John 6 (BOGWICC)

1 Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya), 2 ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala. 3 Kenaka Yesu anakwera pa phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. 4 Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi. 5 Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, “Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?” 6 Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita. 7 Filipo anamuyankha Iye kuti, “Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!” 8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati, 9 “Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?” 10 Yesu anati, “Awuzeni anthuwa akhale pansi.” Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000. 11 Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira. 12 Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.” 13 Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri. 14 Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, “Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi.” 15 Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuwumiriza kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri pa yekha. 16 Pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira ku nyanja, 17 kumene iwo analowa mʼbwato ndi kuyamba kuwoloka nyanja kupita ku Kaperenawo. Tsopano kunali kutada ndipo Yesu anali asanabwerere kwa iwo. 18 Mphepo yamphamvu inawomba ndipo nyanja inalusa. 19 Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha. 20 Koma Iye anawawuza kuti, “Ndine, musaope.” 21 Ndipo iwo analola kumutenga mʼbwatomo, nthawi yomweyo bwatolo linafika ku gombe la nyanja kumene ankapita. 22 Pa tsiku lotsatira gulu la anthu limene linatsala kumbali ina yanyanjayo linaona kuti panali bwato limodzi lokha, ndipo kuti Yesu sanalowe mʼbwatomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzirawo anapita okha. 23 Kenaka mabwato ena ochokera ku Tiberiya anafika pafupi ndi pamalo pamene anthu anadya buledi Ambuye atayamika. 24 Nthawi yomwe gulu la anthu linaona kuti Yesu kapena ophunzira ake sanali pamenepo, ilo linalowanso mʼmabwatowo ndi kupita ku Kaperenawo kukamufunafuna Yesu. 25 Atamupeza mbali ina ya nyanjayo, iwo anamufunsa Iye kuti, “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?” 26 Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta. 27 Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.” 28 Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?” 29 Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.” 30 Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani? 31 Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’ ” 32 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. 33 Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.” 34 Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.” 35 Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu. 36 Monga ndakuwuzani kale, ngakhale kuti mwandiona simukukhulupirirabe. 37 Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja. 38 Pakuti Ine ndinatsika kuchokera kumwamba osati kudzachita chifuniro changa koma cha Iye amene anandituma Ine. 39 Ndipo chifuniro cha Iye amene anandituma Ine nʼchakuti ndisatayepo ngakhale ndi mmodzi yemwe mwa onse amene Iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza. 40 Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.” 41 Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.” 42 Iwo anati, “Kodi uyu si Yesu, mwana wa Yosefe, amene abambo ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga Iyeyu akunena bwanji kuti, ‘Ine ndinatsika kuchokera kumwamba?’ ” 43 Yesu anayankha kuti, “Musangʼungʼudze pakati panu.” 44 Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 45 Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine. 46 Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate. 47 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha. 48 Ine ndine chakudya chamoyo. 49 Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa. 50 Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe. 51 Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.” 52 Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?” 53 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. 54 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 55 Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye. 57 Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58 Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.” 59 Iye ankanena izi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge mu Kaperenawo. 60 Pakumva izi ambiri a ophunzira ake anati, “Ichi ndi chiphunzitso chovuta. Angachilandire ndani?” 61 Pozindikira kuti ophunzira ake ankangʼungʼudza, Yesu anawafunsa kuti, “Kodi izi zikukukhumudwitsani? 62 Nanga mutaona Mwana wa Munthu akukwera kupita kumene Iye anali poyamba! 63 Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo. 64 Komabe alipo ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti Yesu ankadziwa kuyambira pachiyambi ena mwa iwo amene samakhulupirira ndi amene adzamupereka Iye. 65 Iye anapitiriza kunena kuti, “Ichi ndi chifukwa chake ndinakuwuzani kuti palibe wina angabwere kwa Ine pokhapokha Atate atamuthandiza.” 66 Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye. 67 Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, “Kodi inu mukufuna kuchokanso?” 68 Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha. 69 Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu.” 70 Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi Ine sindinakusankheni inu khumi ndi awiri? Komabe mmodzi wa inu ndi mdierekezi.” 71 (Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka).

In Other Versions

John 6 in the ANGEFD

John 6 in the ANTPNG2D

John 6 in the AS21

John 6 in the BAGH

John 6 in the BBPNG

John 6 in the BBT1E

John 6 in the BDS

John 6 in the BEV

John 6 in the BHAD

John 6 in the BIB

John 6 in the BLPT

John 6 in the BNT

John 6 in the BNTABOOT

John 6 in the BNTLV

John 6 in the BOATCB

John 6 in the BOATCB2

John 6 in the BOBCV

John 6 in the BOCNT

John 6 in the BOECS

John 6 in the BOHCB

John 6 in the BOHCV

John 6 in the BOHLNT

John 6 in the BOHNTLTAL

John 6 in the BOICB

John 6 in the BOILNTAP

John 6 in the BOITCV

John 6 in the BOKCV

John 6 in the BOKCV2

John 6 in the BOKHWOG

John 6 in the BOKSSV

John 6 in the BOLCB

John 6 in the BOLCB2

John 6 in the BOMCV

John 6 in the BONAV

John 6 in the BONCB

John 6 in the BONLT

John 6 in the BONUT2

John 6 in the BOPLNT

John 6 in the BOSCB

John 6 in the BOSNC

John 6 in the BOTLNT

John 6 in the BOVCB

John 6 in the BOYCB

John 6 in the BPBB

John 6 in the BPH

John 6 in the BSB

John 6 in the CCB

John 6 in the CUV

John 6 in the CUVS

John 6 in the DBT

John 6 in the DGDNT

John 6 in the DHNT

John 6 in the DNT

John 6 in the ELBE

John 6 in the EMTV

John 6 in the ESV

John 6 in the FBV

John 6 in the FEB

John 6 in the GGMNT

John 6 in the GNT

John 6 in the HARY

John 6 in the HNT

John 6 in the IRVA

John 6 in the IRVB

John 6 in the IRVG

John 6 in the IRVH

John 6 in the IRVK

John 6 in the IRVM

John 6 in the IRVM2

John 6 in the IRVO

John 6 in the IRVP

John 6 in the IRVT

John 6 in the IRVT2

John 6 in the IRVU

John 6 in the ISVN

John 6 in the JSNT

John 6 in the KAPI

John 6 in the KBT1ETNIK

John 6 in the KBV

John 6 in the KJV

John 6 in the KNFD

John 6 in the LBA

John 6 in the LBLA

John 6 in the LNT

John 6 in the LSV

John 6 in the MAAL

John 6 in the MBV

John 6 in the MBV2

John 6 in the MHNT

John 6 in the MKNFD

John 6 in the MNG

John 6 in the MNT

John 6 in the MNT2

John 6 in the MRS1T

John 6 in the NAA

John 6 in the NASB

John 6 in the NBLA

John 6 in the NBS

John 6 in the NBVTP

John 6 in the NET2

John 6 in the NIV11

John 6 in the NNT

John 6 in the NNT2

John 6 in the NNT3

John 6 in the PDDPT

John 6 in the PFNT

John 6 in the RMNT

John 6 in the SBIAS

John 6 in the SBIBS

John 6 in the SBIBS2

John 6 in the SBICS

John 6 in the SBIDS

John 6 in the SBIGS

John 6 in the SBIHS

John 6 in the SBIIS

John 6 in the SBIIS2

John 6 in the SBIIS3

John 6 in the SBIKS

John 6 in the SBIKS2

John 6 in the SBIMS

John 6 in the SBIOS

John 6 in the SBIPS

John 6 in the SBISS

John 6 in the SBITS

John 6 in the SBITS2

John 6 in the SBITS3

John 6 in the SBITS4

John 6 in the SBIUS

John 6 in the SBIVS

John 6 in the SBT

John 6 in the SBT1E

John 6 in the SCHL

John 6 in the SNT

John 6 in the SUSU

John 6 in the SUSU2

John 6 in the SYNO

John 6 in the TBIAOTANT

John 6 in the TBT1E

John 6 in the TBT1E2

John 6 in the TFTIP

John 6 in the TFTU

John 6 in the TGNTATF3T

John 6 in the THAI

John 6 in the TNFD

John 6 in the TNT

John 6 in the TNTIK

John 6 in the TNTIL

John 6 in the TNTIN

John 6 in the TNTIP

John 6 in the TNTIZ

John 6 in the TOMA

John 6 in the TTENT

John 6 in the UBG

John 6 in the UGV

John 6 in the UGV2

John 6 in the UGV3

John 6 in the VBL

John 6 in the VDCC

John 6 in the YALU

John 6 in the YAPE

John 6 in the YBVTP

John 6 in the ZBP