Job 6 (BOGWICC)
1 Tsono Yobu anayankha kuti, 2 “Achikhala mavuto anga anayezedwa,ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo! 3 Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja;nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula. 4 Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya,thupi langa likumva ululu wa miviyo;zoopsa za Mulungu zandizinga. 5 Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu,nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya? 6 Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere,nanga choyera cha dzira chimakoma? 7 Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe;zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi. 8 “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha,chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera, 9 achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye,kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu! 10 Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi,ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawupodziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo. 11 “Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo?Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe? 12 Kodi ine ndili ndi mphamvu?Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo? 13 Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha,nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine? 14 “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka,ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse. 15 Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga,ngati mitsinje imene imathamanga. 16 Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja,imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula, 17 koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe,ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo. 18 Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi;iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu. 19 Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi,anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo. 20 Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi;koma akafika kumeneko, amangokhumudwako. 21 Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza,mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha. 22 Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake,ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu, 23 ndilanditseni mʼdzanja la mdani,ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’ 24 “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete;ndionetseni pomwe ndalakwitsa. 25 Ndithu, mawu owona ndi opweteka!Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani? 26 Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena,ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe? 27 Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiyendi kumugulitsa bwenzi lanu. 28 “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana.Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu? 29 Fewani mtima, musachite zosalungama;ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe. 30 Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga?Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa?
In Other Versions
Job 6 in the ANGEFD
Job 6 in the ANTPNG2D
Job 6 in the AS21
Job 6 in the BAGH
Job 6 in the BBPNG
Job 6 in the BBT1E
Job 6 in the BDS
Job 6 in the BEV
Job 6 in the BHAD
Job 6 in the BIB
Job 6 in the BLPT
Job 6 in the BNT
Job 6 in the BNTABOOT
Job 6 in the BNTLV
Job 6 in the BOATCB
Job 6 in the BOATCB2
Job 6 in the BOBCV
Job 6 in the BOCNT
Job 6 in the BOECS
Job 6 in the BOHCB
Job 6 in the BOHCV
Job 6 in the BOHLNT
Job 6 in the BOHNTLTAL
Job 6 in the BOICB
Job 6 in the BOILNTAP
Job 6 in the BOITCV
Job 6 in the BOKCV
Job 6 in the BOKCV2
Job 6 in the BOKHWOG
Job 6 in the BOKSSV
Job 6 in the BOLCB
Job 6 in the BOLCB2
Job 6 in the BOMCV
Job 6 in the BONAV
Job 6 in the BONCB
Job 6 in the BONLT
Job 6 in the BONUT2
Job 6 in the BOPLNT
Job 6 in the BOSCB
Job 6 in the BOSNC
Job 6 in the BOTLNT
Job 6 in the BOVCB
Job 6 in the BOYCB
Job 6 in the BPBB
Job 6 in the BPH
Job 6 in the BSB
Job 6 in the CCB
Job 6 in the CUV
Job 6 in the CUVS
Job 6 in the DBT
Job 6 in the DGDNT
Job 6 in the DHNT
Job 6 in the DNT
Job 6 in the ELBE
Job 6 in the EMTV
Job 6 in the ESV
Job 6 in the FBV
Job 6 in the FEB
Job 6 in the GGMNT
Job 6 in the GNT
Job 6 in the HARY
Job 6 in the HNT
Job 6 in the IRVA
Job 6 in the IRVB
Job 6 in the IRVG
Job 6 in the IRVH
Job 6 in the IRVK
Job 6 in the IRVM
Job 6 in the IRVM2
Job 6 in the IRVO
Job 6 in the IRVP
Job 6 in the IRVT
Job 6 in the IRVT2
Job 6 in the IRVU
Job 6 in the ISVN
Job 6 in the JSNT
Job 6 in the KAPI
Job 6 in the KBT1ETNIK
Job 6 in the KBV
Job 6 in the KJV
Job 6 in the KNFD
Job 6 in the LBA
Job 6 in the LBLA
Job 6 in the LNT
Job 6 in the LSV
Job 6 in the MAAL
Job 6 in the MBV
Job 6 in the MBV2
Job 6 in the MHNT
Job 6 in the MKNFD
Job 6 in the MNG
Job 6 in the MNT
Job 6 in the MNT2
Job 6 in the MRS1T
Job 6 in the NAA
Job 6 in the NASB
Job 6 in the NBLA
Job 6 in the NBS
Job 6 in the NBVTP
Job 6 in the NET2
Job 6 in the NIV11
Job 6 in the NNT
Job 6 in the NNT2
Job 6 in the NNT3
Job 6 in the PDDPT
Job 6 in the PFNT
Job 6 in the RMNT
Job 6 in the SBIAS
Job 6 in the SBIBS
Job 6 in the SBIBS2
Job 6 in the SBICS
Job 6 in the SBIDS
Job 6 in the SBIGS
Job 6 in the SBIHS
Job 6 in the SBIIS
Job 6 in the SBIIS2
Job 6 in the SBIIS3
Job 6 in the SBIKS
Job 6 in the SBIKS2
Job 6 in the SBIMS
Job 6 in the SBIOS
Job 6 in the SBIPS
Job 6 in the SBISS
Job 6 in the SBITS
Job 6 in the SBITS2
Job 6 in the SBITS3
Job 6 in the SBITS4
Job 6 in the SBIUS
Job 6 in the SBIVS
Job 6 in the SBT
Job 6 in the SBT1E
Job 6 in the SCHL
Job 6 in the SNT
Job 6 in the SUSU
Job 6 in the SUSU2
Job 6 in the SYNO
Job 6 in the TBIAOTANT
Job 6 in the TBT1E
Job 6 in the TBT1E2
Job 6 in the TFTIP
Job 6 in the TFTU
Job 6 in the TGNTATF3T
Job 6 in the THAI
Job 6 in the TNFD
Job 6 in the TNT
Job 6 in the TNTIK
Job 6 in the TNTIL
Job 6 in the TNTIN
Job 6 in the TNTIP
Job 6 in the TNTIZ
Job 6 in the TOMA
Job 6 in the TTENT
Job 6 in the UBG
Job 6 in the UGV
Job 6 in the UGV2
Job 6 in the UGV3
Job 6 in the VBL
Job 6 in the VDCC
Job 6 in the YALU
Job 6 in the YAPE
Job 6 in the YBVTP
Job 6 in the ZBP