Isaiah 65 (BOGWICC)

1 “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu;ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze.Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine,ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’ 2 Tsiku lonse ndatambasulira manja angaanthu owukira aja,amene amachita zoyipa,natsatira zokhumba zawo. 3 Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsamopanda manyazi.Iwo amapereka nsembe mʼmindandi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa. 4 Amakatandala ku mandandipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika.Amadya nyama ya nkhumba,ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa. 5 Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire,chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga,ngati moto umene umayaka tsiku lonse. 6 “Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo;sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthuchifukwa cha machimo awo 7 ndi a makolo awo,”akutero Yehova.“Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapirindi kundinyoza Ine pa zitunda zawo,Ine ndidzawalanga kwathunthu potsatazimene anachita kale.” 8 Yehova akuti,“Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesandipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo,popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’Inenso chifukwa cha mtumiki wanga;sindidzawononga onse. 9 Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo,ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo.Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi,ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko. 10 Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa,ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombekwa anthu anga ondifunafuna Ine. 11 “Koma inu amene mumasiya Yehovandi kuyiwala phiri langa lopatulika,amene munamukonzera Gadi chakudyandi kuthirira Meni chakumwa, 12 ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe,ndipo nonse mudzaphedwa;chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani,ndinayankhula koma simunamvere.Munachita zoyipa pamaso pangandipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.” 13 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti,“Atumiki anga adzadya,koma inu mudzakhala ndi njala;atumiki anga adzamwa,koma inu mudzakhala ndi ludzu;atumiki anga adzakondwa,koma inu mudzakhala ndi manyazi. 14 Atumiki anga adzayimbamosangalala,koma inu mudzalira kwambirichifukwa chovutika mu mtimandipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima. 15 Anthu anga osankhidwaadzatchula dzina lanu potemberera.Ambuye Yehova adzakuphani,koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina. 16 Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomoadzachita zimenezo kwa Mulungu woona;ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomoadzalumbira mwa Mulungu woona.Pakuti mavuto akale adzayiwalikandipo adzachotsedwa pamaso panga. 17 “Taonani, ndikulengamlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.Zinthu zakale sizidzakumbukika,zidzayiwalika kotheratu. 18 Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyayachifukwa cha zimene ndikulenga,pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsandipo anthu ake adzakhala achimwemwe. 19 Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemundipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.Kumeneko sikudzamvekanso kulirandi mfuwu wodandaula. 20 “Ana sadzafa ali akhandandipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.Wamngʼono mwa iwoadzafa ali ndi zaka 100.Amene adzalephere kufika zaka 100adzatengedwa kukhalawotembereredwa. 21 Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake. 22 Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,kapena kudzala ndi ena nʼkudya.Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyowautali ngati mitengo.Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchitoya manja awo nthawi yayitali. 23 Sadzagwira ntchito pachabekapena kubereka ana kuti aone tsoka;chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe. 24 Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale. 25 Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.Pa phiri langa lopatulika sipadzakhalachinthu chopweteka kapena chowononga,”akutero Yehova.

In Other Versions

Isaiah 65 in the ANGEFD

Isaiah 65 in the ANTPNG2D

Isaiah 65 in the AS21

Isaiah 65 in the BAGH

Isaiah 65 in the BBPNG

Isaiah 65 in the BBT1E

Isaiah 65 in the BDS

Isaiah 65 in the BEV

Isaiah 65 in the BHAD

Isaiah 65 in the BIB

Isaiah 65 in the BLPT

Isaiah 65 in the BNT

Isaiah 65 in the BNTABOOT

Isaiah 65 in the BNTLV

Isaiah 65 in the BOATCB

Isaiah 65 in the BOATCB2

Isaiah 65 in the BOBCV

Isaiah 65 in the BOCNT

Isaiah 65 in the BOECS

Isaiah 65 in the BOHCB

Isaiah 65 in the BOHCV

Isaiah 65 in the BOHLNT

Isaiah 65 in the BOHNTLTAL

Isaiah 65 in the BOICB

Isaiah 65 in the BOILNTAP

Isaiah 65 in the BOITCV

Isaiah 65 in the BOKCV

Isaiah 65 in the BOKCV2

Isaiah 65 in the BOKHWOG

Isaiah 65 in the BOKSSV

Isaiah 65 in the BOLCB

Isaiah 65 in the BOLCB2

Isaiah 65 in the BOMCV

Isaiah 65 in the BONAV

Isaiah 65 in the BONCB

Isaiah 65 in the BONLT

Isaiah 65 in the BONUT2

Isaiah 65 in the BOPLNT

Isaiah 65 in the BOSCB

Isaiah 65 in the BOSNC

Isaiah 65 in the BOTLNT

Isaiah 65 in the BOVCB

Isaiah 65 in the BOYCB

Isaiah 65 in the BPBB

Isaiah 65 in the BPH

Isaiah 65 in the BSB

Isaiah 65 in the CCB

Isaiah 65 in the CUV

Isaiah 65 in the CUVS

Isaiah 65 in the DBT

Isaiah 65 in the DGDNT

Isaiah 65 in the DHNT

Isaiah 65 in the DNT

Isaiah 65 in the ELBE

Isaiah 65 in the EMTV

Isaiah 65 in the ESV

Isaiah 65 in the FBV

Isaiah 65 in the FEB

Isaiah 65 in the GGMNT

Isaiah 65 in the GNT

Isaiah 65 in the HARY

Isaiah 65 in the HNT

Isaiah 65 in the IRVA

Isaiah 65 in the IRVB

Isaiah 65 in the IRVG

Isaiah 65 in the IRVH

Isaiah 65 in the IRVK

Isaiah 65 in the IRVM

Isaiah 65 in the IRVM2

Isaiah 65 in the IRVO

Isaiah 65 in the IRVP

Isaiah 65 in the IRVT

Isaiah 65 in the IRVT2

Isaiah 65 in the IRVU

Isaiah 65 in the ISVN

Isaiah 65 in the JSNT

Isaiah 65 in the KAPI

Isaiah 65 in the KBT1ETNIK

Isaiah 65 in the KBV

Isaiah 65 in the KJV

Isaiah 65 in the KNFD

Isaiah 65 in the LBA

Isaiah 65 in the LBLA

Isaiah 65 in the LNT

Isaiah 65 in the LSV

Isaiah 65 in the MAAL

Isaiah 65 in the MBV

Isaiah 65 in the MBV2

Isaiah 65 in the MHNT

Isaiah 65 in the MKNFD

Isaiah 65 in the MNG

Isaiah 65 in the MNT

Isaiah 65 in the MNT2

Isaiah 65 in the MRS1T

Isaiah 65 in the NAA

Isaiah 65 in the NASB

Isaiah 65 in the NBLA

Isaiah 65 in the NBS

Isaiah 65 in the NBVTP

Isaiah 65 in the NET2

Isaiah 65 in the NIV11

Isaiah 65 in the NNT

Isaiah 65 in the NNT2

Isaiah 65 in the NNT3

Isaiah 65 in the PDDPT

Isaiah 65 in the PFNT

Isaiah 65 in the RMNT

Isaiah 65 in the SBIAS

Isaiah 65 in the SBIBS

Isaiah 65 in the SBIBS2

Isaiah 65 in the SBICS

Isaiah 65 in the SBIDS

Isaiah 65 in the SBIGS

Isaiah 65 in the SBIHS

Isaiah 65 in the SBIIS

Isaiah 65 in the SBIIS2

Isaiah 65 in the SBIIS3

Isaiah 65 in the SBIKS

Isaiah 65 in the SBIKS2

Isaiah 65 in the SBIMS

Isaiah 65 in the SBIOS

Isaiah 65 in the SBIPS

Isaiah 65 in the SBISS

Isaiah 65 in the SBITS

Isaiah 65 in the SBITS2

Isaiah 65 in the SBITS3

Isaiah 65 in the SBITS4

Isaiah 65 in the SBIUS

Isaiah 65 in the SBIVS

Isaiah 65 in the SBT

Isaiah 65 in the SBT1E

Isaiah 65 in the SCHL

Isaiah 65 in the SNT

Isaiah 65 in the SUSU

Isaiah 65 in the SUSU2

Isaiah 65 in the SYNO

Isaiah 65 in the TBIAOTANT

Isaiah 65 in the TBT1E

Isaiah 65 in the TBT1E2

Isaiah 65 in the TFTIP

Isaiah 65 in the TFTU

Isaiah 65 in the TGNTATF3T

Isaiah 65 in the THAI

Isaiah 65 in the TNFD

Isaiah 65 in the TNT

Isaiah 65 in the TNTIK

Isaiah 65 in the TNTIL

Isaiah 65 in the TNTIN

Isaiah 65 in the TNTIP

Isaiah 65 in the TNTIZ

Isaiah 65 in the TOMA

Isaiah 65 in the TTENT

Isaiah 65 in the UBG

Isaiah 65 in the UGV

Isaiah 65 in the UGV2

Isaiah 65 in the UGV3

Isaiah 65 in the VBL

Isaiah 65 in the VDCC

Isaiah 65 in the YALU

Isaiah 65 in the YAPE

Isaiah 65 in the YBVTP

Isaiah 65 in the ZBP