1 John 4 (BOGWICC)
1 Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi. 2 Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu, 3 koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi. 4 Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi. 5 Aneneri onyengawa ndi ochokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake amayankhula za dziko lapansi, ndipo dziko lapansi limawamvera. 6 Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo. 7 Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. 8 Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi. 9 Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo. 10 Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. 11 Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake. 12 Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife. 13 Ife tikudziwa kuti timakhala mwa Iye ndipo Iyeyo amakhala mwa ife chifukwa anatipatsa Mzimu wake. 14 Ndipo taona ndipo tikuchitira umboni, kuti Atate anatuma Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. 15 Ngati aliyense avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye ndipo iyeyo amakhala mwa Mulungu. 16 Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife.Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye. 17 Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu. 18 Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro. 19 Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda. 20 Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone. 21 Ndipo Iye anatipatsa lamulo lakuti: Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso mʼbale wake.
In Other Versions
1 John 4 in the ANGEFD
1 John 4 in the ANTPNG2D
1 John 4 in the AS21
1 John 4 in the BAGH
1 John 4 in the BBPNG
1 John 4 in the BBT1E
1 John 4 in the BDS
1 John 4 in the BEV
1 John 4 in the BHAD
1 John 4 in the BIB
1 John 4 in the BLPT
1 John 4 in the BNT
1 John 4 in the BNTABOOT
1 John 4 in the BNTLV
1 John 4 in the BOATCB
1 John 4 in the BOATCB2
1 John 4 in the BOBCV
1 John 4 in the BOCNT
1 John 4 in the BOECS
1 John 4 in the BOHCB
1 John 4 in the BOHCV
1 John 4 in the BOHLNT
1 John 4 in the BOHNTLTAL
1 John 4 in the BOICB
1 John 4 in the BOILNTAP
1 John 4 in the BOITCV
1 John 4 in the BOKCV
1 John 4 in the BOKCV2
1 John 4 in the BOKHWOG
1 John 4 in the BOKSSV
1 John 4 in the BOLCB
1 John 4 in the BOLCB2
1 John 4 in the BOMCV
1 John 4 in the BONAV
1 John 4 in the BONCB
1 John 4 in the BONLT
1 John 4 in the BONUT2
1 John 4 in the BOPLNT
1 John 4 in the BOSCB
1 John 4 in the BOSNC
1 John 4 in the BOTLNT
1 John 4 in the BOVCB
1 John 4 in the BOYCB
1 John 4 in the BPBB
1 John 4 in the BPH
1 John 4 in the BSB
1 John 4 in the CCB
1 John 4 in the CUV
1 John 4 in the CUVS
1 John 4 in the DBT
1 John 4 in the DGDNT
1 John 4 in the DHNT
1 John 4 in the DNT
1 John 4 in the ELBE
1 John 4 in the EMTV
1 John 4 in the ESV
1 John 4 in the FBV
1 John 4 in the FEB
1 John 4 in the GGMNT
1 John 4 in the GNT
1 John 4 in the HARY
1 John 4 in the HNT
1 John 4 in the IRVA
1 John 4 in the IRVB
1 John 4 in the IRVG
1 John 4 in the IRVH
1 John 4 in the IRVK
1 John 4 in the IRVM
1 John 4 in the IRVM2
1 John 4 in the IRVO
1 John 4 in the IRVP
1 John 4 in the IRVT
1 John 4 in the IRVT2
1 John 4 in the IRVU
1 John 4 in the ISVN
1 John 4 in the JSNT
1 John 4 in the KAPI
1 John 4 in the KBT1ETNIK
1 John 4 in the KBV
1 John 4 in the KJV
1 John 4 in the KNFD
1 John 4 in the LBA
1 John 4 in the LBLA
1 John 4 in the LNT
1 John 4 in the LSV
1 John 4 in the MAAL
1 John 4 in the MBV
1 John 4 in the MBV2
1 John 4 in the MHNT
1 John 4 in the MKNFD
1 John 4 in the MNG
1 John 4 in the MNT
1 John 4 in the MNT2
1 John 4 in the MRS1T
1 John 4 in the NAA
1 John 4 in the NASB
1 John 4 in the NBLA
1 John 4 in the NBS
1 John 4 in the NBVTP
1 John 4 in the NET2
1 John 4 in the NIV11
1 John 4 in the NNT
1 John 4 in the NNT2
1 John 4 in the NNT3
1 John 4 in the PDDPT
1 John 4 in the PFNT
1 John 4 in the RMNT
1 John 4 in the SBIAS
1 John 4 in the SBIBS
1 John 4 in the SBIBS2
1 John 4 in the SBICS
1 John 4 in the SBIDS
1 John 4 in the SBIGS
1 John 4 in the SBIHS
1 John 4 in the SBIIS
1 John 4 in the SBIIS2
1 John 4 in the SBIIS3
1 John 4 in the SBIKS
1 John 4 in the SBIKS2
1 John 4 in the SBIMS
1 John 4 in the SBIOS
1 John 4 in the SBIPS
1 John 4 in the SBISS
1 John 4 in the SBITS
1 John 4 in the SBITS2
1 John 4 in the SBITS3
1 John 4 in the SBITS4
1 John 4 in the SBIUS
1 John 4 in the SBIVS
1 John 4 in the SBT
1 John 4 in the SBT1E
1 John 4 in the SCHL
1 John 4 in the SNT
1 John 4 in the SUSU
1 John 4 in the SUSU2
1 John 4 in the SYNO
1 John 4 in the TBIAOTANT
1 John 4 in the TBT1E
1 John 4 in the TBT1E2
1 John 4 in the TFTIP
1 John 4 in the TFTU
1 John 4 in the TGNTATF3T
1 John 4 in the THAI
1 John 4 in the TNFD
1 John 4 in the TNT
1 John 4 in the TNTIK
1 John 4 in the TNTIL
1 John 4 in the TNTIN
1 John 4 in the TNTIP
1 John 4 in the TNTIZ
1 John 4 in the TOMA
1 John 4 in the TTENT
1 John 4 in the UBG
1 John 4 in the UGV
1 John 4 in the UGV2
1 John 4 in the UGV3
1 John 4 in the VBL
1 John 4 in the VDCC
1 John 4 in the YALU
1 John 4 in the YAPE
1 John 4 in the YBVTP
1 John 4 in the ZBP