Lamentations 3 (BOGWICC)
1 Ine ndine munthu amene ndaona masautsondi ndodo ya ukali wake. 2 Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsamu mdima osati mʼkuwala; 3 zoonadi anandikantha ndi dzanja lakemobwerezabwereza tsiku lonse. 4 Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga,ndipo waphwanya mafupa anga. 5 Wandizinga ndi kundizungulirandi zowawa ndi zolemetsa. 6 Wandikhazika mu mdimangati amene anafa kale. 7 Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe,wandimanga ndi maunyolo. 8 Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo,amakana pemphero langa. 9 Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema;ndipo wakhotetsa tinjira tanga. 10 Wandidikirira ngati chimbalangondo,wandibisalira ngati mkango. 11 Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba,ndipo wandisiya wopanda thandizo. 12 Wakoka uta wakendipo walunjikitsa mivi yake pa ine. 13 Walasa mtima wangandi mivi ya mʼphodo mwake. 14 Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse;amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse. 15 Wandidyetsa zowawandipo wandimwetsa ndulu. 16 Wathyola mano anga ndi miyala;wandiviviniza mʼfumbi; 17 Wandichotsera mtendere;ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani. 18 Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachokandi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.” 19 Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala,zili ngati zowawa ndi ndulu. 20 Ine ndikuzikumbukira bwino izi,ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga. 21 Komabe ndimakumbukira zimenezi,nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo. 22 Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu,ndi chifundo chake ndi chosatha. 23 Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse;kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu. 24 Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse;motero ndimamuyembekezera.” 25 Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo; 26 nʼkwabwino kudikira chipulumutso chaYehova modekha. 27 Nʼkwabwino kuti munthu asenze golipamene ali wamngʼono. 28 Akhale chete pa yekha,chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo. 29 Abise nkhope yake mʼfumbimwina chiyembekezo nʼkukhalapobe. 30 Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye,ndipo amuchititse manyazi. 31 Chifukwa Ambuye satayiratuanthu nthawi zonse. 32 Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo,chifukwa chikondi chake ndi chosatha. 33 Pakuti sabweretsa masautso mwadala,kapena zowawa kwa ana a anthu. 34 Kuphwanya ndi phazia mʼndende onse a mʼdziko, 35 kukaniza munthu ufulu wakepamaso pa Wammwambamwamba, 36 kumana munthu chiweruzo cholungama—kodi Ambuye saona zonsezi? 37 Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitikangati Ambuye sanavomereze? 38 Kodi zovuta ndi zabwino sizitulukamʼkamwa mwa Wammwambamwamba? 39 Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaulaakalangidwa chifukwa cha machimo ake? 40 Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu,ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova. 41 Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athukwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti: 42 “Ife tachimwa ndi kuwukirandipo inu simunakhululuke. 43 “Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipomwatitha mopanda chifundo. 44 Mwadzikuta mu mtambokotero mapemphero athu sakukufikani. 45 Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalalapakati pa mitundu ya anthu. 46 “Adani anthu atitsekulira pakamwa. 47 Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje,tapasuka ndi kuwonongedwa.” 48 Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwechifukwa anthu anga akuwonongedwa. 49 Misozi idzatsika kosalekeza,ndipo sidzasiya, 50 mpaka Yehova ayangʼane pansikuchokera kumwamba ndi kuona. 51 Mtima wanga ukupweteka poona zimenezichifukwa cha akazi onse a mu mzinda. 52 Akundisaka ngati mbalame,amene anali adani anga, popanda chifukwa. 53 Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenjendi kundiponya miyala; 54 madzi anamiza mutu wangandipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira. 55 Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova,kuchokera mʼdzenje lozama. 56 Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimverekulira kwanga kopempha thandizo.” 57 Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani,ndipo munati, “Usaope.” 58 Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga;munapulumutsa moyo wanga. 59 Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira.Mundiweruzire ndinu! 60 Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo,chiwembu chawo chonse pa ine. 61 Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo,chiwembu chawo chonse pa ine, 62 manongʼonongʼo a adani angaondiwukira ine tsiku lonse. 63 Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira,akundinyoza mu nyimbo zawo. 64 Inu Yehova, muwabwezere chowayenera,chifukwa cha zimene manja awo achita. 65 Phimbani mitima yawo,ndipo matemberero anu akhale pa iwo! 66 Muwalondole mwaukali ndipomuwawonongeretu pa dziko lapansi.
In Other Versions
Lamentations 3 in the ANTPNG2D
Lamentations 3 in the BNTABOOT
Lamentations 3 in the BOHNTLTAL
Lamentations 3 in the BOILNTAP
Lamentations 3 in the KBT1ETNIK
Lamentations 3 in the TBIAOTANT