Proverbs 14 (BOGWICC)
1 Mkazi wanzeru amamanga banja lake,koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe. 2 Amene amayenda molungama amaopa Yehova,koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova. 3 Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana,koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza. 4 Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya,koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso. 5 Mboni yokhulupirika sinama,koma mboni yonyenga imayankhula zabodza. 6 Wonyoza anzake amafunafuna nzeru koma osayipeza,koma munthu womvetsa bwino amadziwa zinthu msanga. 7 Khala kutali ndi munthu wopusachifukwa sudzapeza mawu a nzeru. 8 Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake.Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe. 9 Zitsiru zimanyoza za kulapa machimo, awo,koma kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama. 10 Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake,ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake. 11 Nyumba ya munthu woyipa idzapasuka,koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika. 12 Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu,koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa. 13 Ngakhale poseka mtima utha kumva kuwawa,ndipo mathero achimwemwe akhoza kukhala chisoni. 14 Munthu wosakhulupirika adzalandira zogwirizana ndi ntchito yake,koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito yake. 15 Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse,koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake. 16 Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa,koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala. 17 Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru,ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo. 18 Anthu opusa amalandira uchitsiru,koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu. 19 Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino,ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama. 20 Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda,koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri. 21 Wonyoza mnansi wake ndi wochimwakoma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa. 22 Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera?Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika. 23 Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu,koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi. 24 Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe,koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru. 25 Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo,koma mboni yabodza imaphetsa. 26 Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanirandipo iye adzakhala pothawira pa ana ake. 27 Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo,kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa. 28 Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu,koma popanda anthu kalonga amawonongeka. 29 Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri,koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake. 30 Mtima wodekha umapatsa thupi moyo,koma nsanje imawoletsa mafupa. 31 Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake,koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu. 32 Anthu oyipa adzakanthidwa chifukwa cha ntchito zawo zomwe,koma olungama adzatetezedwa mwa imfa yawo. 33 Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu,koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru. 34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse. 35 Mfumu imasangalatsidwa ndi wantchito wanzeru,koma imachitira ukali wantchito wochititsa manyazi.
In Other Versions
Proverbs 14 in the ANGEFD
Proverbs 14 in the ANTPNG2D
Proverbs 14 in the AS21
Proverbs 14 in the BAGH
Proverbs 14 in the BBPNG
Proverbs 14 in the BBT1E
Proverbs 14 in the BDS
Proverbs 14 in the BEV
Proverbs 14 in the BHAD
Proverbs 14 in the BIB
Proverbs 14 in the BLPT
Proverbs 14 in the BNT
Proverbs 14 in the BNTABOOT
Proverbs 14 in the BNTLV
Proverbs 14 in the BOATCB
Proverbs 14 in the BOATCB2
Proverbs 14 in the BOBCV
Proverbs 14 in the BOCNT
Proverbs 14 in the BOECS
Proverbs 14 in the BOHCB
Proverbs 14 in the BOHCV
Proverbs 14 in the BOHLNT
Proverbs 14 in the BOHNTLTAL
Proverbs 14 in the BOICB
Proverbs 14 in the BOILNTAP
Proverbs 14 in the BOITCV
Proverbs 14 in the BOKCV
Proverbs 14 in the BOKCV2
Proverbs 14 in the BOKHWOG
Proverbs 14 in the BOKSSV
Proverbs 14 in the BOLCB
Proverbs 14 in the BOLCB2
Proverbs 14 in the BOMCV
Proverbs 14 in the BONAV
Proverbs 14 in the BONCB
Proverbs 14 in the BONLT
Proverbs 14 in the BONUT2
Proverbs 14 in the BOPLNT
Proverbs 14 in the BOSCB
Proverbs 14 in the BOSNC
Proverbs 14 in the BOTLNT
Proverbs 14 in the BOVCB
Proverbs 14 in the BOYCB
Proverbs 14 in the BPBB
Proverbs 14 in the BPH
Proverbs 14 in the BSB
Proverbs 14 in the CCB
Proverbs 14 in the CUV
Proverbs 14 in the CUVS
Proverbs 14 in the DBT
Proverbs 14 in the DGDNT
Proverbs 14 in the DHNT
Proverbs 14 in the DNT
Proverbs 14 in the ELBE
Proverbs 14 in the EMTV
Proverbs 14 in the ESV
Proverbs 14 in the FBV
Proverbs 14 in the FEB
Proverbs 14 in the GGMNT
Proverbs 14 in the GNT
Proverbs 14 in the HARY
Proverbs 14 in the HNT
Proverbs 14 in the IRVA
Proverbs 14 in the IRVB
Proverbs 14 in the IRVG
Proverbs 14 in the IRVH
Proverbs 14 in the IRVK
Proverbs 14 in the IRVM
Proverbs 14 in the IRVM2
Proverbs 14 in the IRVO
Proverbs 14 in the IRVP
Proverbs 14 in the IRVT
Proverbs 14 in the IRVT2
Proverbs 14 in the IRVU
Proverbs 14 in the ISVN
Proverbs 14 in the JSNT
Proverbs 14 in the KAPI
Proverbs 14 in the KBT1ETNIK
Proverbs 14 in the KBV
Proverbs 14 in the KJV
Proverbs 14 in the KNFD
Proverbs 14 in the LBA
Proverbs 14 in the LBLA
Proverbs 14 in the LNT
Proverbs 14 in the LSV
Proverbs 14 in the MAAL
Proverbs 14 in the MBV
Proverbs 14 in the MBV2
Proverbs 14 in the MHNT
Proverbs 14 in the MKNFD
Proverbs 14 in the MNG
Proverbs 14 in the MNT
Proverbs 14 in the MNT2
Proverbs 14 in the MRS1T
Proverbs 14 in the NAA
Proverbs 14 in the NASB
Proverbs 14 in the NBLA
Proverbs 14 in the NBS
Proverbs 14 in the NBVTP
Proverbs 14 in the NET2
Proverbs 14 in the NIV11
Proverbs 14 in the NNT
Proverbs 14 in the NNT2
Proverbs 14 in the NNT3
Proverbs 14 in the PDDPT
Proverbs 14 in the PFNT
Proverbs 14 in the RMNT
Proverbs 14 in the SBIAS
Proverbs 14 in the SBIBS
Proverbs 14 in the SBIBS2
Proverbs 14 in the SBICS
Proverbs 14 in the SBIDS
Proverbs 14 in the SBIGS
Proverbs 14 in the SBIHS
Proverbs 14 in the SBIIS
Proverbs 14 in the SBIIS2
Proverbs 14 in the SBIIS3
Proverbs 14 in the SBIKS
Proverbs 14 in the SBIKS2
Proverbs 14 in the SBIMS
Proverbs 14 in the SBIOS
Proverbs 14 in the SBIPS
Proverbs 14 in the SBISS
Proverbs 14 in the SBITS
Proverbs 14 in the SBITS2
Proverbs 14 in the SBITS3
Proverbs 14 in the SBITS4
Proverbs 14 in the SBIUS
Proverbs 14 in the SBIVS
Proverbs 14 in the SBT
Proverbs 14 in the SBT1E
Proverbs 14 in the SCHL
Proverbs 14 in the SNT
Proverbs 14 in the SUSU
Proverbs 14 in the SUSU2
Proverbs 14 in the SYNO
Proverbs 14 in the TBIAOTANT
Proverbs 14 in the TBT1E
Proverbs 14 in the TBT1E2
Proverbs 14 in the TFTIP
Proverbs 14 in the TFTU
Proverbs 14 in the TGNTATF3T
Proverbs 14 in the THAI
Proverbs 14 in the TNFD
Proverbs 14 in the TNT
Proverbs 14 in the TNTIK
Proverbs 14 in the TNTIL
Proverbs 14 in the TNTIN
Proverbs 14 in the TNTIP
Proverbs 14 in the TNTIZ
Proverbs 14 in the TOMA
Proverbs 14 in the TTENT
Proverbs 14 in the UBG
Proverbs 14 in the UGV
Proverbs 14 in the UGV2
Proverbs 14 in the UGV3
Proverbs 14 in the VBL
Proverbs 14 in the VDCC
Proverbs 14 in the YALU
Proverbs 14 in the YAPE
Proverbs 14 in the YBVTP
Proverbs 14 in the ZBP