Mark 12 (BOGWICC)

1 Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. 2 Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. 3 Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. 4 Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. 5 Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha. 6 “Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’ 7 “Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ 8 Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa. 9 “Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena. 10 Kodi simunawerenge lemba lakuti: “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana wakhala mwala wa pa ngodya. 11 Ambuye achita zimenezi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ” 12 Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita. 13 Pambuyo pake anatuma ena a Afarisi ndi Aherode kwa Yesu kuti adzamukole mawu ake. 14 Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?”Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” 16 Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?”Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” 17 Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”Ndipo anazizwa naye. 18 Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. 19 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 20 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. 22 Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. 23 Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?” 24 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? 25 Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 26 Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ 27 Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!” 28 Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?” 29 Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi! 30 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ 31 Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.” 32 Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. 33 Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.” 34 Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso. 35 Yesu akuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amanena kuti, ‘Khristu ndi Mwana wa Davide?’ 36 Pajatu Davide mwini wake, poyankhula mwa Mzimu Woyera, ananena kuti, “Ambuye anati kwa Ambuye anga: ‘Khalani pa dzanja langa lamanja kufikira nditayika adani anu pansi pa mapazi anu.’ 37 Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?”Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo. 38 Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika. 39 Ndipo amakhala pa mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malo aulemu pa maphwando. 40 Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.” 41 Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. 42 Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama. 43 Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. 44 Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”

In Other Versions

Mark 12 in the ANGEFD

Mark 12 in the ANTPNG2D

Mark 12 in the AS21

Mark 12 in the BAGH

Mark 12 in the BBPNG

Mark 12 in the BBT1E

Mark 12 in the BDS

Mark 12 in the BEV

Mark 12 in the BHAD

Mark 12 in the BIB

Mark 12 in the BLPT

Mark 12 in the BNT

Mark 12 in the BNTABOOT

Mark 12 in the BNTLV

Mark 12 in the BOATCB

Mark 12 in the BOATCB2

Mark 12 in the BOBCV

Mark 12 in the BOCNT

Mark 12 in the BOECS

Mark 12 in the BOHCB

Mark 12 in the BOHCV

Mark 12 in the BOHLNT

Mark 12 in the BOHNTLTAL

Mark 12 in the BOICB

Mark 12 in the BOILNTAP

Mark 12 in the BOITCV

Mark 12 in the BOKCV

Mark 12 in the BOKCV2

Mark 12 in the BOKHWOG

Mark 12 in the BOKSSV

Mark 12 in the BOLCB

Mark 12 in the BOLCB2

Mark 12 in the BOMCV

Mark 12 in the BONAV

Mark 12 in the BONCB

Mark 12 in the BONLT

Mark 12 in the BONUT2

Mark 12 in the BOPLNT

Mark 12 in the BOSCB

Mark 12 in the BOSNC

Mark 12 in the BOTLNT

Mark 12 in the BOVCB

Mark 12 in the BOYCB

Mark 12 in the BPBB

Mark 12 in the BPH

Mark 12 in the BSB

Mark 12 in the CCB

Mark 12 in the CUV

Mark 12 in the CUVS

Mark 12 in the DBT

Mark 12 in the DGDNT

Mark 12 in the DHNT

Mark 12 in the DNT

Mark 12 in the ELBE

Mark 12 in the EMTV

Mark 12 in the ESV

Mark 12 in the FBV

Mark 12 in the FEB

Mark 12 in the GGMNT

Mark 12 in the GNT

Mark 12 in the HARY

Mark 12 in the HNT

Mark 12 in the IRVA

Mark 12 in the IRVB

Mark 12 in the IRVG

Mark 12 in the IRVH

Mark 12 in the IRVK

Mark 12 in the IRVM

Mark 12 in the IRVM2

Mark 12 in the IRVO

Mark 12 in the IRVP

Mark 12 in the IRVT

Mark 12 in the IRVT2

Mark 12 in the IRVU

Mark 12 in the ISVN

Mark 12 in the JSNT

Mark 12 in the KAPI

Mark 12 in the KBT1ETNIK

Mark 12 in the KBV

Mark 12 in the KJV

Mark 12 in the KNFD

Mark 12 in the LBA

Mark 12 in the LBLA

Mark 12 in the LNT

Mark 12 in the LSV

Mark 12 in the MAAL

Mark 12 in the MBV

Mark 12 in the MBV2

Mark 12 in the MHNT

Mark 12 in the MKNFD

Mark 12 in the MNG

Mark 12 in the MNT

Mark 12 in the MNT2

Mark 12 in the MRS1T

Mark 12 in the NAA

Mark 12 in the NASB

Mark 12 in the NBLA

Mark 12 in the NBS

Mark 12 in the NBVTP

Mark 12 in the NET2

Mark 12 in the NIV11

Mark 12 in the NNT

Mark 12 in the NNT2

Mark 12 in the NNT3

Mark 12 in the PDDPT

Mark 12 in the PFNT

Mark 12 in the RMNT

Mark 12 in the SBIAS

Mark 12 in the SBIBS

Mark 12 in the SBIBS2

Mark 12 in the SBICS

Mark 12 in the SBIDS

Mark 12 in the SBIGS

Mark 12 in the SBIHS

Mark 12 in the SBIIS

Mark 12 in the SBIIS2

Mark 12 in the SBIIS3

Mark 12 in the SBIKS

Mark 12 in the SBIKS2

Mark 12 in the SBIMS

Mark 12 in the SBIOS

Mark 12 in the SBIPS

Mark 12 in the SBISS

Mark 12 in the SBITS

Mark 12 in the SBITS2

Mark 12 in the SBITS3

Mark 12 in the SBITS4

Mark 12 in the SBIUS

Mark 12 in the SBIVS

Mark 12 in the SBT

Mark 12 in the SBT1E

Mark 12 in the SCHL

Mark 12 in the SNT

Mark 12 in the SUSU

Mark 12 in the SUSU2

Mark 12 in the SYNO

Mark 12 in the TBIAOTANT

Mark 12 in the TBT1E

Mark 12 in the TBT1E2

Mark 12 in the TFTIP

Mark 12 in the TFTU

Mark 12 in the TGNTATF3T

Mark 12 in the THAI

Mark 12 in the TNFD

Mark 12 in the TNT

Mark 12 in the TNTIK

Mark 12 in the TNTIL

Mark 12 in the TNTIN

Mark 12 in the TNTIP

Mark 12 in the TNTIZ

Mark 12 in the TOMA

Mark 12 in the TTENT

Mark 12 in the UBG

Mark 12 in the UGV

Mark 12 in the UGV2

Mark 12 in the UGV3

Mark 12 in the VBL

Mark 12 in the VDCC

Mark 12 in the YALU

Mark 12 in the YAPE

Mark 12 in the YBVTP

Mark 12 in the ZBP