Job 3 (BOGWICC)
1 Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa. 2 Ndipo Yobu anati: 3 “Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwendi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’ 4 Tsiku limenelo lisanduke mdima;Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso;kuwala kusaonekenso pa tsikulo. 5 Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli;mtambo uphimbe tsikuli;mdima wandiweyani udetse kuwala kwake. 6 Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani;usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka,kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse. 7 Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino;kusamvekenso nthungululu za chikondwerero. 8 Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo,iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani. 9 Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima;tsikulo liyembekezere kucha pachabendipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha. 10 Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi angandipo ndi limene linandionetsa zovuta. 11 “Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwandi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba? 12 Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapondi mawere woti andiyamwitsepo? 13 Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere;ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo 14 pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi,amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja, 15 pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide,amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva. 16 Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale,ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa? 17 Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto,ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo. 18 A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere;sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo. 19 Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko,ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake. 20 “Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto,ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima, 21 kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera,amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika, 22 amene amakondwa ndi kusangalalaakamalowa mʼmanda? 23 Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthuamene njira yake yabisika,amene Mulungu wamuzinga ponseponse? 24 Mʼmalo moti ndidye, ndimalira,ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza. 25 Chimene ndinkachiopa chandigwera;chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira. 26 Ndilibe mtendere kapena bata,ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.”
In Other Versions
Job 3 in the ANGEFD
Job 3 in the ANTPNG2D
Job 3 in the AS21
Job 3 in the BAGH
Job 3 in the BBPNG
Job 3 in the BBT1E
Job 3 in the BDS
Job 3 in the BEV
Job 3 in the BHAD
Job 3 in the BIB
Job 3 in the BLPT
Job 3 in the BNT
Job 3 in the BNTABOOT
Job 3 in the BNTLV
Job 3 in the BOATCB
Job 3 in the BOATCB2
Job 3 in the BOBCV
Job 3 in the BOCNT
Job 3 in the BOECS
Job 3 in the BOHCB
Job 3 in the BOHCV
Job 3 in the BOHLNT
Job 3 in the BOHNTLTAL
Job 3 in the BOICB
Job 3 in the BOILNTAP
Job 3 in the BOITCV
Job 3 in the BOKCV
Job 3 in the BOKCV2
Job 3 in the BOKHWOG
Job 3 in the BOKSSV
Job 3 in the BOLCB
Job 3 in the BOLCB2
Job 3 in the BOMCV
Job 3 in the BONAV
Job 3 in the BONCB
Job 3 in the BONLT
Job 3 in the BONUT2
Job 3 in the BOPLNT
Job 3 in the BOSCB
Job 3 in the BOSNC
Job 3 in the BOTLNT
Job 3 in the BOVCB
Job 3 in the BOYCB
Job 3 in the BPBB
Job 3 in the BPH
Job 3 in the BSB
Job 3 in the CCB
Job 3 in the CUV
Job 3 in the CUVS
Job 3 in the DBT
Job 3 in the DGDNT
Job 3 in the DHNT
Job 3 in the DNT
Job 3 in the ELBE
Job 3 in the EMTV
Job 3 in the ESV
Job 3 in the FBV
Job 3 in the FEB
Job 3 in the GGMNT
Job 3 in the GNT
Job 3 in the HARY
Job 3 in the HNT
Job 3 in the IRVA
Job 3 in the IRVB
Job 3 in the IRVG
Job 3 in the IRVH
Job 3 in the IRVK
Job 3 in the IRVM
Job 3 in the IRVM2
Job 3 in the IRVO
Job 3 in the IRVP
Job 3 in the IRVT
Job 3 in the IRVT2
Job 3 in the IRVU
Job 3 in the ISVN
Job 3 in the JSNT
Job 3 in the KAPI
Job 3 in the KBT1ETNIK
Job 3 in the KBV
Job 3 in the KJV
Job 3 in the KNFD
Job 3 in the LBA
Job 3 in the LBLA
Job 3 in the LNT
Job 3 in the LSV
Job 3 in the MAAL
Job 3 in the MBV
Job 3 in the MBV2
Job 3 in the MHNT
Job 3 in the MKNFD
Job 3 in the MNG
Job 3 in the MNT
Job 3 in the MNT2
Job 3 in the MRS1T
Job 3 in the NAA
Job 3 in the NASB
Job 3 in the NBLA
Job 3 in the NBS
Job 3 in the NBVTP
Job 3 in the NET2
Job 3 in the NIV11
Job 3 in the NNT
Job 3 in the NNT2
Job 3 in the NNT3
Job 3 in the PDDPT
Job 3 in the PFNT
Job 3 in the RMNT
Job 3 in the SBIAS
Job 3 in the SBIBS
Job 3 in the SBIBS2
Job 3 in the SBICS
Job 3 in the SBIDS
Job 3 in the SBIGS
Job 3 in the SBIHS
Job 3 in the SBIIS
Job 3 in the SBIIS2
Job 3 in the SBIIS3
Job 3 in the SBIKS
Job 3 in the SBIKS2
Job 3 in the SBIMS
Job 3 in the SBIOS
Job 3 in the SBIPS
Job 3 in the SBISS
Job 3 in the SBITS
Job 3 in the SBITS2
Job 3 in the SBITS3
Job 3 in the SBITS4
Job 3 in the SBIUS
Job 3 in the SBIVS
Job 3 in the SBT
Job 3 in the SBT1E
Job 3 in the SCHL
Job 3 in the SNT
Job 3 in the SUSU
Job 3 in the SUSU2
Job 3 in the SYNO
Job 3 in the TBIAOTANT
Job 3 in the TBT1E
Job 3 in the TBT1E2
Job 3 in the TFTIP
Job 3 in the TFTU
Job 3 in the TGNTATF3T
Job 3 in the THAI
Job 3 in the TNFD
Job 3 in the TNT
Job 3 in the TNTIK
Job 3 in the TNTIL
Job 3 in the TNTIN
Job 3 in the TNTIP
Job 3 in the TNTIZ
Job 3 in the TOMA
Job 3 in the TTENT
Job 3 in the UBG
Job 3 in the UGV
Job 3 in the UGV2
Job 3 in the UGV3
Job 3 in the VBL
Job 3 in the VDCC
Job 3 in the YALU
Job 3 in the YAPE
Job 3 in the YBVTP
Job 3 in the ZBP