John 17 (BOGWICC)

1 Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. 2 Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. 3 Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. 4 Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. 5 Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe. 6 “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. 7 Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. 8 Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. 9 Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10 Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11 Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12 Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe. 13 “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14 Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15 Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16 Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17 Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18 Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19 Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni. 20 “Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. 21 Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22 Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23 Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine. 24 “Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe. 25 “Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. 26 Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”

In Other Versions

John 17 in the ANGEFD

John 17 in the ANTPNG2D

John 17 in the AS21

John 17 in the BAGH

John 17 in the BBPNG

John 17 in the BBT1E

John 17 in the BDS

John 17 in the BEV

John 17 in the BHAD

John 17 in the BIB

John 17 in the BLPT

John 17 in the BNT

John 17 in the BNTABOOT

John 17 in the BNTLV

John 17 in the BOATCB

John 17 in the BOATCB2

John 17 in the BOBCV

John 17 in the BOCNT

John 17 in the BOECS

John 17 in the BOHCB

John 17 in the BOHCV

John 17 in the BOHLNT

John 17 in the BOHNTLTAL

John 17 in the BOICB

John 17 in the BOILNTAP

John 17 in the BOITCV

John 17 in the BOKCV

John 17 in the BOKCV2

John 17 in the BOKHWOG

John 17 in the BOKSSV

John 17 in the BOLCB

John 17 in the BOLCB2

John 17 in the BOMCV

John 17 in the BONAV

John 17 in the BONCB

John 17 in the BONLT

John 17 in the BONUT2

John 17 in the BOPLNT

John 17 in the BOSCB

John 17 in the BOSNC

John 17 in the BOTLNT

John 17 in the BOVCB

John 17 in the BOYCB

John 17 in the BPBB

John 17 in the BPH

John 17 in the BSB

John 17 in the CCB

John 17 in the CUV

John 17 in the CUVS

John 17 in the DBT

John 17 in the DGDNT

John 17 in the DHNT

John 17 in the DNT

John 17 in the ELBE

John 17 in the EMTV

John 17 in the ESV

John 17 in the FBV

John 17 in the FEB

John 17 in the GGMNT

John 17 in the GNT

John 17 in the HARY

John 17 in the HNT

John 17 in the IRVA

John 17 in the IRVB

John 17 in the IRVG

John 17 in the IRVH

John 17 in the IRVK

John 17 in the IRVM

John 17 in the IRVM2

John 17 in the IRVO

John 17 in the IRVP

John 17 in the IRVT

John 17 in the IRVT2

John 17 in the IRVU

John 17 in the ISVN

John 17 in the JSNT

John 17 in the KAPI

John 17 in the KBT1ETNIK

John 17 in the KBV

John 17 in the KJV

John 17 in the KNFD

John 17 in the LBA

John 17 in the LBLA

John 17 in the LNT

John 17 in the LSV

John 17 in the MAAL

John 17 in the MBV

John 17 in the MBV2

John 17 in the MHNT

John 17 in the MKNFD

John 17 in the MNG

John 17 in the MNT

John 17 in the MNT2

John 17 in the MRS1T

John 17 in the NAA

John 17 in the NASB

John 17 in the NBLA

John 17 in the NBS

John 17 in the NBVTP

John 17 in the NET2

John 17 in the NIV11

John 17 in the NNT

John 17 in the NNT2

John 17 in the NNT3

John 17 in the PDDPT

John 17 in the PFNT

John 17 in the RMNT

John 17 in the SBIAS

John 17 in the SBIBS

John 17 in the SBIBS2

John 17 in the SBICS

John 17 in the SBIDS

John 17 in the SBIGS

John 17 in the SBIHS

John 17 in the SBIIS

John 17 in the SBIIS2

John 17 in the SBIIS3

John 17 in the SBIKS

John 17 in the SBIKS2

John 17 in the SBIMS

John 17 in the SBIOS

John 17 in the SBIPS

John 17 in the SBISS

John 17 in the SBITS

John 17 in the SBITS2

John 17 in the SBITS3

John 17 in the SBITS4

John 17 in the SBIUS

John 17 in the SBIVS

John 17 in the SBT

John 17 in the SBT1E

John 17 in the SCHL

John 17 in the SNT

John 17 in the SUSU

John 17 in the SUSU2

John 17 in the SYNO

John 17 in the TBIAOTANT

John 17 in the TBT1E

John 17 in the TBT1E2

John 17 in the TFTIP

John 17 in the TFTU

John 17 in the TGNTATF3T

John 17 in the THAI

John 17 in the TNFD

John 17 in the TNT

John 17 in the TNTIK

John 17 in the TNTIL

John 17 in the TNTIN

John 17 in the TNTIP

John 17 in the TNTIZ

John 17 in the TOMA

John 17 in the TTENT

John 17 in the UBG

John 17 in the UGV

John 17 in the UGV2

John 17 in the UGV3

John 17 in the VBL

John 17 in the VDCC

John 17 in the YALU

John 17 in the YAPE

John 17 in the YBVTP

John 17 in the ZBP