Romans 11 (BOGWICC)

1 Ine ndikufunsa kuti kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Inenso ndine Mwisraeli, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini. 2 Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati, 3 “Ambuye, anthuwa apha aneneri anu ndi kugwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha wamoyo ndipo akufuna kundipha?” 4 Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.” 5 Chimodzimodzinso lero lino, alipo Aisraeli pangʼono osankhidwa mwachisomo. 6 Ndipo ngati ndi mwachisomo, sikungakhalenso mwa ntchito. Ngati zikanatero, chisomo sichikanakhalanso chisomo ayi. 7 Nʼchiyani tsopano? Chimene Aisraeli anachifuna ndi mtima wonse sanachipeze koma osankhidwawo anachipeza. Enawo anawumitsidwa mtima 8 monga kwalembedwa kuti,“Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu,maso osatha kupenya;makutu osatha kumvampaka lero lino.” 9 Ndipo Davide akuti,“Maphwando awo asanduke msampha ndi diwa lowakolandi chopunthwitsa kuti alandire chilango. 10 Maso awo atsekedwe kuti asaone,ndi misana yawo ikhale yokhota nthawi zonse.” 11 Ine ndikufunsanso kuti, kodi iwo anapunthwa ndi kugwa kotheratu? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo, chipulumutso chinafika kwa a mitundu ina kuti Aisraeli achite nsanje. 12 Koma ngati kulakwa kwawo kwapindulitsa dziko lapansi ndi kulephera kwawo kwapindulitsa a mitundu ina, nanga kudzakhala kupindula kwakukulu chotani iwo akadzabwera chonse! 13 Ine ndikuyankhula kwa inu a mitundu ina monga ine ndili mtumwi wa kwa a mitundu ina ndipo ndimawunyadira utumiki wangawu. 14 Ine cholinga changa nʼchakuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga kuti ena mwa iwo apulumutsidwe. 15 Pakuti ngati kukanidwa kwawo kunayanjanitsa anthu a dziko lapansi ndi Mulungu, nanga kudzatani, Iye akadzawalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka. 16 Ngati chigawo chimodzi cha buledi woperekedwa monga zipatso zoyamba ndi choyera, ndiye kuti zonsezo ndi zoyera. Ngati muzu ndi oyera, nʼchimodzimodzinso nthambi zake. 17 Ngati nthambi zina zinakhadzulidwa ndipo inu, inu ndiye nthambi za olivi wakuthengo, nʼkulumikizidwa pamalo pa nthambi zimenezo, ndipo tsopano mukulandira nawo zakudya zochokera ku mizu ya olivi, 18 musadzitame kunyoza nthambi zinazo. Ngati mutero, ganizirani ichi kuti Inu simugwiriziza mizu, koma muzu ukugwiriziza inu. 19 Tsono mudzati, “Nthambizo zinakhadzulidwa kuti ine ndilumikizidwepo.” 20 Nʼzoona. Koma iwo anakhadzulidwa chifukwa chosakhulupirira ndipo inu mukuyima mwachikhulupiriro. Musadzitukumule, koma muchite mantha. 21 Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachibadwidwe, Iye sadzakulekererani inunso. 22 Nʼchifukwa chake ganizirani za kukoma mtima ndi za ukali wa Mulungu. Ukali uli kwa iwo amene anagwa koma kukoma mtima kwa inu, malinga ngati musamala kukoma mtima kwakeko kupanda kutero inunso mudzakhadzulidwanso. 23 Ngati iwo asiya kukhala osakhulupirira, adzalumikizidwanso pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24 Pakuti ngati inu, mwa chilengedwe munali mtengo wa olivi wa kuthengo, Mulungu anakukhadzulani nakulumikizani ku mtengo wa olivi wodzalidwa, zomwe ndi zotsutsana ndi chilengedwe, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuwalumikizanso mu mtengo wawowawo wa olivi? 25 Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa za chinsinsi ichi, kuti mungadziyese nokha anzeru. Kuwuma mtima kumene Aisraeli akuchita ndi kwa kanthawi kufikira chiwerengero cha a mitundu chitalowa. 26 Kotero tsono Aisraeli onse adzapulumuka, monga kwalembedwa kuti,“Mpulumutsi adzachokera ku Ziyoni;Iye adzachotsa zoyipa zonse za Yakobo. 27 Ndipo ili lidzakhala pangano langa ndi iwopamene Ine ndidzachotsa machimo awo.” 28 Chifukwa cha Uthenga Wabwino, Aisraeli asanduka adani a Mulungu kuti inu mupindule. Koma kunena za kusankhidwa, iwo ndi okondedwa ndi Mulungu chifukwa cha makolo awo aja. 29 Pakuti Mulungu akayitana munthu ndi kumupatsa mphatso sangasinthenso. 30 Monga mmene inu munalili, osamvera Mulungu pa nthawi ina, tsopano mwalandira chifundo chifukwa cha kusamvera kwawo. 31 Chonchonso iwo akhala osamvera tsopano kuti iwonso alandire chifundo chifukwa cha chifundo cha Mulungu kwa inu. 32 Pakuti Mulungu anasandutsa anthu onse a mʼndende ya kusamvera kuti Iye akaonetse chifundo kwa onse. 33 Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri!Ndani angazindikire maweruzidwe ake,ndipo njira zake angazitulukire ndani? 34 “Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye?Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?” 35 “Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu,kuti Mulunguyo amubwezere iye?” 36 Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye.Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

In Other Versions

Romans 11 in the ANGEFD

Romans 11 in the ANTPNG2D

Romans 11 in the AS21

Romans 11 in the BAGH

Romans 11 in the BBPNG

Romans 11 in the BBT1E

Romans 11 in the BDS

Romans 11 in the BEV

Romans 11 in the BHAD

Romans 11 in the BIB

Romans 11 in the BLPT

Romans 11 in the BNT

Romans 11 in the BNTABOOT

Romans 11 in the BNTLV

Romans 11 in the BOATCB

Romans 11 in the BOATCB2

Romans 11 in the BOBCV

Romans 11 in the BOCNT

Romans 11 in the BOECS

Romans 11 in the BOHCB

Romans 11 in the BOHCV

Romans 11 in the BOHLNT

Romans 11 in the BOHNTLTAL

Romans 11 in the BOICB

Romans 11 in the BOILNTAP

Romans 11 in the BOITCV

Romans 11 in the BOKCV

Romans 11 in the BOKCV2

Romans 11 in the BOKHWOG

Romans 11 in the BOKSSV

Romans 11 in the BOLCB

Romans 11 in the BOLCB2

Romans 11 in the BOMCV

Romans 11 in the BONAV

Romans 11 in the BONCB

Romans 11 in the BONLT

Romans 11 in the BONUT2

Romans 11 in the BOPLNT

Romans 11 in the BOSCB

Romans 11 in the BOSNC

Romans 11 in the BOTLNT

Romans 11 in the BOVCB

Romans 11 in the BOYCB

Romans 11 in the BPBB

Romans 11 in the BPH

Romans 11 in the BSB

Romans 11 in the CCB

Romans 11 in the CUV

Romans 11 in the CUVS

Romans 11 in the DBT

Romans 11 in the DGDNT

Romans 11 in the DHNT

Romans 11 in the DNT

Romans 11 in the ELBE

Romans 11 in the EMTV

Romans 11 in the ESV

Romans 11 in the FBV

Romans 11 in the FEB

Romans 11 in the GGMNT

Romans 11 in the GNT

Romans 11 in the HARY

Romans 11 in the HNT

Romans 11 in the IRVA

Romans 11 in the IRVB

Romans 11 in the IRVG

Romans 11 in the IRVH

Romans 11 in the IRVK

Romans 11 in the IRVM

Romans 11 in the IRVM2

Romans 11 in the IRVO

Romans 11 in the IRVP

Romans 11 in the IRVT

Romans 11 in the IRVT2

Romans 11 in the IRVU

Romans 11 in the ISVN

Romans 11 in the JSNT

Romans 11 in the KAPI

Romans 11 in the KBT1ETNIK

Romans 11 in the KBV

Romans 11 in the KJV

Romans 11 in the KNFD

Romans 11 in the LBA

Romans 11 in the LBLA

Romans 11 in the LNT

Romans 11 in the LSV

Romans 11 in the MAAL

Romans 11 in the MBV

Romans 11 in the MBV2

Romans 11 in the MHNT

Romans 11 in the MKNFD

Romans 11 in the MNG

Romans 11 in the MNT

Romans 11 in the MNT2

Romans 11 in the MRS1T

Romans 11 in the NAA

Romans 11 in the NASB

Romans 11 in the NBLA

Romans 11 in the NBS

Romans 11 in the NBVTP

Romans 11 in the NET2

Romans 11 in the NIV11

Romans 11 in the NNT

Romans 11 in the NNT2

Romans 11 in the NNT3

Romans 11 in the PDDPT

Romans 11 in the PFNT

Romans 11 in the RMNT

Romans 11 in the SBIAS

Romans 11 in the SBIBS

Romans 11 in the SBIBS2

Romans 11 in the SBICS

Romans 11 in the SBIDS

Romans 11 in the SBIGS

Romans 11 in the SBIHS

Romans 11 in the SBIIS

Romans 11 in the SBIIS2

Romans 11 in the SBIIS3

Romans 11 in the SBIKS

Romans 11 in the SBIKS2

Romans 11 in the SBIMS

Romans 11 in the SBIOS

Romans 11 in the SBIPS

Romans 11 in the SBISS

Romans 11 in the SBITS

Romans 11 in the SBITS2

Romans 11 in the SBITS3

Romans 11 in the SBITS4

Romans 11 in the SBIUS

Romans 11 in the SBIVS

Romans 11 in the SBT

Romans 11 in the SBT1E

Romans 11 in the SCHL

Romans 11 in the SNT

Romans 11 in the SUSU

Romans 11 in the SUSU2

Romans 11 in the SYNO

Romans 11 in the TBIAOTANT

Romans 11 in the TBT1E

Romans 11 in the TBT1E2

Romans 11 in the TFTIP

Romans 11 in the TFTU

Romans 11 in the TGNTATF3T

Romans 11 in the THAI

Romans 11 in the TNFD

Romans 11 in the TNT

Romans 11 in the TNTIK

Romans 11 in the TNTIL

Romans 11 in the TNTIN

Romans 11 in the TNTIP

Romans 11 in the TNTIZ

Romans 11 in the TOMA

Romans 11 in the TTENT

Romans 11 in the UBG

Romans 11 in the UGV

Romans 11 in the UGV2

Romans 11 in the UGV3

Romans 11 in the VBL

Romans 11 in the VDCC

Romans 11 in the YALU

Romans 11 in the YAPE

Romans 11 in the YBVTP

Romans 11 in the ZBP