Psalms 105 (BOGWICC)

1 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita. 2 Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa. 3 Munyadire dzina lake loyera;mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere. 4 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;funafunani nkhope yake nthawi yonse. 5 Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka, 6 inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,inu ana a Yakobo, osankhika ake. 7 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi. 8 Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,mawu amene analamula kwa mibado yonse, 9 pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,lumbiro limene analumbira kwa Isake. 10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,kwa Israeli monga pangano lamuyaya: 11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaaningati gawo la cholowa chako.” 12 Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero,ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo, 13 ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina,kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina. 14 Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza;anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo: 15 “Musakhudze odzozedwa anga;musachitire choyipa aneneri anga.” 16 Iye anabweretsa njala pa dzikondipo anawononga chakudya chonse; 17 Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo,Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo. 18 Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza,khosi lake analiyika mʼzitsulo, 19 mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa,mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona. 20 Mfumu inatuma munthu kukamumasula,wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo. 21 Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake,wolamulira zonse zimene iye anali nazo, 22 kulangiza ana a mfumu monga ankafunirandi kuphunzitsa nzeru akuluakulu. 23 Tsono Israeli analowa mu Igupto;Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu. 24 Yehova anachulukitsa anthu ake;ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo; 25 amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake,kukonzera chiwembu atumiki ake. 26 Yehova anatuma Mose mtumiki wake,ndi Aaroni amene Iye anamusankha. 27 Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo,zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu. 28 Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima.Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova. 29 Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi,kuchititsa kuti nsomba zawo zife. 30 Dziko lawo linadzaza ndi achuleamene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo. 31 Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochulukandi nsabwe mʼdziko lawo lonse. 32 Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala,ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse; 33 Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu,nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo. 34 Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera,ziwala zosawerengeka; 35 zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo,zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo. 36 Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo,zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse. 37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka. 38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo. 39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,ndi moto owawunikira usiku. 40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinzirindipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba. 41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;ngati mtsinje anayenda mʼchipululu. 42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limenelinaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake. 43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,osankhika ake akufuwula mwachimwemwe; 44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu inandipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira, 45 kuti iwo asunge malangizo akendi kutsatira malamulo ake. Tamandani Yehova.

In Other Versions

Psalms 105 in the ANGEFD

Psalms 105 in the ANTPNG2D

Psalms 105 in the AS21

Psalms 105 in the BAGH

Psalms 105 in the BBPNG

Psalms 105 in the BBT1E

Psalms 105 in the BDS

Psalms 105 in the BEV

Psalms 105 in the BHAD

Psalms 105 in the BIB

Psalms 105 in the BLPT

Psalms 105 in the BNT

Psalms 105 in the BNTABOOT

Psalms 105 in the BNTLV

Psalms 105 in the BOATCB

Psalms 105 in the BOATCB2

Psalms 105 in the BOBCV

Psalms 105 in the BOCNT

Psalms 105 in the BOECS

Psalms 105 in the BOHCB

Psalms 105 in the BOHCV

Psalms 105 in the BOHLNT

Psalms 105 in the BOHNTLTAL

Psalms 105 in the BOICB

Psalms 105 in the BOILNTAP

Psalms 105 in the BOITCV

Psalms 105 in the BOKCV

Psalms 105 in the BOKCV2

Psalms 105 in the BOKHWOG

Psalms 105 in the BOKSSV

Psalms 105 in the BOLCB

Psalms 105 in the BOLCB2

Psalms 105 in the BOMCV

Psalms 105 in the BONAV

Psalms 105 in the BONCB

Psalms 105 in the BONLT

Psalms 105 in the BONUT2

Psalms 105 in the BOPLNT

Psalms 105 in the BOSCB

Psalms 105 in the BOSNC

Psalms 105 in the BOTLNT

Psalms 105 in the BOVCB

Psalms 105 in the BOYCB

Psalms 105 in the BPBB

Psalms 105 in the BPH

Psalms 105 in the BSB

Psalms 105 in the CCB

Psalms 105 in the CUV

Psalms 105 in the CUVS

Psalms 105 in the DBT

Psalms 105 in the DGDNT

Psalms 105 in the DHNT

Psalms 105 in the DNT

Psalms 105 in the ELBE

Psalms 105 in the EMTV

Psalms 105 in the ESV

Psalms 105 in the FBV

Psalms 105 in the FEB

Psalms 105 in the GGMNT

Psalms 105 in the GNT

Psalms 105 in the HARY

Psalms 105 in the HNT

Psalms 105 in the IRVA

Psalms 105 in the IRVB

Psalms 105 in the IRVG

Psalms 105 in the IRVH

Psalms 105 in the IRVK

Psalms 105 in the IRVM

Psalms 105 in the IRVM2

Psalms 105 in the IRVO

Psalms 105 in the IRVP

Psalms 105 in the IRVT

Psalms 105 in the IRVT2

Psalms 105 in the IRVU

Psalms 105 in the ISVN

Psalms 105 in the JSNT

Psalms 105 in the KAPI

Psalms 105 in the KBT1ETNIK

Psalms 105 in the KBV

Psalms 105 in the KJV

Psalms 105 in the KNFD

Psalms 105 in the LBA

Psalms 105 in the LBLA

Psalms 105 in the LNT

Psalms 105 in the LSV

Psalms 105 in the MAAL

Psalms 105 in the MBV

Psalms 105 in the MBV2

Psalms 105 in the MHNT

Psalms 105 in the MKNFD

Psalms 105 in the MNG

Psalms 105 in the MNT

Psalms 105 in the MNT2

Psalms 105 in the MRS1T

Psalms 105 in the NAA

Psalms 105 in the NASB

Psalms 105 in the NBLA

Psalms 105 in the NBS

Psalms 105 in the NBVTP

Psalms 105 in the NET2

Psalms 105 in the NIV11

Psalms 105 in the NNT

Psalms 105 in the NNT2

Psalms 105 in the NNT3

Psalms 105 in the PDDPT

Psalms 105 in the PFNT

Psalms 105 in the RMNT

Psalms 105 in the SBIAS

Psalms 105 in the SBIBS

Psalms 105 in the SBIBS2

Psalms 105 in the SBICS

Psalms 105 in the SBIDS

Psalms 105 in the SBIGS

Psalms 105 in the SBIHS

Psalms 105 in the SBIIS

Psalms 105 in the SBIIS2

Psalms 105 in the SBIIS3

Psalms 105 in the SBIKS

Psalms 105 in the SBIKS2

Psalms 105 in the SBIMS

Psalms 105 in the SBIOS

Psalms 105 in the SBIPS

Psalms 105 in the SBISS

Psalms 105 in the SBITS

Psalms 105 in the SBITS2

Psalms 105 in the SBITS3

Psalms 105 in the SBITS4

Psalms 105 in the SBIUS

Psalms 105 in the SBIVS

Psalms 105 in the SBT

Psalms 105 in the SBT1E

Psalms 105 in the SCHL

Psalms 105 in the SNT

Psalms 105 in the SUSU

Psalms 105 in the SUSU2

Psalms 105 in the SYNO

Psalms 105 in the TBIAOTANT

Psalms 105 in the TBT1E

Psalms 105 in the TBT1E2

Psalms 105 in the TFTIP

Psalms 105 in the TFTU

Psalms 105 in the TGNTATF3T

Psalms 105 in the THAI

Psalms 105 in the TNFD

Psalms 105 in the TNT

Psalms 105 in the TNTIK

Psalms 105 in the TNTIL

Psalms 105 in the TNTIN

Psalms 105 in the TNTIP

Psalms 105 in the TNTIZ

Psalms 105 in the TOMA

Psalms 105 in the TTENT

Psalms 105 in the UBG

Psalms 105 in the UGV

Psalms 105 in the UGV2

Psalms 105 in the UGV3

Psalms 105 in the VBL

Psalms 105 in the VDCC

Psalms 105 in the YALU

Psalms 105 in the YAPE

Psalms 105 in the YBVTP

Psalms 105 in the ZBP