Matthew 18 (BOGWICC)

1 Pa nthawi imeneyo ophunzira anabwera kwa Yesu ndipo anamufunsa kuti, “Wamkulu woposa onse ndani mu ufumu wakumwamba?” 2 Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. 3 Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. 4 Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba. 5 Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine. 6 “Koma ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana awa, amene akhulupirira Ine, kuti achimwe, kukanakhala bwino kuti iye amangiriridwe chimwala chachikulu mʼkhosi mwake ndi kumizidwa pansi pa nyanja. 7 Tsoka dziko lapansi chifukwa cha zinthu zimene ziyenera kubwera, koma tsoka kwa munthu amene abweretsa zotere! 8 Ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kulowa mʼmoyo wosatha wolumala kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri kapena mapazi awiri ndi kukaponyedwa ku moto wosatha. 9 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kuti ukalowe ku moyo wosatha ndi diso limodzi kuposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kukaponyedwa ku moto wa gehena.” 10 “Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.” 11 (Mwana wa Munthu anabwera kudzapulumutsa chimene chinatayika). 12 “Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo? 13 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti akayipeza amasangalala kwambiri chifukwa cha nkhosa imodziyo kuposa nkhosa 99 zimene sizinasochere. 14 Chimodzimodzinso Atate anu akumwamba safuna kuti mmodzi wa anawa atayike. 15 “Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo. 16 Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, ‘kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.’ 17 Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho. 18 “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba. 19 “Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani. 20 Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.” 21 Kenaka Petro anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Ambuye, kodi mʼbale wanga akandichimwira ndimukhululukire kokwanira kangati? Mpaka kasanu nʼkawiri?” 22 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza iwe kuti osati kasanu nʼkawiri, koma ka 70 kuchulukitsa ndi kasanu nʼkawiri. 23 “Nʼchifukwa chake, ufumu wakumwamba ukufanana ndi mfumu imene inafuna kuti antchito ake abweze ngongole. 24 Atangoyamba kulandira, anamubweretsa munthu kwa iye amene anakongola ndalama 10,000. 25 Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo. 26 “Wantchitoyo anagwada pamaso pake namupempha iye kuti, ‘Lezereni mtima ndipo ndidzabweza zonse.’ 27 Bwana wakeyo anamuchitira chifundo, namukhululukira ngongoleyo ndipo anamulola apite. 28 “Koma wantchito uja atatuluka, anakumana ndi wantchito mnzake amene anakongola kwa iye madinari 100. Anamugwira, nayamba kumukanyanga pa khosi, namuwumiriza nati, ‘Bwezere zimene unakongola kwa ine!’ 29 “Wantchito mnzakeyo anagwada namupempha iye kuti, ‘Lezere mtima ine, ndipo ndidzakubwezera.’ 30 “Koma iye anakana. Mʼmalo mwake, anachoka nakamumangitsa kufikira atabweza ngongoleyo. 31 Pamene antchito ena anaona zomwe zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita nakawuza bwana wawo zonse zimene zinachitika. 32 “Pamenepo bwanayo anayitana wantchitoyo nati, ‘Iwe wantchito woyipa mtima, ndinakukhululukira ngongole yako yonse chifukwa unandipempha. 33 Kodi iwe sukanamuchitira chifundo wantchito mnzako monga momwe ine ndinakuchitira iwe?’ 34 Ndi mkwiyo, bwana wakeyo anamupereka kwa oyangʼanira ndende kuti amuzuze mpaka atabweza zonse zimene anakongola. 35 “Umu ndi mmene Atate anga akumwamba adzachitira ndi aliyense wa inu ngati simukhululukira mʼbale wanu ndi mtima wonse.”

In Other Versions

Matthew 18 in the ANGEFD

Matthew 18 in the ANTPNG2D

Matthew 18 in the AS21

Matthew 18 in the BAGH

Matthew 18 in the BBPNG

Matthew 18 in the BBT1E

Matthew 18 in the BDS

Matthew 18 in the BEV

Matthew 18 in the BHAD

Matthew 18 in the BIB

Matthew 18 in the BLPT

Matthew 18 in the BNT

Matthew 18 in the BNTABOOT

Matthew 18 in the BNTLV

Matthew 18 in the BOATCB

Matthew 18 in the BOATCB2

Matthew 18 in the BOBCV

Matthew 18 in the BOCNT

Matthew 18 in the BOECS

Matthew 18 in the BOHCB

Matthew 18 in the BOHCV

Matthew 18 in the BOHLNT

Matthew 18 in the BOHNTLTAL

Matthew 18 in the BOICB

Matthew 18 in the BOILNTAP

Matthew 18 in the BOITCV

Matthew 18 in the BOKCV

Matthew 18 in the BOKCV2

Matthew 18 in the BOKHWOG

Matthew 18 in the BOKSSV

Matthew 18 in the BOLCB

Matthew 18 in the BOLCB2

Matthew 18 in the BOMCV

Matthew 18 in the BONAV

Matthew 18 in the BONCB

Matthew 18 in the BONLT

Matthew 18 in the BONUT2

Matthew 18 in the BOPLNT

Matthew 18 in the BOSCB

Matthew 18 in the BOSNC

Matthew 18 in the BOTLNT

Matthew 18 in the BOVCB

Matthew 18 in the BOYCB

Matthew 18 in the BPBB

Matthew 18 in the BPH

Matthew 18 in the BSB

Matthew 18 in the CCB

Matthew 18 in the CUV

Matthew 18 in the CUVS

Matthew 18 in the DBT

Matthew 18 in the DGDNT

Matthew 18 in the DHNT

Matthew 18 in the DNT

Matthew 18 in the ELBE

Matthew 18 in the EMTV

Matthew 18 in the ESV

Matthew 18 in the FBV

Matthew 18 in the FEB

Matthew 18 in the GGMNT

Matthew 18 in the GNT

Matthew 18 in the HARY

Matthew 18 in the HNT

Matthew 18 in the IRVA

Matthew 18 in the IRVB

Matthew 18 in the IRVG

Matthew 18 in the IRVH

Matthew 18 in the IRVK

Matthew 18 in the IRVM

Matthew 18 in the IRVM2

Matthew 18 in the IRVO

Matthew 18 in the IRVP

Matthew 18 in the IRVT

Matthew 18 in the IRVT2

Matthew 18 in the IRVU

Matthew 18 in the ISVN

Matthew 18 in the JSNT

Matthew 18 in the KAPI

Matthew 18 in the KBT1ETNIK

Matthew 18 in the KBV

Matthew 18 in the KJV

Matthew 18 in the KNFD

Matthew 18 in the LBA

Matthew 18 in the LBLA

Matthew 18 in the LNT

Matthew 18 in the LSV

Matthew 18 in the MAAL

Matthew 18 in the MBV

Matthew 18 in the MBV2

Matthew 18 in the MHNT

Matthew 18 in the MKNFD

Matthew 18 in the MNG

Matthew 18 in the MNT

Matthew 18 in the MNT2

Matthew 18 in the MRS1T

Matthew 18 in the NAA

Matthew 18 in the NASB

Matthew 18 in the NBLA

Matthew 18 in the NBS

Matthew 18 in the NBVTP

Matthew 18 in the NET2

Matthew 18 in the NIV11

Matthew 18 in the NNT

Matthew 18 in the NNT2

Matthew 18 in the NNT3

Matthew 18 in the PDDPT

Matthew 18 in the PFNT

Matthew 18 in the RMNT

Matthew 18 in the SBIAS

Matthew 18 in the SBIBS

Matthew 18 in the SBIBS2

Matthew 18 in the SBICS

Matthew 18 in the SBIDS

Matthew 18 in the SBIGS

Matthew 18 in the SBIHS

Matthew 18 in the SBIIS

Matthew 18 in the SBIIS2

Matthew 18 in the SBIIS3

Matthew 18 in the SBIKS

Matthew 18 in the SBIKS2

Matthew 18 in the SBIMS

Matthew 18 in the SBIOS

Matthew 18 in the SBIPS

Matthew 18 in the SBISS

Matthew 18 in the SBITS

Matthew 18 in the SBITS2

Matthew 18 in the SBITS3

Matthew 18 in the SBITS4

Matthew 18 in the SBIUS

Matthew 18 in the SBIVS

Matthew 18 in the SBT

Matthew 18 in the SBT1E

Matthew 18 in the SCHL

Matthew 18 in the SNT

Matthew 18 in the SUSU

Matthew 18 in the SUSU2

Matthew 18 in the SYNO

Matthew 18 in the TBIAOTANT

Matthew 18 in the TBT1E

Matthew 18 in the TBT1E2

Matthew 18 in the TFTIP

Matthew 18 in the TFTU

Matthew 18 in the TGNTATF3T

Matthew 18 in the THAI

Matthew 18 in the TNFD

Matthew 18 in the TNT

Matthew 18 in the TNTIK

Matthew 18 in the TNTIL

Matthew 18 in the TNTIN

Matthew 18 in the TNTIP

Matthew 18 in the TNTIZ

Matthew 18 in the TOMA

Matthew 18 in the TTENT

Matthew 18 in the UBG

Matthew 18 in the UGV

Matthew 18 in the UGV2

Matthew 18 in the UGV3

Matthew 18 in the VBL

Matthew 18 in the VDCC

Matthew 18 in the YALU

Matthew 18 in the YAPE

Matthew 18 in the YBVTP

Matthew 18 in the ZBP