Romans 6 (BOGWICC)

1 Nanga tinene chiyani? Kodi tipitirire kuchimwa kuti chisomo chichulukebe? 2 Ayi. Mʼnjira iliyonse! Popeza tinafa ku tchimo, nanga tidzapitirira bwanji kukhalabe mʼmenemo? 3 Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? 4 Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano. 5 Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake. 6 Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo 7 chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo. 8 Koma ngati tinafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. 9 Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. 10 Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu. 11 Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu. 12 Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. 13 Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo. 14 Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo. 15 Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! 16 Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake. 17 Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira. 18 Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo. 19 Ine ndikufanizira zinthu za tsiku ndi tsiku chifukwa chikhalidwe chanu nʼchofowoka. Monga momwe munkapereka ziwalo za matupi kukhala akapolo a zonyansa ndi makhalidwe oyipa, zimene zimanka zichulukirabe, choncho tsopano dziperekeni ziwalozo kuti zikhale akapolo achilungamo ndi a kuyera mtima. 20 Pomwe munali akapolo atchimo, simunkalabadira za chilungamo. 21 Kodi munapeza phindu lanji pochita zinthu zimenezi, zomwe tsopano mukuchita nazo manyazi? Zinthu zimenezo zotsatira zake ndi imfa! 22 Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha. 23 Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

In Other Versions

Romans 6 in the ANGEFD

Romans 6 in the ANTPNG2D

Romans 6 in the AS21

Romans 6 in the BAGH

Romans 6 in the BBPNG

Romans 6 in the BBT1E

Romans 6 in the BDS

Romans 6 in the BEV

Romans 6 in the BHAD

Romans 6 in the BIB

Romans 6 in the BLPT

Romans 6 in the BNT

Romans 6 in the BNTABOOT

Romans 6 in the BNTLV

Romans 6 in the BOATCB

Romans 6 in the BOATCB2

Romans 6 in the BOBCV

Romans 6 in the BOCNT

Romans 6 in the BOECS

Romans 6 in the BOHCB

Romans 6 in the BOHCV

Romans 6 in the BOHLNT

Romans 6 in the BOHNTLTAL

Romans 6 in the BOICB

Romans 6 in the BOILNTAP

Romans 6 in the BOITCV

Romans 6 in the BOKCV

Romans 6 in the BOKCV2

Romans 6 in the BOKHWOG

Romans 6 in the BOKSSV

Romans 6 in the BOLCB

Romans 6 in the BOLCB2

Romans 6 in the BOMCV

Romans 6 in the BONAV

Romans 6 in the BONCB

Romans 6 in the BONLT

Romans 6 in the BONUT2

Romans 6 in the BOPLNT

Romans 6 in the BOSCB

Romans 6 in the BOSNC

Romans 6 in the BOTLNT

Romans 6 in the BOVCB

Romans 6 in the BOYCB

Romans 6 in the BPBB

Romans 6 in the BPH

Romans 6 in the BSB

Romans 6 in the CCB

Romans 6 in the CUV

Romans 6 in the CUVS

Romans 6 in the DBT

Romans 6 in the DGDNT

Romans 6 in the DHNT

Romans 6 in the DNT

Romans 6 in the ELBE

Romans 6 in the EMTV

Romans 6 in the ESV

Romans 6 in the FBV

Romans 6 in the FEB

Romans 6 in the GGMNT

Romans 6 in the GNT

Romans 6 in the HARY

Romans 6 in the HNT

Romans 6 in the IRVA

Romans 6 in the IRVB

Romans 6 in the IRVG

Romans 6 in the IRVH

Romans 6 in the IRVK

Romans 6 in the IRVM

Romans 6 in the IRVM2

Romans 6 in the IRVO

Romans 6 in the IRVP

Romans 6 in the IRVT

Romans 6 in the IRVT2

Romans 6 in the IRVU

Romans 6 in the ISVN

Romans 6 in the JSNT

Romans 6 in the KAPI

Romans 6 in the KBT1ETNIK

Romans 6 in the KBV

Romans 6 in the KJV

Romans 6 in the KNFD

Romans 6 in the LBA

Romans 6 in the LBLA

Romans 6 in the LNT

Romans 6 in the LSV

Romans 6 in the MAAL

Romans 6 in the MBV

Romans 6 in the MBV2

Romans 6 in the MHNT

Romans 6 in the MKNFD

Romans 6 in the MNG

Romans 6 in the MNT

Romans 6 in the MNT2

Romans 6 in the MRS1T

Romans 6 in the NAA

Romans 6 in the NASB

Romans 6 in the NBLA

Romans 6 in the NBS

Romans 6 in the NBVTP

Romans 6 in the NET2

Romans 6 in the NIV11

Romans 6 in the NNT

Romans 6 in the NNT2

Romans 6 in the NNT3

Romans 6 in the PDDPT

Romans 6 in the PFNT

Romans 6 in the RMNT

Romans 6 in the SBIAS

Romans 6 in the SBIBS

Romans 6 in the SBIBS2

Romans 6 in the SBICS

Romans 6 in the SBIDS

Romans 6 in the SBIGS

Romans 6 in the SBIHS

Romans 6 in the SBIIS

Romans 6 in the SBIIS2

Romans 6 in the SBIIS3

Romans 6 in the SBIKS

Romans 6 in the SBIKS2

Romans 6 in the SBIMS

Romans 6 in the SBIOS

Romans 6 in the SBIPS

Romans 6 in the SBISS

Romans 6 in the SBITS

Romans 6 in the SBITS2

Romans 6 in the SBITS3

Romans 6 in the SBITS4

Romans 6 in the SBIUS

Romans 6 in the SBIVS

Romans 6 in the SBT

Romans 6 in the SBT1E

Romans 6 in the SCHL

Romans 6 in the SNT

Romans 6 in the SUSU

Romans 6 in the SUSU2

Romans 6 in the SYNO

Romans 6 in the TBIAOTANT

Romans 6 in the TBT1E

Romans 6 in the TBT1E2

Romans 6 in the TFTIP

Romans 6 in the TFTU

Romans 6 in the TGNTATF3T

Romans 6 in the THAI

Romans 6 in the TNFD

Romans 6 in the TNT

Romans 6 in the TNTIK

Romans 6 in the TNTIL

Romans 6 in the TNTIN

Romans 6 in the TNTIP

Romans 6 in the TNTIZ

Romans 6 in the TOMA

Romans 6 in the TTENT

Romans 6 in the UBG

Romans 6 in the UGV

Romans 6 in the UGV2

Romans 6 in the UGV3

Romans 6 in the VBL

Romans 6 in the VDCC

Romans 6 in the YALU

Romans 6 in the YAPE

Romans 6 in the YBVTP

Romans 6 in the ZBP