Isaiah 22 (BOGWICC)
1 Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya:Kodi chachitika nʼchiyani,kuti nonsenu mukwere pa madenga? 2 Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,kapena kufera pa nkhondo. 3 Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi;koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe.Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo,ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali. 4 Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.Musayesere kunditonthozachifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.” 5 Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tionemavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezomʼChigwa cha Masomphenya.Malinga agumuka,komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri. 6 Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaletandi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango. 7 Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda; 8 zonse zoteteza Yuda zachotsedwa. Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼanazida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango; 9 inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davideanali ndi malo ambiri ogumuka;munasunga madzimu chidziwe chakumunsi. 10 Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemundipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija. 11 Pakati pa makoma awiri munamanga chitsimechosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe. 12 Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonseanakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi;kumeta mutu wanu mpalandi kuvala ziguduli. 13 Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;munapha ngʼombe ndi nkhosa;munadya nyama ndi kumwa vinyo.Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwapakuti mawa tifa!” 14 Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse. 15 Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,amene amayangʼanira nyumba yaufumu: 16 Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezokuti udzikumbire manda kuno,kudzikumbira manda pa phirindi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe? 17 “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimbandi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu. 18 Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpirandipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.Kumeneko ndiko ukaferendipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako. 19 Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wakondipo ndidzakutsitsa pa udindo wako. 20 “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. 21 Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. 22 Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. 23 Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. 24 Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo. 25 “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
In Other Versions
Isaiah 22 in the ANGEFD
Isaiah 22 in the ANTPNG2D
Isaiah 22 in the AS21
Isaiah 22 in the BAGH
Isaiah 22 in the BBPNG
Isaiah 22 in the BBT1E
Isaiah 22 in the BDS
Isaiah 22 in the BEV
Isaiah 22 in the BHAD
Isaiah 22 in the BIB
Isaiah 22 in the BLPT
Isaiah 22 in the BNT
Isaiah 22 in the BNTABOOT
Isaiah 22 in the BNTLV
Isaiah 22 in the BOATCB
Isaiah 22 in the BOATCB2
Isaiah 22 in the BOBCV
Isaiah 22 in the BOCNT
Isaiah 22 in the BOECS
Isaiah 22 in the BOHCB
Isaiah 22 in the BOHCV
Isaiah 22 in the BOHLNT
Isaiah 22 in the BOHNTLTAL
Isaiah 22 in the BOICB
Isaiah 22 in the BOILNTAP
Isaiah 22 in the BOITCV
Isaiah 22 in the BOKCV
Isaiah 22 in the BOKCV2
Isaiah 22 in the BOKHWOG
Isaiah 22 in the BOKSSV
Isaiah 22 in the BOLCB
Isaiah 22 in the BOLCB2
Isaiah 22 in the BOMCV
Isaiah 22 in the BONAV
Isaiah 22 in the BONCB
Isaiah 22 in the BONLT
Isaiah 22 in the BONUT2
Isaiah 22 in the BOPLNT
Isaiah 22 in the BOSCB
Isaiah 22 in the BOSNC
Isaiah 22 in the BOTLNT
Isaiah 22 in the BOVCB
Isaiah 22 in the BOYCB
Isaiah 22 in the BPBB
Isaiah 22 in the BPH
Isaiah 22 in the BSB
Isaiah 22 in the CCB
Isaiah 22 in the CUV
Isaiah 22 in the CUVS
Isaiah 22 in the DBT
Isaiah 22 in the DGDNT
Isaiah 22 in the DHNT
Isaiah 22 in the DNT
Isaiah 22 in the ELBE
Isaiah 22 in the EMTV
Isaiah 22 in the ESV
Isaiah 22 in the FBV
Isaiah 22 in the FEB
Isaiah 22 in the GGMNT
Isaiah 22 in the GNT
Isaiah 22 in the HARY
Isaiah 22 in the HNT
Isaiah 22 in the IRVA
Isaiah 22 in the IRVB
Isaiah 22 in the IRVG
Isaiah 22 in the IRVH
Isaiah 22 in the IRVK
Isaiah 22 in the IRVM
Isaiah 22 in the IRVM2
Isaiah 22 in the IRVO
Isaiah 22 in the IRVP
Isaiah 22 in the IRVT
Isaiah 22 in the IRVT2
Isaiah 22 in the IRVU
Isaiah 22 in the ISVN
Isaiah 22 in the JSNT
Isaiah 22 in the KAPI
Isaiah 22 in the KBT1ETNIK
Isaiah 22 in the KBV
Isaiah 22 in the KJV
Isaiah 22 in the KNFD
Isaiah 22 in the LBA
Isaiah 22 in the LBLA
Isaiah 22 in the LNT
Isaiah 22 in the LSV
Isaiah 22 in the MAAL
Isaiah 22 in the MBV
Isaiah 22 in the MBV2
Isaiah 22 in the MHNT
Isaiah 22 in the MKNFD
Isaiah 22 in the MNG
Isaiah 22 in the MNT
Isaiah 22 in the MNT2
Isaiah 22 in the MRS1T
Isaiah 22 in the NAA
Isaiah 22 in the NASB
Isaiah 22 in the NBLA
Isaiah 22 in the NBS
Isaiah 22 in the NBVTP
Isaiah 22 in the NET2
Isaiah 22 in the NIV11
Isaiah 22 in the NNT
Isaiah 22 in the NNT2
Isaiah 22 in the NNT3
Isaiah 22 in the PDDPT
Isaiah 22 in the PFNT
Isaiah 22 in the RMNT
Isaiah 22 in the SBIAS
Isaiah 22 in the SBIBS
Isaiah 22 in the SBIBS2
Isaiah 22 in the SBICS
Isaiah 22 in the SBIDS
Isaiah 22 in the SBIGS
Isaiah 22 in the SBIHS
Isaiah 22 in the SBIIS
Isaiah 22 in the SBIIS2
Isaiah 22 in the SBIIS3
Isaiah 22 in the SBIKS
Isaiah 22 in the SBIKS2
Isaiah 22 in the SBIMS
Isaiah 22 in the SBIOS
Isaiah 22 in the SBIPS
Isaiah 22 in the SBISS
Isaiah 22 in the SBITS
Isaiah 22 in the SBITS2
Isaiah 22 in the SBITS3
Isaiah 22 in the SBITS4
Isaiah 22 in the SBIUS
Isaiah 22 in the SBIVS
Isaiah 22 in the SBT
Isaiah 22 in the SBT1E
Isaiah 22 in the SCHL
Isaiah 22 in the SNT
Isaiah 22 in the SUSU
Isaiah 22 in the SUSU2
Isaiah 22 in the SYNO
Isaiah 22 in the TBIAOTANT
Isaiah 22 in the TBT1E
Isaiah 22 in the TBT1E2
Isaiah 22 in the TFTIP
Isaiah 22 in the TFTU
Isaiah 22 in the TGNTATF3T
Isaiah 22 in the THAI
Isaiah 22 in the TNFD
Isaiah 22 in the TNT
Isaiah 22 in the TNTIK
Isaiah 22 in the TNTIL
Isaiah 22 in the TNTIN
Isaiah 22 in the TNTIP
Isaiah 22 in the TNTIZ
Isaiah 22 in the TOMA
Isaiah 22 in the TTENT
Isaiah 22 in the UBG
Isaiah 22 in the UGV
Isaiah 22 in the UGV2
Isaiah 22 in the UGV3
Isaiah 22 in the VBL
Isaiah 22 in the VDCC
Isaiah 22 in the YALU
Isaiah 22 in the YAPE
Isaiah 22 in the YBVTP
Isaiah 22 in the ZBP