Jeremiah 8 (BOGWICC)

1 Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa. 2 Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka. 3 Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ ” 4 “Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:“ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso?Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso? 5 Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo?Iwo akangamira chinyengo;akukana kubwerera. 6 Ine ndinatchera khutu kumvetserakoma iwo sanayankhulepo zoona.Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake,nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’Aliyense akutsatira njira yakengati kavalo wothamangira nkhondo. 7 Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwanthawi yake mlengalenga.Koma nkhunda, namzeze ndi chingaluzimadziwa nthawi yonyamukira ulendo,koma anthu anga sadziwamalamulo a Yehova. 8 “ ‘Inu mukunena bwanji kuti,‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’Koma ndi alembi anuamene akulemba zabodza. 9 Anthu anzeru achita manyazi;athedwa nzeru ndipo agwidwa.Iwo anakana mawu a Yehova.Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji? 10 Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna enandipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse.Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba.Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,onse amachita zachinyengo. 11 Iwo amapoletsa zilonda za anthu angapamwamba chabenʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’pamene palibe mtendere. 12 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe;iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe.Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga,akutero Yehova. 13 “ ‘Ndidzatenga zokolola zawo,Sipadzakhalanso mphesa pa mpesakapena nkhuyu pa mkuyu,ndipo masamba ake adzawuma.Zinthu zimene ndinawapatsandidzawachotsera.’ ” 14 Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani?Tiyeni tonse pamodzitithawire ku mizinda yotetezedwandi kukafera kumeneko.Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa.Watipatsa madzi aululu kuti timwe,chifukwa tamuchimwira. 15 Tinkayembekezera mtenderekoma palibe chabwino chomwe chinachitika,tinkayembekezera kuchirakoma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha. 16 Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdanikukumveka kuchokera ku Dani;dziko lonse likunjenjemerachifukwa cha kulira kwa akavalowo.Akubwera kudzawononga dzikondi zonse zimene zili mʼmenemo.Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.” 17 Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza,ndipo zidzakulumani,” 18 Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,mtima wanga walefukiratu. 19 Imvani kulira kwa anthu angakuchokera ku dziko lakutali:akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni?Kodi mfumu yake sili kumeneko?” “Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema,ndi milungu yawo yachilendo?” 20 “Nthawi yokolola yapita,chilimwe chapita,koma sitinapulumuke.” 21 Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira. 22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?Kodi kumeneko kulibe singʼanga?Nanga chifukwa chiyani mabalaa anthu anga sanapole?

In Other Versions

Jeremiah 8 in the ANGEFD

Jeremiah 8 in the ANTPNG2D

Jeremiah 8 in the AS21

Jeremiah 8 in the BAGH

Jeremiah 8 in the BBPNG

Jeremiah 8 in the BBT1E

Jeremiah 8 in the BDS

Jeremiah 8 in the BEV

Jeremiah 8 in the BHAD

Jeremiah 8 in the BIB

Jeremiah 8 in the BLPT

Jeremiah 8 in the BNT

Jeremiah 8 in the BNTABOOT

Jeremiah 8 in the BNTLV

Jeremiah 8 in the BOATCB

Jeremiah 8 in the BOATCB2

Jeremiah 8 in the BOBCV

Jeremiah 8 in the BOCNT

Jeremiah 8 in the BOECS

Jeremiah 8 in the BOHCB

Jeremiah 8 in the BOHCV

Jeremiah 8 in the BOHLNT

Jeremiah 8 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 8 in the BOICB

Jeremiah 8 in the BOILNTAP

Jeremiah 8 in the BOITCV

Jeremiah 8 in the BOKCV

Jeremiah 8 in the BOKCV2

Jeremiah 8 in the BOKHWOG

Jeremiah 8 in the BOKSSV

Jeremiah 8 in the BOLCB

Jeremiah 8 in the BOLCB2

Jeremiah 8 in the BOMCV

Jeremiah 8 in the BONAV

Jeremiah 8 in the BONCB

Jeremiah 8 in the BONLT

Jeremiah 8 in the BONUT2

Jeremiah 8 in the BOPLNT

Jeremiah 8 in the BOSCB

Jeremiah 8 in the BOSNC

Jeremiah 8 in the BOTLNT

Jeremiah 8 in the BOVCB

Jeremiah 8 in the BOYCB

Jeremiah 8 in the BPBB

Jeremiah 8 in the BPH

Jeremiah 8 in the BSB

Jeremiah 8 in the CCB

Jeremiah 8 in the CUV

Jeremiah 8 in the CUVS

Jeremiah 8 in the DBT

Jeremiah 8 in the DGDNT

Jeremiah 8 in the DHNT

Jeremiah 8 in the DNT

Jeremiah 8 in the ELBE

Jeremiah 8 in the EMTV

Jeremiah 8 in the ESV

Jeremiah 8 in the FBV

Jeremiah 8 in the FEB

Jeremiah 8 in the GGMNT

Jeremiah 8 in the GNT

Jeremiah 8 in the HARY

Jeremiah 8 in the HNT

Jeremiah 8 in the IRVA

Jeremiah 8 in the IRVB

Jeremiah 8 in the IRVG

Jeremiah 8 in the IRVH

Jeremiah 8 in the IRVK

Jeremiah 8 in the IRVM

Jeremiah 8 in the IRVM2

Jeremiah 8 in the IRVO

Jeremiah 8 in the IRVP

Jeremiah 8 in the IRVT

Jeremiah 8 in the IRVT2

Jeremiah 8 in the IRVU

Jeremiah 8 in the ISVN

Jeremiah 8 in the JSNT

Jeremiah 8 in the KAPI

Jeremiah 8 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 8 in the KBV

Jeremiah 8 in the KJV

Jeremiah 8 in the KNFD

Jeremiah 8 in the LBA

Jeremiah 8 in the LBLA

Jeremiah 8 in the LNT

Jeremiah 8 in the LSV

Jeremiah 8 in the MAAL

Jeremiah 8 in the MBV

Jeremiah 8 in the MBV2

Jeremiah 8 in the MHNT

Jeremiah 8 in the MKNFD

Jeremiah 8 in the MNG

Jeremiah 8 in the MNT

Jeremiah 8 in the MNT2

Jeremiah 8 in the MRS1T

Jeremiah 8 in the NAA

Jeremiah 8 in the NASB

Jeremiah 8 in the NBLA

Jeremiah 8 in the NBS

Jeremiah 8 in the NBVTP

Jeremiah 8 in the NET2

Jeremiah 8 in the NIV11

Jeremiah 8 in the NNT

Jeremiah 8 in the NNT2

Jeremiah 8 in the NNT3

Jeremiah 8 in the PDDPT

Jeremiah 8 in the PFNT

Jeremiah 8 in the RMNT

Jeremiah 8 in the SBIAS

Jeremiah 8 in the SBIBS

Jeremiah 8 in the SBIBS2

Jeremiah 8 in the SBICS

Jeremiah 8 in the SBIDS

Jeremiah 8 in the SBIGS

Jeremiah 8 in the SBIHS

Jeremiah 8 in the SBIIS

Jeremiah 8 in the SBIIS2

Jeremiah 8 in the SBIIS3

Jeremiah 8 in the SBIKS

Jeremiah 8 in the SBIKS2

Jeremiah 8 in the SBIMS

Jeremiah 8 in the SBIOS

Jeremiah 8 in the SBIPS

Jeremiah 8 in the SBISS

Jeremiah 8 in the SBITS

Jeremiah 8 in the SBITS2

Jeremiah 8 in the SBITS3

Jeremiah 8 in the SBITS4

Jeremiah 8 in the SBIUS

Jeremiah 8 in the SBIVS

Jeremiah 8 in the SBT

Jeremiah 8 in the SBT1E

Jeremiah 8 in the SCHL

Jeremiah 8 in the SNT

Jeremiah 8 in the SUSU

Jeremiah 8 in the SUSU2

Jeremiah 8 in the SYNO

Jeremiah 8 in the TBIAOTANT

Jeremiah 8 in the TBT1E

Jeremiah 8 in the TBT1E2

Jeremiah 8 in the TFTIP

Jeremiah 8 in the TFTU

Jeremiah 8 in the TGNTATF3T

Jeremiah 8 in the THAI

Jeremiah 8 in the TNFD

Jeremiah 8 in the TNT

Jeremiah 8 in the TNTIK

Jeremiah 8 in the TNTIL

Jeremiah 8 in the TNTIN

Jeremiah 8 in the TNTIP

Jeremiah 8 in the TNTIZ

Jeremiah 8 in the TOMA

Jeremiah 8 in the TTENT

Jeremiah 8 in the UBG

Jeremiah 8 in the UGV

Jeremiah 8 in the UGV2

Jeremiah 8 in the UGV3

Jeremiah 8 in the VBL

Jeremiah 8 in the VDCC

Jeremiah 8 in the YALU

Jeremiah 8 in the YAPE

Jeremiah 8 in the YBVTP

Jeremiah 8 in the ZBP