Psalms 68 (BOGWICC)

undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 1 Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;adani ake athawe pamaso pake. 2 Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.Monga phula limasungunukira pa moto,oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu. 3 Koma olungama asangalalendi kukondwera pamaso pa Mulungu;iwo akondwere ndi kusangalala. 4 Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake. 5 Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera. 6 Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi. 7 Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,pamene munayenda kudutsa chipululu, 8 dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli. 9 Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka. 10 Anthu anu anakhala mʼmenemondipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu. 11 Ambuye analengeza mawu,ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa; 12 “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro;mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo. 13 Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto,mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva,nthenga zake ndi golide wonyezimira.” 14 Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko,zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni. 15 Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero;mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri. 16 Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri,pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira,kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya? 17 Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka,ndi miyandamiyanda;Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika. 18 Pamene Inu munakwera mmwamba,munatsogolera a mʼndende ambiri;munalandira mphatso kuchokera kwa anthu,ngakhale kuchokera kwa owukira,kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko. 19 Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathuamene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu. 20 Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa. 21 Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo. 22 Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani;ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama. 23 Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu,pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.” 24 Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu;mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika. 25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo;pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini. 26 Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu;tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli. 27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera,pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda,ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali. 28 Kungani mphamvu zanu Mulungu;tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba. 29 Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso. 30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo. 31 Nthumwi zidzachokera ku Igupto;Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu. 32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansiimbirani Ambuye matamando. Sela 33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwambaamene amabangula ndi mawu amphamvu. 34 Lengezani za mphamvu za Mulungu,amene ulemerero wake uli pa Israeliamene mphamvu zake zili mʼmitambo. 35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake. Matamando akhale kwa Mulungu!

In Other Versions

Psalms 68 in the ANGEFD

Psalms 68 in the ANTPNG2D

Psalms 68 in the AS21

Psalms 68 in the BAGH

Psalms 68 in the BBPNG

Psalms 68 in the BBT1E

Psalms 68 in the BDS

Psalms 68 in the BEV

Psalms 68 in the BHAD

Psalms 68 in the BIB

Psalms 68 in the BLPT

Psalms 68 in the BNT

Psalms 68 in the BNTABOOT

Psalms 68 in the BNTLV

Psalms 68 in the BOATCB

Psalms 68 in the BOATCB2

Psalms 68 in the BOBCV

Psalms 68 in the BOCNT

Psalms 68 in the BOECS

Psalms 68 in the BOHCB

Psalms 68 in the BOHCV

Psalms 68 in the BOHLNT

Psalms 68 in the BOHNTLTAL

Psalms 68 in the BOICB

Psalms 68 in the BOILNTAP

Psalms 68 in the BOITCV

Psalms 68 in the BOKCV

Psalms 68 in the BOKCV2

Psalms 68 in the BOKHWOG

Psalms 68 in the BOKSSV

Psalms 68 in the BOLCB

Psalms 68 in the BOLCB2

Psalms 68 in the BOMCV

Psalms 68 in the BONAV

Psalms 68 in the BONCB

Psalms 68 in the BONLT

Psalms 68 in the BONUT2

Psalms 68 in the BOPLNT

Psalms 68 in the BOSCB

Psalms 68 in the BOSNC

Psalms 68 in the BOTLNT

Psalms 68 in the BOVCB

Psalms 68 in the BOYCB

Psalms 68 in the BPBB

Psalms 68 in the BPH

Psalms 68 in the BSB

Psalms 68 in the CCB

Psalms 68 in the CUV

Psalms 68 in the CUVS

Psalms 68 in the DBT

Psalms 68 in the DGDNT

Psalms 68 in the DHNT

Psalms 68 in the DNT

Psalms 68 in the ELBE

Psalms 68 in the EMTV

Psalms 68 in the ESV

Psalms 68 in the FBV

Psalms 68 in the FEB

Psalms 68 in the GGMNT

Psalms 68 in the GNT

Psalms 68 in the HARY

Psalms 68 in the HNT

Psalms 68 in the IRVA

Psalms 68 in the IRVB

Psalms 68 in the IRVG

Psalms 68 in the IRVH

Psalms 68 in the IRVK

Psalms 68 in the IRVM

Psalms 68 in the IRVM2

Psalms 68 in the IRVO

Psalms 68 in the IRVP

Psalms 68 in the IRVT

Psalms 68 in the IRVT2

Psalms 68 in the IRVU

Psalms 68 in the ISVN

Psalms 68 in the JSNT

Psalms 68 in the KAPI

Psalms 68 in the KBT1ETNIK

Psalms 68 in the KBV

Psalms 68 in the KJV

Psalms 68 in the KNFD

Psalms 68 in the LBA

Psalms 68 in the LBLA

Psalms 68 in the LNT

Psalms 68 in the LSV

Psalms 68 in the MAAL

Psalms 68 in the MBV

Psalms 68 in the MBV2

Psalms 68 in the MHNT

Psalms 68 in the MKNFD

Psalms 68 in the MNG

Psalms 68 in the MNT

Psalms 68 in the MNT2

Psalms 68 in the MRS1T

Psalms 68 in the NAA

Psalms 68 in the NASB

Psalms 68 in the NBLA

Psalms 68 in the NBS

Psalms 68 in the NBVTP

Psalms 68 in the NET2

Psalms 68 in the NIV11

Psalms 68 in the NNT

Psalms 68 in the NNT2

Psalms 68 in the NNT3

Psalms 68 in the PDDPT

Psalms 68 in the PFNT

Psalms 68 in the RMNT

Psalms 68 in the SBIAS

Psalms 68 in the SBIBS

Psalms 68 in the SBIBS2

Psalms 68 in the SBICS

Psalms 68 in the SBIDS

Psalms 68 in the SBIGS

Psalms 68 in the SBIHS

Psalms 68 in the SBIIS

Psalms 68 in the SBIIS2

Psalms 68 in the SBIIS3

Psalms 68 in the SBIKS

Psalms 68 in the SBIKS2

Psalms 68 in the SBIMS

Psalms 68 in the SBIOS

Psalms 68 in the SBIPS

Psalms 68 in the SBISS

Psalms 68 in the SBITS

Psalms 68 in the SBITS2

Psalms 68 in the SBITS3

Psalms 68 in the SBITS4

Psalms 68 in the SBIUS

Psalms 68 in the SBIVS

Psalms 68 in the SBT

Psalms 68 in the SBT1E

Psalms 68 in the SCHL

Psalms 68 in the SNT

Psalms 68 in the SUSU

Psalms 68 in the SUSU2

Psalms 68 in the SYNO

Psalms 68 in the TBIAOTANT

Psalms 68 in the TBT1E

Psalms 68 in the TBT1E2

Psalms 68 in the TFTIP

Psalms 68 in the TFTU

Psalms 68 in the TGNTATF3T

Psalms 68 in the THAI

Psalms 68 in the TNFD

Psalms 68 in the TNT

Psalms 68 in the TNTIK

Psalms 68 in the TNTIL

Psalms 68 in the TNTIN

Psalms 68 in the TNTIP

Psalms 68 in the TNTIZ

Psalms 68 in the TOMA

Psalms 68 in the TTENT

Psalms 68 in the UBG

Psalms 68 in the UGV

Psalms 68 in the UGV2

Psalms 68 in the UGV3

Psalms 68 in the VBL

Psalms 68 in the VDCC

Psalms 68 in the YALU

Psalms 68 in the YAPE

Psalms 68 in the YBVTP

Psalms 68 in the ZBP