1 Peter 1 (BOGWICC)

1 Ndine Petro, mtumwi wa Yesu Khristu.Ndikulemba kalatayi kwa onse osankhidwa ndi Mulungu, alendo mʼdziko lapansi, obalalikira ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya ndi Bituniya. 2 Mulungu Atate anakusankhani, atakudziwani kuyambira pachiyambi, ndipo Mzimu Woyera wakuyeretsani kuti mumvere Yesu Khristu ndikutsukidwa ndi magazi ake.Chisomo ndi mtendere zikhale ndi inu mochuluka. 3 Alemekezedwe Mulungu, Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu. Mwachifundo chake chachikulu anatibadwitsa kwatsopano, mʼchiyembekezo chamoyo pomuukitsa Yesu Khristu kwa akufa, 4 kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba. 5 Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza. 6 Zimenezi zikukondweretseni kwambiri, ngakhale tsopano, kwa kanthawi kochepa, mukumva zowawa mʼmayesero osiyanasiyana. 7 Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. 8 Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. 9 Motero mukulandira mphotho ya chikhulupiriro chanu, ndiyo chipulumutso cha moyo wanu. 10 Kunena za chipulumutso chimenechi, aneneri amene ananeneratu za chisomo chimene chimabwera kwa inu, anafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi, 11 kufuna kudziwa nthawi ndi momwe zidzachitikire zinthu zimene Mzimu wa Khristu amene ali mwa iwo ankanenera za kuvutika kwa Khristu, ndi ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake. 12 Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi. 13 Choncho konzani mtima wanu, khalani odziretsa; khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa chisomo chimene mudzapatsidwe pamene Yesu Khristu adzaonekera. 14 Monga ana omvera, musatsatenso zilakolako zoyipa zomwe munali nazo pamene munali osadziwa. 15 Koma monga amene anakuyitanani ndi woyera, inunso khalani oyera mtima mʼmakhalidwe anu wonse. 16 Pakuti, kwalembedwa kuti, “Khalani oyera mtima, chifukwa Ine ndine Woyera.” 17 Popeza mumapemphera kwa Atate amene amaweruza munthu aliyense mopanda tsankho molingana ndi zochita zake, pa nthawi imene muli alendo pa dziko lapansi khalani moopa Mulungu. 18 Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu. 19 Koma munawomboledwa ndi magazi a mtengowapatali a Khristu, Mwana Wankhosa wopanda banga kapena chilema. 20 Iye anasankhidwa lisanalengedwe dziko lapansi, koma waonetsedwa chifukwa cha inu pa nthawi ino yotsiriza. 21 Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa namupatsa ulemerero. Nʼchifukwa chake chikhulupiriro ndi chiyembekezo chanu chili mwa Mulungu. 22 Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima. 23 Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. 24 Pakuti,“Anthu onse ali ngati udzu,ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.Udzu umafota ndipo duwa limathothoka, 25 koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.”Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.

In Other Versions

1 Peter 1 in the ANGEFD

1 Peter 1 in the ANTPNG2D

1 Peter 1 in the AS21

1 Peter 1 in the BAGH

1 Peter 1 in the BBPNG

1 Peter 1 in the BBT1E

1 Peter 1 in the BDS

1 Peter 1 in the BEV

1 Peter 1 in the BHAD

1 Peter 1 in the BIB

1 Peter 1 in the BLPT

1 Peter 1 in the BNT

1 Peter 1 in the BNTABOOT

1 Peter 1 in the BNTLV

1 Peter 1 in the BOATCB

1 Peter 1 in the BOATCB2

1 Peter 1 in the BOBCV

1 Peter 1 in the BOCNT

1 Peter 1 in the BOECS

1 Peter 1 in the BOHCB

1 Peter 1 in the BOHCV

1 Peter 1 in the BOHLNT

1 Peter 1 in the BOHNTLTAL

1 Peter 1 in the BOICB

1 Peter 1 in the BOILNTAP

1 Peter 1 in the BOITCV

1 Peter 1 in the BOKCV

1 Peter 1 in the BOKCV2

1 Peter 1 in the BOKHWOG

1 Peter 1 in the BOKSSV

1 Peter 1 in the BOLCB

1 Peter 1 in the BOLCB2

1 Peter 1 in the BOMCV

1 Peter 1 in the BONAV

1 Peter 1 in the BONCB

1 Peter 1 in the BONLT

1 Peter 1 in the BONUT2

1 Peter 1 in the BOPLNT

1 Peter 1 in the BOSCB

1 Peter 1 in the BOSNC

1 Peter 1 in the BOTLNT

1 Peter 1 in the BOVCB

1 Peter 1 in the BOYCB

1 Peter 1 in the BPBB

1 Peter 1 in the BPH

1 Peter 1 in the BSB

1 Peter 1 in the CCB

1 Peter 1 in the CUV

1 Peter 1 in the CUVS

1 Peter 1 in the DBT

1 Peter 1 in the DGDNT

1 Peter 1 in the DHNT

1 Peter 1 in the DNT

1 Peter 1 in the ELBE

1 Peter 1 in the EMTV

1 Peter 1 in the ESV

1 Peter 1 in the FBV

1 Peter 1 in the FEB

1 Peter 1 in the GGMNT

1 Peter 1 in the GNT

1 Peter 1 in the HARY

1 Peter 1 in the HNT

1 Peter 1 in the IRVA

1 Peter 1 in the IRVB

1 Peter 1 in the IRVG

1 Peter 1 in the IRVH

1 Peter 1 in the IRVK

1 Peter 1 in the IRVM

1 Peter 1 in the IRVM2

1 Peter 1 in the IRVO

1 Peter 1 in the IRVP

1 Peter 1 in the IRVT

1 Peter 1 in the IRVT2

1 Peter 1 in the IRVU

1 Peter 1 in the ISVN

1 Peter 1 in the JSNT

1 Peter 1 in the KAPI

1 Peter 1 in the KBT1ETNIK

1 Peter 1 in the KBV

1 Peter 1 in the KJV

1 Peter 1 in the KNFD

1 Peter 1 in the LBA

1 Peter 1 in the LBLA

1 Peter 1 in the LNT

1 Peter 1 in the LSV

1 Peter 1 in the MAAL

1 Peter 1 in the MBV

1 Peter 1 in the MBV2

1 Peter 1 in the MHNT

1 Peter 1 in the MKNFD

1 Peter 1 in the MNG

1 Peter 1 in the MNT

1 Peter 1 in the MNT2

1 Peter 1 in the MRS1T

1 Peter 1 in the NAA

1 Peter 1 in the NASB

1 Peter 1 in the NBLA

1 Peter 1 in the NBS

1 Peter 1 in the NBVTP

1 Peter 1 in the NET2

1 Peter 1 in the NIV11

1 Peter 1 in the NNT

1 Peter 1 in the NNT2

1 Peter 1 in the NNT3

1 Peter 1 in the PDDPT

1 Peter 1 in the PFNT

1 Peter 1 in the RMNT

1 Peter 1 in the SBIAS

1 Peter 1 in the SBIBS

1 Peter 1 in the SBIBS2

1 Peter 1 in the SBICS

1 Peter 1 in the SBIDS

1 Peter 1 in the SBIGS

1 Peter 1 in the SBIHS

1 Peter 1 in the SBIIS

1 Peter 1 in the SBIIS2

1 Peter 1 in the SBIIS3

1 Peter 1 in the SBIKS

1 Peter 1 in the SBIKS2

1 Peter 1 in the SBIMS

1 Peter 1 in the SBIOS

1 Peter 1 in the SBIPS

1 Peter 1 in the SBISS

1 Peter 1 in the SBITS

1 Peter 1 in the SBITS2

1 Peter 1 in the SBITS3

1 Peter 1 in the SBITS4

1 Peter 1 in the SBIUS

1 Peter 1 in the SBIVS

1 Peter 1 in the SBT

1 Peter 1 in the SBT1E

1 Peter 1 in the SCHL

1 Peter 1 in the SNT

1 Peter 1 in the SUSU

1 Peter 1 in the SUSU2

1 Peter 1 in the SYNO

1 Peter 1 in the TBIAOTANT

1 Peter 1 in the TBT1E

1 Peter 1 in the TBT1E2

1 Peter 1 in the TFTIP

1 Peter 1 in the TFTU

1 Peter 1 in the TGNTATF3T

1 Peter 1 in the THAI

1 Peter 1 in the TNFD

1 Peter 1 in the TNT

1 Peter 1 in the TNTIK

1 Peter 1 in the TNTIL

1 Peter 1 in the TNTIN

1 Peter 1 in the TNTIP

1 Peter 1 in the TNTIZ

1 Peter 1 in the TOMA

1 Peter 1 in the TTENT

1 Peter 1 in the UBG

1 Peter 1 in the UGV

1 Peter 1 in the UGV2

1 Peter 1 in the UGV3

1 Peter 1 in the VBL

1 Peter 1 in the VDCC

1 Peter 1 in the YALU

1 Peter 1 in the YAPE

1 Peter 1 in the YBVTP

1 Peter 1 in the ZBP