Job 15 (BOGWICC)

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti, 2 “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere,kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa? 3 Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake,kapena kuyankhula mawu opanda phindu? 4 Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungundipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu. 5 Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo;ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali. 6 Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga;milomo yakoyo ikukutsutsa. 7 “Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe? 8 Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu?Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha? 9 Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa?Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe? 10 Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu,anthu amvulazakale kupambana abambo ako. 11 Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira,mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe? 12 Chifukwa chiyani ukupsa mtima,ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako, 13 moti ukupsera mtima Mulungundi kuyankhula mawu otero pakamwa pako? 14 “Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtimakapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima? 15 Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake,ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake, 16 nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota,amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi. 17 “Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera;ndilole ndikuwuze zimene ndaziona, 18 zimene anandiphunzitsa anthu anzeru,sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo. 19 (Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwapamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo). 20 Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake,munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse. 21 Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake,pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo. 22 Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa;iyeyo ndi woyenera kuphedwa. 23 Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya;amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi. 24 Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri;zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo, 25 chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungundipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse. 26 Amapita mwa mwano kukalimbana nayeatanyamula chishango chochindikala ndi cholimba. 27 “Ngakhale nkhope yake ndi yonenepandipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri, 28 munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongekandi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu,nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka. 29 Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa,ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi. 30 Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo;lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake,ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa. 31 Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe,pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu. 32 Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane,ndipo nthambi zake sizidzaphukanso. 33 Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse,adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake. 34 Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabalandipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu. 35 Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa;mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”

In Other Versions

Job 15 in the ANGEFD

Job 15 in the ANTPNG2D

Job 15 in the AS21

Job 15 in the BAGH

Job 15 in the BBPNG

Job 15 in the BBT1E

Job 15 in the BDS

Job 15 in the BEV

Job 15 in the BHAD

Job 15 in the BIB

Job 15 in the BLPT

Job 15 in the BNT

Job 15 in the BNTABOOT

Job 15 in the BNTLV

Job 15 in the BOATCB

Job 15 in the BOATCB2

Job 15 in the BOBCV

Job 15 in the BOCNT

Job 15 in the BOECS

Job 15 in the BOHCB

Job 15 in the BOHCV

Job 15 in the BOHLNT

Job 15 in the BOHNTLTAL

Job 15 in the BOICB

Job 15 in the BOILNTAP

Job 15 in the BOITCV

Job 15 in the BOKCV

Job 15 in the BOKCV2

Job 15 in the BOKHWOG

Job 15 in the BOKSSV

Job 15 in the BOLCB

Job 15 in the BOLCB2

Job 15 in the BOMCV

Job 15 in the BONAV

Job 15 in the BONCB

Job 15 in the BONLT

Job 15 in the BONUT2

Job 15 in the BOPLNT

Job 15 in the BOSCB

Job 15 in the BOSNC

Job 15 in the BOTLNT

Job 15 in the BOVCB

Job 15 in the BOYCB

Job 15 in the BPBB

Job 15 in the BPH

Job 15 in the BSB

Job 15 in the CCB

Job 15 in the CUV

Job 15 in the CUVS

Job 15 in the DBT

Job 15 in the DGDNT

Job 15 in the DHNT

Job 15 in the DNT

Job 15 in the ELBE

Job 15 in the EMTV

Job 15 in the ESV

Job 15 in the FBV

Job 15 in the FEB

Job 15 in the GGMNT

Job 15 in the GNT

Job 15 in the HARY

Job 15 in the HNT

Job 15 in the IRVA

Job 15 in the IRVB

Job 15 in the IRVG

Job 15 in the IRVH

Job 15 in the IRVK

Job 15 in the IRVM

Job 15 in the IRVM2

Job 15 in the IRVO

Job 15 in the IRVP

Job 15 in the IRVT

Job 15 in the IRVT2

Job 15 in the IRVU

Job 15 in the ISVN

Job 15 in the JSNT

Job 15 in the KAPI

Job 15 in the KBT1ETNIK

Job 15 in the KBV

Job 15 in the KJV

Job 15 in the KNFD

Job 15 in the LBA

Job 15 in the LBLA

Job 15 in the LNT

Job 15 in the LSV

Job 15 in the MAAL

Job 15 in the MBV

Job 15 in the MBV2

Job 15 in the MHNT

Job 15 in the MKNFD

Job 15 in the MNG

Job 15 in the MNT

Job 15 in the MNT2

Job 15 in the MRS1T

Job 15 in the NAA

Job 15 in the NASB

Job 15 in the NBLA

Job 15 in the NBS

Job 15 in the NBVTP

Job 15 in the NET2

Job 15 in the NIV11

Job 15 in the NNT

Job 15 in the NNT2

Job 15 in the NNT3

Job 15 in the PDDPT

Job 15 in the PFNT

Job 15 in the RMNT

Job 15 in the SBIAS

Job 15 in the SBIBS

Job 15 in the SBIBS2

Job 15 in the SBICS

Job 15 in the SBIDS

Job 15 in the SBIGS

Job 15 in the SBIHS

Job 15 in the SBIIS

Job 15 in the SBIIS2

Job 15 in the SBIIS3

Job 15 in the SBIKS

Job 15 in the SBIKS2

Job 15 in the SBIMS

Job 15 in the SBIOS

Job 15 in the SBIPS

Job 15 in the SBISS

Job 15 in the SBITS

Job 15 in the SBITS2

Job 15 in the SBITS3

Job 15 in the SBITS4

Job 15 in the SBIUS

Job 15 in the SBIVS

Job 15 in the SBT

Job 15 in the SBT1E

Job 15 in the SCHL

Job 15 in the SNT

Job 15 in the SUSU

Job 15 in the SUSU2

Job 15 in the SYNO

Job 15 in the TBIAOTANT

Job 15 in the TBT1E

Job 15 in the TBT1E2

Job 15 in the TFTIP

Job 15 in the TFTU

Job 15 in the TGNTATF3T

Job 15 in the THAI

Job 15 in the TNFD

Job 15 in the TNT

Job 15 in the TNTIK

Job 15 in the TNTIL

Job 15 in the TNTIN

Job 15 in the TNTIP

Job 15 in the TNTIZ

Job 15 in the TOMA

Job 15 in the TTENT

Job 15 in the UBG

Job 15 in the UGV

Job 15 in the UGV2

Job 15 in the UGV3

Job 15 in the VBL

Job 15 in the VDCC

Job 15 in the YALU

Job 15 in the YAPE

Job 15 in the YBVTP

Job 15 in the ZBP