Nahum 3 (BOGWICC)
1 Tsoka kwa mzinda wopha anthu,mzinda wodzaza ndi mabodza,mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo,mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse! 2 Kulira kwa zikwapu,mkokomo wa mikombero,kufuwula kwa akavalondiponso phokoso la magaleta! 3 Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo,kungʼanima kwa malupangandi kunyezimira kwa mikondo!Anthu ambiri ophedwa,milumilu ya anthu akufa,mitembo yosawerengeka,anthu akupunthwa pa mitemboyo. 4 Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere,wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga,amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake,ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake. 5 Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Ine ndikutsutsana nawe.Ndidzakuvula chovala chako.Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wakondipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse. 6 Ndidzakuthira zonyansa,ndidzakuchititsa manyazindiponso kukusandutsa chinthu choseketsa. 7 Onse amene adzakuona adzakuthawa ndipo adzati,‘Ninive wasanduka bwinja,adzamulira ndani?’Kodi ndingamupeze kuti munthu woti nʼkukutonthoza?” 8 Kodi ndiwe wopambana Tebesi,mzinda wokhala mʼmbali mwa Nailo,wozunguliridwa ndi madzi?Mtsinjewo unali chitetezo chake,madziwo anali linga lake. 9 Mphamvu zake zinali Kusi ndi Igupto,Puti ndi Libiya anali ena mwa abwenzi ake. 10 Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwandipo anapita ku ukapolo.Ana ake anawaphwanyitsa pansimʼmisewu yonse ya mu mzindamo.Anachita maere ogawana anthu ake otchuka,ndipo anthu ake onse amphamvuanamangidwa ndi maunyolo. 11 Iwenso Ninive udzaledzera;udzabisalandipo udzafunafuna malo othawirako kuopa mdani. 12 Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyuyokhala ndi zipatso zoyambirira kucha;pamene agwedeza mitengoyo,nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya. 13 Tayangʼana ankhondo ako,onse ali ngati akazi!Zipata za dziko lako zatsekukira adani ako;moto wapsereza mipiringidzo yake. 14 Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu,limbitsani chitetezo chanu!Pondani dothi,ikani mʼchikombole,konzani khoma la njerwa! 15 Kumeneko moto udzakupserezani;lupanga lidzakukanthanindipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala.Chulukanani ngati ziwala,chulukanani ngati dzombe! 16 Mwachulukitsa chiwerengero cha anthu a malonda anumpaka kupambana nyenyezi za mlengalenga,koma iwo ngati dzombe akuwononga dzikondipo kenaka akuwuluka nʼkuchoka. 17 Akalonga ako ali ngati dzombe,akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombelimene lamatirira pa khoma nthawi yozizira,koma pamene dzuwa latuluka limawuluka,ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita. 18 Iwe mfumu ya ku Asiriya,abusa ako agona tulo;anthu ako olemekezeka amwalira.Anthu ako amwazikira ku mapiripopanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa. 19 Palibe chimene chingachize bala lako;chilonda chako sichingapole.Aliyense amene amamva za iweamawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako,kodi alipo amene sanazilaweponkhanza zako zosatha?
In Other Versions
Nahum 3 in the ANGEFD
Nahum 3 in the ANTPNG2D
Nahum 3 in the AS21
Nahum 3 in the BAGH
Nahum 3 in the BBPNG
Nahum 3 in the BBT1E
Nahum 3 in the BDS
Nahum 3 in the BEV
Nahum 3 in the BHAD
Nahum 3 in the BIB
Nahum 3 in the BLPT
Nahum 3 in the BNT
Nahum 3 in the BNTABOOT
Nahum 3 in the BNTLV
Nahum 3 in the BOATCB
Nahum 3 in the BOATCB2
Nahum 3 in the BOBCV
Nahum 3 in the BOCNT
Nahum 3 in the BOECS
Nahum 3 in the BOHCB
Nahum 3 in the BOHCV
Nahum 3 in the BOHLNT
Nahum 3 in the BOHNTLTAL
Nahum 3 in the BOICB
Nahum 3 in the BOILNTAP
Nahum 3 in the BOITCV
Nahum 3 in the BOKCV
Nahum 3 in the BOKCV2
Nahum 3 in the BOKHWOG
Nahum 3 in the BOKSSV
Nahum 3 in the BOLCB
Nahum 3 in the BOLCB2
Nahum 3 in the BOMCV
Nahum 3 in the BONAV
Nahum 3 in the BONCB
Nahum 3 in the BONLT
Nahum 3 in the BONUT2
Nahum 3 in the BOPLNT
Nahum 3 in the BOSCB
Nahum 3 in the BOSNC
Nahum 3 in the BOTLNT
Nahum 3 in the BOVCB
Nahum 3 in the BOYCB
Nahum 3 in the BPBB
Nahum 3 in the BPH
Nahum 3 in the BSB
Nahum 3 in the CCB
Nahum 3 in the CUV
Nahum 3 in the CUVS
Nahum 3 in the DBT
Nahum 3 in the DGDNT
Nahum 3 in the DHNT
Nahum 3 in the DNT
Nahum 3 in the ELBE
Nahum 3 in the EMTV
Nahum 3 in the ESV
Nahum 3 in the FBV
Nahum 3 in the FEB
Nahum 3 in the GGMNT
Nahum 3 in the GNT
Nahum 3 in the HARY
Nahum 3 in the HNT
Nahum 3 in the IRVA
Nahum 3 in the IRVB
Nahum 3 in the IRVG
Nahum 3 in the IRVH
Nahum 3 in the IRVK
Nahum 3 in the IRVM
Nahum 3 in the IRVM2
Nahum 3 in the IRVO
Nahum 3 in the IRVP
Nahum 3 in the IRVT
Nahum 3 in the IRVT2
Nahum 3 in the IRVU
Nahum 3 in the ISVN
Nahum 3 in the JSNT
Nahum 3 in the KAPI
Nahum 3 in the KBT1ETNIK
Nahum 3 in the KBV
Nahum 3 in the KJV
Nahum 3 in the KNFD
Nahum 3 in the LBA
Nahum 3 in the LBLA
Nahum 3 in the LNT
Nahum 3 in the LSV
Nahum 3 in the MAAL
Nahum 3 in the MBV
Nahum 3 in the MBV2
Nahum 3 in the MHNT
Nahum 3 in the MKNFD
Nahum 3 in the MNG
Nahum 3 in the MNT
Nahum 3 in the MNT2
Nahum 3 in the MRS1T
Nahum 3 in the NAA
Nahum 3 in the NASB
Nahum 3 in the NBLA
Nahum 3 in the NBS
Nahum 3 in the NBVTP
Nahum 3 in the NET2
Nahum 3 in the NIV11
Nahum 3 in the NNT
Nahum 3 in the NNT2
Nahum 3 in the NNT3
Nahum 3 in the PDDPT
Nahum 3 in the PFNT
Nahum 3 in the RMNT
Nahum 3 in the SBIAS
Nahum 3 in the SBIBS
Nahum 3 in the SBIBS2
Nahum 3 in the SBICS
Nahum 3 in the SBIDS
Nahum 3 in the SBIGS
Nahum 3 in the SBIHS
Nahum 3 in the SBIIS
Nahum 3 in the SBIIS2
Nahum 3 in the SBIIS3
Nahum 3 in the SBIKS
Nahum 3 in the SBIKS2
Nahum 3 in the SBIMS
Nahum 3 in the SBIOS
Nahum 3 in the SBIPS
Nahum 3 in the SBISS
Nahum 3 in the SBITS
Nahum 3 in the SBITS2
Nahum 3 in the SBITS3
Nahum 3 in the SBITS4
Nahum 3 in the SBIUS
Nahum 3 in the SBIVS
Nahum 3 in the SBT
Nahum 3 in the SBT1E
Nahum 3 in the SCHL
Nahum 3 in the SNT
Nahum 3 in the SUSU
Nahum 3 in the SUSU2
Nahum 3 in the SYNO
Nahum 3 in the TBIAOTANT
Nahum 3 in the TBT1E
Nahum 3 in the TBT1E2
Nahum 3 in the TFTIP
Nahum 3 in the TFTU
Nahum 3 in the TGNTATF3T
Nahum 3 in the THAI
Nahum 3 in the TNFD
Nahum 3 in the TNT
Nahum 3 in the TNTIK
Nahum 3 in the TNTIL
Nahum 3 in the TNTIN
Nahum 3 in the TNTIP
Nahum 3 in the TNTIZ
Nahum 3 in the TOMA
Nahum 3 in the TTENT
Nahum 3 in the UBG
Nahum 3 in the UGV
Nahum 3 in the UGV2
Nahum 3 in the UGV3
Nahum 3 in the VBL
Nahum 3 in the VDCC
Nahum 3 in the YALU
Nahum 3 in the YAPE
Nahum 3 in the YBVTP
Nahum 3 in the ZBP