremiah 51 in the TNTIL

Jeremiah 51 in the TNTIN

Jeremiah 51 in the TNTIP

Jeremiah 51 in the TNTIZ

Jeremiah 51 in the TOMA

Jeremiah 51 in the TTENT

Jeremiah 51 in the UBG

Jeremiah 51 in the UGV

Jeremiah 51 in the UGV2

Jeremiah 51 in the UGV3

Jeremiah 51 in the VBL

Jeremiah 51 in the VDCC

Jeremiah 51 in the YALU

Jeremiah 51 in the YAPE

Jeremiah 51 in the YBVTP

Jeremiah 51 in the ZBP