Isaiah 3 (BOGWICC)
1 Taonani tsopano, AmbuyeYehova Wamphamvuzonse,ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yudazinthu pamodzi ndi thandizo;adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse, 2 anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,oweruza ndi aneneri,anthu olosera ndi akuluakulu, 3 atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera. 4 Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo;ana akhanda ndiwo adzawalamulire. 5 Anthu adzazunzana,munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake.Anthu wamba adzanyozaakuluakulu. 6 Munthu adzagwira mʼbale wakemʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati,“Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu;lamulira malo opasuka ano!” 7 Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti,“Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake.Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga;musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.” 8 Yerusalemu akudzandira,Yuda akugwa;zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova,sakulabadira ulemerero wa Mulungu. 9 Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa;amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu;salibisa tchimo lawolo.Tsoka kwa iwoodziputira okha mavuto. 10 Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino,pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo. 11 Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo!Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita. 12 Achinyamata akupondereza anthu anga,ndipo amene akuwalamulira ndi akazi.Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani;akukuchotsani pa njira yanu. 13 Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu;wakonzeka kuti aweruze anthu ake. 14 Yehova akuwazenga milanduakuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi. 15 Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga,nʼkudyera masuku pamutu amphawi?”Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse. 16 Yehova akunena kuti,“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,akuyenda atakweza makosi awo,akukopa amuna ndi maso awoakuyenda monyangʼamaakuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo 17 Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.” 18 Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi, 19 ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope, 20 maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa, 21 mphete ndi zipini, 22 zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama, 23 magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa. 24 Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi. 25 Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,asilikali ako adzafera ku nkhondo. 26 Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.
In Other Versions
Isaiah 3 in the ANGEFD
Isaiah 3 in the ANTPNG2D
Isaiah 3 in the AS21
Isaiah 3 in the BAGH
Isaiah 3 in the BBPNG
Isaiah 3 in the BBT1E
Isaiah 3 in the BDS
Isaiah 3 in the BEV
Isaiah 3 in the BHAD
Isaiah 3 in the BIB
Isaiah 3 in the BLPT
Isaiah 3 in the BNT
Isaiah 3 in the BNTABOOT
Isaiah 3 in the BNTLV
Isaiah 3 in the BOATCB
Isaiah 3 in the BOATCB2
Isaiah 3 in the BOBCV
Isaiah 3 in the BOCNT
Isaiah 3 in the BOECS
Isaiah 3 in the BOHCB
Isaiah 3 in the BOHCV
Isaiah 3 in the BOHLNT
Isaiah 3 in the BOHNTLTAL
Isaiah 3 in the BOICB
Isaiah 3 in the BOILNTAP
Isaiah 3 in the BOITCV
Isaiah 3 in the BOKCV
Isaiah 3 in the BOKCV2
Isaiah 3 in the BOKHWOG
Isaiah 3 in the BOKSSV
Isaiah 3 in the BOLCB
Isaiah 3 in the BOLCB2
Isaiah 3 in the BOMCV
Isaiah 3 in the BONAV
Isaiah 3 in the BONCB
Isaiah 3 in the BONLT
Isaiah 3 in the BONUT2
Isaiah 3 in the BOPLNT
Isaiah 3 in the BOSCB
Isaiah 3 in the BOSNC
Isaiah 3 in the BOTLNT
Isaiah 3 in the BOVCB
Isaiah 3 in the BOYCB
Isaiah 3 in the BPBB
Isaiah 3 in the BPH
Isaiah 3 in the BSB
Isaiah 3 in the CCB
Isaiah 3 in the CUV
Isaiah 3 in the CUVS
Isaiah 3 in the DBT
Isaiah 3 in the DGDNT
Isaiah 3 in the DHNT
Isaiah 3 in the DNT
Isaiah 3 in the ELBE
Isaiah 3 in the EMTV
Isaiah 3 in the ESV
Isaiah 3 in the FBV
Isaiah 3 in the FEB
Isaiah 3 in the GGMNT
Isaiah 3 in the GNT
Isaiah 3 in the HARY
Isaiah 3 in the HNT
Isaiah 3 in the IRVA
Isaiah 3 in the IRVB
Isaiah 3 in the IRVG
Isaiah 3 in the IRVH
Isaiah 3 in the IRVK
Isaiah 3 in the IRVM
Isaiah 3 in the IRVM2
Isaiah 3 in the IRVO
Isaiah 3 in the IRVP
Isaiah 3 in the IRVT
Isaiah 3 in the IRVT2
Isaiah 3 in the IRVU
Isaiah 3 in the ISVN
Isaiah 3 in the JSNT
Isaiah 3 in the KAPI
Isaiah 3 in the KBT1ETNIK
Isaiah 3 in the KBV
Isaiah 3 in the KJV
Isaiah 3 in the KNFD
Isaiah 3 in the LBA
Isaiah 3 in the LBLA
Isaiah 3 in the LNT
Isaiah 3 in the LSV
Isaiah 3 in the MAAL
Isaiah 3 in the MBV
Isaiah 3 in the MBV2
Isaiah 3 in the MHNT
Isaiah 3 in the MKNFD
Isaiah 3 in the MNG
Isaiah 3 in the MNT
Isaiah 3 in the MNT2
Isaiah 3 in the MRS1T
Isaiah 3 in the NAA
Isaiah 3 in the NASB
Isaiah 3 in the NBLA
Isaiah 3 in the NBS
Isaiah 3 in the NBVTP
Isaiah 3 in the NET2
Isaiah 3 in the NIV11
Isaiah 3 in the NNT
Isaiah 3 in the NNT2
Isaiah 3 in the NNT3
Isaiah 3 in the PDDPT
Isaiah 3 in the PFNT
Isaiah 3 in the RMNT
Isaiah 3 in the SBIAS
Isaiah 3 in the SBIBS
Isaiah 3 in the SBIBS2
Isaiah 3 in the SBICS
Isaiah 3 in the SBIDS
Isaiah 3 in the SBIGS
Isaiah 3 in the SBIHS
Isaiah 3 in the SBIIS
Isaiah 3 in the SBIIS2
Isaiah 3 in the SBIIS3
Isaiah 3 in the SBIKS
Isaiah 3 in the SBIKS2
Isaiah 3 in the SBIMS
Isaiah 3 in the SBIOS
Isaiah 3 in the SBIPS
Isaiah 3 in the SBISS
Isaiah 3 in the SBITS
Isaiah 3 in the SBITS2
Isaiah 3 in the SBITS3
Isaiah 3 in the SBITS4
Isaiah 3 in the SBIUS
Isaiah 3 in the SBIVS
Isaiah 3 in the SBT
Isaiah 3 in the SBT1E
Isaiah 3 in the SCHL
Isaiah 3 in the SNT
Isaiah 3 in the SUSU
Isaiah 3 in the SUSU2
Isaiah 3 in the SYNO
Isaiah 3 in the TBIAOTANT
Isaiah 3 in the TBT1E
Isaiah 3 in the TBT1E2
Isaiah 3 in the TFTIP
Isaiah 3 in the TFTU
Isaiah 3 in the TGNTATF3T
Isaiah 3 in the THAI
Isaiah 3 in the TNFD
Isaiah 3 in the TNT
Isaiah 3 in the TNTIK
Isaiah 3 in the TNTIL
Isaiah 3 in the TNTIN
Isaiah 3 in the TNTIP
Isaiah 3 in the TNTIZ
Isaiah 3 in the TOMA
Isaiah 3 in the TTENT
Isaiah 3 in the UBG
Isaiah 3 in the UGV
Isaiah 3 in the UGV2
Isaiah 3 in the UGV3
Isaiah 3 in the VBL
Isaiah 3 in the VDCC
Isaiah 3 in the YALU
Isaiah 3 in the YAPE
Isaiah 3 in the YBVTP
Isaiah 3 in the ZBP