Isaiah 51 (BOGWICC)

1 “Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutsondiponso amene mumafunafuna Yehova:Taganizani za thanthwe kumene munasemedwandipo ku ngwenya kumene anakukumbani; 2 taganizani za Abrahamu, kholo lanu,ndi Sara, amene anakubalani.Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana,koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri. 3 Yehova adzatonthozadi Ziyoni,ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse;Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni,malo ake owuma ngati munda wa Yehova.Anthu adzayimba nyimbo zonditamandandi kundiyamika. 4 “Mverani Ine, anthu anga:tcherani khutu, inu mtundu wanga:malangizo adzachokera kwa Ine;cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse. 5 Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga.Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga;ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse.Mayiko akutali akundiyembekezera.Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse. 6 Kwezani maso anu mlengalenga,yangʼanani pansi pa dziko;mlengalenga udzazimirira ngati utsi,dziko lapansi lidzatha ngati chovalandipo anthu ake adzafa ngati nsabwe.Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse. 7 “Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi,anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu;musaope kudzudzulidwa ndi anthukapena kuopsezedwa akamakulalatirani. 8 Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala;mbozi idzawadya ngati thonje.Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya,chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.” 9 Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe,Inu Yehova;dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana,monga nthawi ya mibado yakale.Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe,amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija? 10 Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu,madzi ozama kwambiri aja?Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama,kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma? 11 Anthu amene Yehova anawawombola adzabwereranakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa;chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo.Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe,chisoni ndi kubuwula zidzathawa. 12 Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima.Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa?Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa. 13 Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu,amene anayala za mlengalengandi kuyika maziko a dziko lapansi.Inu nthawi zonse mumaopsezedwachifukwa cha ukali wa anthu okuponderezaniamene angofuna kukuwonongani.Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo? 14 Amʼndende adzamasulidwa posachedwa;sadzalowa mʼmanda awo,kapena kusowa chakudya. 15 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma.Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. 16 Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanundipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa.Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga,ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi,ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ” 17 Dzambatuka, dzambatuka!Imirira iwe Yerusalemu.Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyochimene Yehova anakupatsa.Iwe amene unagugudizachikho chochititsa chizwezwe. 18 Mwa ana onse amene anabereka,panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera;mwa ana onse amene analera,panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja. 19 Mavuto awiriwa akugwera iwe.Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga.Ndani angakumvere chisoni?Ndani angakutonthoze? 20 Ana ako akomoka;ali lambalamba pa msewu,ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde.Ukali wa Yehovandi chidzudzulo chake zidzawagwera. 21 Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika,iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo. 22 Ambuye Yehova wanu,Mulungu amene amateteza anthu ake akuti,“Taona, ndachotsa mʼdzanja lakochikho chimene chimakuchititsa kudzandira;sudzamwanso chikhocha ukali wanga. 23 Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza,amene ankakuwuza kuti,‘gona pansi tikuyende pa msana.’Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo,ngati msewu woti ayendepo.”

In Other Versions

Isaiah 51 in the ANGEFD

Isaiah 51 in the ANTPNG2D

Isaiah 51 in the AS21

Isaiah 51 in the BAGH

Isaiah 51 in the BBPNG

Isaiah 51 in the BBT1E

Isaiah 51 in the BDS

Isaiah 51 in the BEV

Isaiah 51 in the BHAD

Isaiah 51 in the BIB

Isaiah 51 in the BLPT

Isaiah 51 in the BNT

Isaiah 51 in the BNTABOOT

Isaiah 51 in the BNTLV

Isaiah 51 in the BOATCB

Isaiah 51 in the BOATCB2

Isaiah 51 in the BOBCV

Isaiah 51 in the BOCNT

Isaiah 51 in the BOECS

Isaiah 51 in the BOHCB

Isaiah 51 in the BOHCV

Isaiah 51 in the BOHLNT

Isaiah 51 in the BOHNTLTAL

Isaiah 51 in the BOICB

Isaiah 51 in the BOILNTAP

Isaiah 51 in the BOITCV

Isaiah 51 in the BOKCV

Isaiah 51 in the BOKCV2

Isaiah 51 in the BOKHWOG

Isaiah 51 in the BOKSSV

Isaiah 51 in the BOLCB

Isaiah 51 in the BOLCB2

Isaiah 51 in the BOMCV

Isaiah 51 in the BONAV

Isaiah 51 in the BONCB

Isaiah 51 in the BONLT

Isaiah 51 in the BONUT2

Isaiah 51 in the BOPLNT

Isaiah 51 in the BOSCB

Isaiah 51 in the BOSNC

Isaiah 51 in the BOTLNT

Isaiah 51 in the BOVCB

Isaiah 51 in the BOYCB

Isaiah 51 in the BPBB

Isaiah 51 in the BPH

Isaiah 51 in the BSB

Isaiah 51 in the CCB

Isaiah 51 in the CUV

Isaiah 51 in the CUVS

Isaiah 51 in the DBT

Isaiah 51 in the DGDNT

Isaiah 51 in the DHNT

Isaiah 51 in the DNT

Isaiah 51 in the ELBE

Isaiah 51 in the EMTV

Isaiah 51 in the ESV

Isaiah 51 in the FBV

Isaiah 51 in the FEB

Isaiah 51 in the GGMNT

Isaiah 51 in the GNT

Isaiah 51 in the HARY

Isaiah 51 in the HNT

Isaiah 51 in the IRVA

Isaiah 51 in the IRVB

Isaiah 51 in the IRVG

Isaiah 51 in the IRVH

Isaiah 51 in the IRVK

Isaiah 51 in the IRVM

Isaiah 51 in the IRVM2

Isaiah 51 in the IRVO

Isaiah 51 in the IRVP

Isaiah 51 in the IRVT

Isaiah 51 in the IRVT2

Isaiah 51 in the IRVU

Isaiah 51 in the ISVN

Isaiah 51 in the JSNT

Isaiah 51 in the KAPI

Isaiah 51 in the KBT1ETNIK

Isaiah 51 in the KBV

Isaiah 51 in the KJV

Isaiah 51 in the KNFD

Isaiah 51 in the LBA

Isaiah 51 in the LBLA

Isaiah 51 in the LNT

Isaiah 51 in the LSV

Isaiah 51 in the MAAL

Isaiah 51 in the MBV

Isaiah 51 in the MBV2

Isaiah 51 in the MHNT

Isaiah 51 in the MKNFD

Isaiah 51 in the MNG

Isaiah 51 in the MNT

Isaiah 51 in the MNT2

Isaiah 51 in the MRS1T

Isaiah 51 in the NAA

Isaiah 51 in the NASB

Isaiah 51 in the NBLA

Isaiah 51 in the NBS

Isaiah 51 in the NBVTP

Isaiah 51 in the NET2

Isaiah 51 in the NIV11

Isaiah 51 in the NNT

Isaiah 51 in the NNT2

Isaiah 51 in the NNT3

Isaiah 51 in the PDDPT

Isaiah 51 in the PFNT

Isaiah 51 in the RMNT

Isaiah 51 in the SBIAS

Isaiah 51 in the SBIBS

Isaiah 51 in the SBIBS2

Isaiah 51 in the SBICS

Isaiah 51 in the SBIDS

Isaiah 51 in the SBIGS

Isaiah 51 in the SBIHS

Isaiah 51 in the SBIIS

Isaiah 51 in the SBIIS2

Isaiah 51 in the SBIIS3

Isaiah 51 in the SBIKS

Isaiah 51 in the SBIKS2

Isaiah 51 in the SBIMS

Isaiah 51 in the SBIOS

Isaiah 51 in the SBIPS

Isaiah 51 in the SBISS

Isaiah 51 in the SBITS

Isaiah 51 in the SBITS2

Isaiah 51 in the SBITS3

Isaiah 51 in the SBITS4

Isaiah 51 in the SBIUS

Isaiah 51 in the SBIVS

Isaiah 51 in the SBT

Isaiah 51 in the SBT1E

Isaiah 51 in the SCHL

Isaiah 51 in the SNT

Isaiah 51 in the SUSU

Isaiah 51 in the SUSU2

Isaiah 51 in the SYNO

Isaiah 51 in the TBIAOTANT

Isaiah 51 in the TBT1E

Isaiah 51 in the TBT1E2

Isaiah 51 in the TFTIP

Isaiah 51 in the TFTU

Isaiah 51 in the TGNTATF3T

Isaiah 51 in the THAI

Isaiah 51 in the TNFD

Isaiah 51 in the TNT

Isaiah 51 in the TNTIK

Isaiah 51 in the TNTIL

Isaiah 51 in the TNTIN

Isaiah 51 in the TNTIP

Isaiah 51 in the TNTIZ

Isaiah 51 in the TOMA

Isaiah 51 in the TTENT

Isaiah 51 in the UBG

Isaiah 51 in the UGV

Isaiah 51 in the UGV2

Isaiah 51 in the UGV3

Isaiah 51 in the VBL

Isaiah 51 in the VDCC

Isaiah 51 in the YALU

Isaiah 51 in the YAPE

Isaiah 51 in the YBVTP

Isaiah 51 in the ZBP